bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Acts 17
Acts 17
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 18 →
1
Pamene anapitirira pa Amfipoli, ndi Apoloniya, anafika ku Tesalonika, kumene kunali sunagoge wa Ayuda.
2
Ndipo Paulo, monga amachita, analowa kwa iwo; ndipo masabata atatu ananena ndi iwo za m'malembo, natanthauzira,
3
natsimikiza, kuti kunayenera Khristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Khristu.
4
Ndipo ena a iwo anakopedwa, nadziphatika kwa Paulo ndi Silasi; ndi Agriki akupembedza aunyinji ndithu, ndi akazi akulu osati owerengeka.
5
Koma Ayuda anadukidwa mtima, natenga anthu ena oipa achabe a pabwalo, nasonkhanitsa khamu la anthu, nachititsa phokoso m'mudzi; ndipo anagumukira kunyumba ya Yasoni, nafuna kuwatulutsira kwa anthu.
6
Pamene sanawapeza anakokera Yasoni ndi abale ena pamaso pa akulu a mudzi, nafuula kuti, Omwe aja asanduliza dziko lokhalamo anthu, afika kunonso;
7
amene Yasoni walandira; ndipo onsewo achita zokana malamulo a Kaisara; nanena kuti pali mfumu ina, Yesu.
8
Ndipo anavuta anthu, ndi akulu a mudzi, pamene anamva zimenezi.
9
Ndipo pamene analandira chikole kwa Yasoni ndi enawo, anawamasula.
10
Pomwepo abale anatumiza Paulo ndi Silasi usiku kunka ku Berea; pamene iwo anafika komweko analowa m'sunagoge wa Ayuda.
11
Amenewa anali mfulu koposa a m'Tesalonika, popeza analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m'malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.
12
Ndipo ambiri a iwo anakhulupirira; ndi akazi a Chigriki omveka, ndi amuna, osati owerengeka.
13
Koma pamene Ayuda a ku Tesalonika anazindikira kuti mau a Mulungu analalikidwa ndi Paulo ku Bereanso, anadza komwekonso, nautsa, navuta makamu.
14
Pomwepo abale anatulutsa Paulo amuke kufikira kunyanja; koma Silasi ndi Timoteo anakhalabe komweko.
15
Koma iwo amene anaperekeza Paulo anadza naye kufikira ku Atene; ndipo polandira iwo lamulo la kwa Silasi ndi Timoteo kuti afulumire kudza kwa iye ndi changu chonse, anachoka.
16
Pamene Paulo analandira iwo pa Atene, anavutidwa mtima pamene anaona mudzi wonse wadzala ndi mafano.
17
Chotero tsono anatsutsana ndi Ayuda ndi akupembedza m'sunagoge, ndi m'bwalo la malonda masiku onse ndi iwo amene anakomana nao.
18
Ndipo akukonda nzeru ena a Epikurea ndi a Stoiki anatengana naye. Ena anati, Ichi chiyani afuna kunena wobwetuka uyu? Ndipo ena, Anga wolalikira ziwanda zachilendo, chifukwa analalikira Yesu ndi kuuka kwa akufa.
19
Ndipo anamgwira, nanka naye ku Areopagi, nati, Kodi tingathe kudziwa chiphunzitso ichi chatsopano uchinena iwe?
20
Pakuti ufika nazo kumakutu athu zachilendo: tifuna tsono kudziwa, izi zitani?
21
(Koma Aatene onse ndi alendo akukhalamo anakhalitsa nthawi zao, osachita kanthu kena koma kunena kapena kumva cha tsopano.)
22
Ndipo anaimirira Paulo pakati pa Areopagi nati, Amuna inu a Atene, m'zinthu zonse ndiona kuti muli akupembedzetsa.
23
Pakuti popita, ndi kuona zinthu zimene muzipembedza, ndipezanso guwa la nsembe lolembedwa potere, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA. Chimene muchipembedza osachidziwa, chimenecho ndichilalikira kwa inu.
24
Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse zili momwemo, Iyeyo, ndiye mwini kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m'nyumba za kachisi zomangidwa ndi manja;
25
satumikiridwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu, popeza Iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse;
26
ndipo ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zao, ndi malekezero a pokhala pao;
27
kuti afunefune Mulungu, kapena akamfufuze ndi kumpeza, ngakhale sakhala patali ndi yense wa ife;
28
pakuti mwa Iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu; monga enanso a akuimba anu ati, Pakuti ifenso tili mbadwa zake.
29
Popeza tsono tili mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofanafana ndi golide, kapena siliva, kapena mwala, wolocha ndi luso ndi zolingalira za anthu.
30
Nthawi za kusadziwako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponseponse atembenuke mtima;
31
chifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m'chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse chitsimikizo, pamene anamuukitsa Iye kwa akufa.
32
Ndipo pamene anamva za kuuka kwa akufa ena anaseka pwepwete; koma ena anati, Tidzakumvanso za chimenechi.
33
Choncho Paulo anatuluka pakati pao.
34
Koma ena anadziphatika kwa iye, nakhulupirira; mwa iwonso munali Dionizio Mwareopagi, ndi mkazi dzina lake Damarisi, ndi ena pamodzi nao.
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28