bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Acts 21
Acts 21
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 22 →
1
Ndipo kunali, titalekana nao ndi kukankha ngalawa, tinadza molunjika ku Kosi, ndi m'mawa mwake ku Rode, ndipo pochokerapo ku Patara;
2
ndipo m'mene tinapeza ngalawa yakuoloka kunka ku Fenisiya, tinalowamo, ndi kupita nayo.
3
Ndipo pamene tinafika popenyana ndi Kipro, tinachisiya kulamanzere, nkupita ku Siriya; ndipo tinakocheza ku Tiro; pakuti pamenepo ngalawa inafuna kutula akatundu ake.
4
Ndipo m'mene tinapeza ophunzira, tinakhalako masiku asanu ndi awiri; ndipo iwowa ananena ndi Paulo mwa Mzimu, kuti asakwere ku Yerusalemu.
5
Ndipo kunali pamene tidatsiriza masikuwa, tidachoka ndi kunka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana, anatiperekeza kufikira kutuluka m'mudzi; ndipo pogwadira pa mchenga wa kunyanja, tinapemphera,
6
ndi kulawirana; ndipo tinalowa m'ngalawa, koma iwo anabwera kwao.
7
Ndipo ife titatsiriza ulendo wathu wochokera ku Tiro, tinafika ku Ptolemaisi; ndipo m'mene tidalonjera abale, tinakhala nao tsiku limodzi.
8
Ndipo m'mawa mwake tinachoka, ndipo tinafika ku Kesareya, ndipo m'mene tinalowa m'nyumba ya Filipo mlaliki, mmodzi wa asanu ndi awiri aja, tinakhala naye.
9
Ndipo munthuyu anali nao ana akazi anai, anamwali, amene ananenera.
10
Ndipo pokhalapo masiku ambiri, anatsika ku Yudeya mneneri, dzina lake Agabu.
11
Ndipo anadza kwa ife natenga lamba la Paulo, nadzimanga yekha manja ndi mapazi, nati, Atero Mzimu Woyera, Munthu mwini lamba ili, adzammanga kotero Ayuda a m'Yerusalemu, nadzampereka m'manja a amitundu.
12
Koma pamene tinamva izi tinamdandaulira ife ndi iwo a komweko, asakwere iye kunka ku Yerusalemu.
13
Pamenepo Paulo anayankha, Muchitanji, polira ndi kundiswera mtima? Pakuti ndakonzeka ine si kumangidwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.
14
Ndipo pokana iye kukopeka, tinaleka, ndi kuti, Kufuna kwa Ambuye kuchitidwe.
15
Ndipo atapita masiku awa tinakonza akatundu athu, ntikwera ku Yerusalemu.
16
Ndipo anamuka nafenso ena a ophunzira a ku Kesareya, natenganso wina Mnasoni wa ku Kipro, wophunzira wakale, amene adzatichereza.
17
Ndipo pofika ife ku Yerusalemu, abale anatilandira mokondwera.
18
Ndipo m'mawa mwake Paulo analowa nafe kwa Yakobo; ndi akulu onse anali pomwepo.
19
Ndipo atawalonjera iwo, anawafotokozera chimodzichimodzi zimene Mulungu anachita kwa amitundu mwa utumiki wake.
20
Ndipo pamene anazimva, analemekeza Mulungu; nati kwa iye, Uona, mbale, kuti ambirimbiri mwa Ayuda akhulupirira; ndipo ali nacho changu onsewa, cha pa chilamulo;
21
ndipo anamva za iwe, kuti uphunzitsa Ayuda onse a kwa amitundu apatukane naye Mose, ndi kuti asadule ana ao, kapena asayende monga mwa miyambo.
22
Nchiyani tsono? Adzamva ndithu kuti wafika.
23
Chifukwa chake uchite ichi tikuuza iwe; tili nao amuna anai amene anawinda;
24
amenewa uwatenge nudziyeretse nao pamodzi, nuwalipirire, kuti amete mutu; ndipo adzadziwa onse kuti zomveka za iwe nzachabe, koma kuti iwe wekhanso uyenda molunjika, nusunga chilamulo.
25
Koma kunena za amitundu adakhulupirirawo, tinalembera ndi kulamulira kuti asale zoperekedwa kwa mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama.
26
Pamenepo Paulo anatenga anthuwo, ndipo m'mawa mwake m'mene anadziyeretsa nao pamodzi, analowa m'Kachisi, nauza chimalizidwe cha masiku a kuyeretsa, kufikira adawaperekera iwo onse mtulo.
27
Ndipo pamene masiku asanu ndi awiri anati amalizidwe, Ayuda a ku Asiya pomuona iye m'Kachisi, anautsa khamu lonse la anthu, namgwira,
28
nafuula, Amuna a Israele, tithandizeni; ameneyu ndi munthu uja anaphunzitsa onse ponsepo ponenera anthu, ndi chilamulo, ndi malo ano; ndiponso anatenga Agriki nalowa nao m'Kachisi, nadetsa malo ano oyera.
29
Pakuti adaona Trofimo wa ku Efeso kale pamodzi ndi iye mumzinda; ameneyo anayesa kuti Paulo anamtenga nalowa naye ku Kachisi.
30
Ndipo mudzi wonse unasokonezeka, ndipo anthu anathamangira pamodzi; nagwira Paulo namkoka kumtulutsa m'Kachisi; ndipo pomwepo pamakomo panatsekedwa.
31
Ndipo m'mene anafuna kumupha iye, wina anamuuza kapitao wamkulu wa gululo kuti m'Yerusalemu monse muli piringupiringu.
32
Ndipo posachedwa iye anatenga asilikali ndi akenturiyo, nathamanga, nawatsikira; ndipo iwowa, pakuona kapitao wamkulu ndi asilikali, analeka kumpanda Paulo.
33
Pamenepo poyandikira kapitao wamkulu anamgwira iye, nalamulira ammange ndi maunyolo awiri; ndipo anafunsira, ndiye yani, ndipo anachita chiyani?
34
Koma wina anafuula kena, wina kena, m'khamumo; ndipo m'mene sanathe kudziwa zoona chifukwa cha phokosolo analamulira amuke naye kulinga.
35
Ndipo pamene anafika pamakwerero, kudatero kuti anamsenza asilikali chifukwa cha kulimbalimba kwa khamulo;
36
pakuti unyinji wa anthu unatsata, nufuula, Mchotse iye.
37
Ndipo poti alowe naye m'linga, Paulo ananena kwa kapitao wamkulu, Mundilole ndikuuzeni kanthu? Ndipo anati, Kodi udziwa Chigriki?
38
Si ndiwe Mwejipito uja kodi, unachita mipanduko kale lija, ndi kutsogolera ambanda aja zikwi zinai kuchipululu?
39
Koma Paulo anati, Ine ndine munthu Myuda, wa ku Tariso wa m'Silisiya, mfulu ya mudzi womveka; ndipo ndikupemphani mundilole ndilankhule ndi anthu.
40
Ndipo m'mene adamlola, Paulo anaimirira pamakwerero, natambalitsira anthu dzanja; ndipo pokhala chete onse, analankhula nao m'chinenedwe cha Chihebri, nanena:
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28