bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Acts 22
Acts 22
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 23 →
1
Amuna, abale, ndi atate, mverani chodzikanira changa tsopano, cha kwa inu.
2
Ndipo pakumva kuti analankhula nao m'chinenedwe cha Chihebri, anaposa kukhala chete; ndipo anati:
3
Ine ndine munthu Myuda, wobadwa m'Tariso wa Silisiya, koma ndaleredwa m'mzinda muno, pa mapazi a Gamaliele, wolangizidwa monga mwa chitsatidwe chenicheni cha chilamulo cha makolo athu, ndipo ndinali wachangu, cholinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero;
4
ndipo ndinalondalonda Njira iyi kufikira imfa, ndi kumanga ndi kupereka kundende amuna ndi akazi.
5
Monganso mkulu wa ansembe andichitira umboni, ndi bwalo lonse la akulu; kwa iwo amenenso ndinalandira akalata kunka nao kwa abale, ndipo ndinapita ku Damasiko, kuti ndikatenge iwonso akukhala kumeneko kudza nao omangidwa ku Yerusalemu, kuti alangidwe.
6
Ndipo kunali, pakupita ine ndi kuyandikira ku Damasiko, monga usana, mwadzidzidzi kunandiwalira pondizungulira ine kuunika kwakukulu kochokera kumwamba.
7
Ndipo ndinagwa pansitu, ndipo ndinamva mau akunena nane, Saulo, Saulo, undilondalonderanji Ine?
8
Ndipo ndinayankha, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati kwa ine, Ndine Yesu wa ku Nazarete, amene umlondalonda.
9
Ndipo iwo akukhala nane anaonadi kuunika, koma sanamva mau akulankhula nane.
10
Ndipo ndinati, Ndidzachita chiyani, Ambuye? Ndipo Ambuye anati kwa ine, Tauka, pita ku Damasiko; kumeneko adzakufotokozera zonse zoikika kwa iwe uzichite.
11
Ndipo popeza sindinapenya, chifukwa cha ulemerero wa kuunikako, anandigwira dzanja iwo amene anali ndi ine, ndipo ndinafika ku Damasiko.
12
Ndipo munthu dzina lake Ananiya, ndiye munthu wopembedza monga mwa chilamulo, amene amchitira umboni wabwino Ayuda onse akukhalako,
13
anadza kwa ine, ndipo poimirirapo anati kwa ine, Saulo, mbale, penyanso. Ndipo ine, ora lomweli ndinampenya.
14
Ndipo anati, Mulungu wa makolo athu anakusankhiratu udziwe chifuniro chake, nuone Wolungamayo, numve mau otuluka m'kamwa mwake.
15
Ndipo udzamkhalira Iye mboni kwa anthu onse, za izo udaziona ndi kuzimva.
16
Ndipo tsopano uchedweranji? Tauka, nubatizidwe ndi kusamba kuchotsa machimo ako, nuitane pa dzina lake.
17
Ndipo kunali, nditabwera ku Yerusalemu ndinalikupemphera m'Kachisi, ndinachita ngati kukomoka,
18
ndipo ndinamuona Iye, nanena nane, Fulumira, tuluka msanga m'Yerusalemu; popeza sadzalandira umboni wako wakunena za Ine.
19
Ndipo ndinati ine, Ambuye, adziwa iwo okha kuti ndinali kuika m'ndende ndi kuwapanda m'masunagoge onse iwo akukhulupirira Inu;
20
ndipo pamene anakhetsa mwazi wa Stefano mboni yanu, ine ndemwe ndinalikuimirirako, ndi kuvomerezana nao, ndi kusunga zovala za iwo amene anamupha iye.
21
Ndipo anati kwa ine, Pita; chifukwa Ine ndidzakutuma iwe kunka kutali kwa amitundu.
22
Ndipo adamumva kufikira mau awa; ndipo anakweza mau ao nanena, Achoke pa dziko lapansi munthu wotere; pakuti sayenera iye kukhala ndi moyo.
23
Ndipo pakufuula iwo, ndi kutaya zovala zao, ndi kuwaza fumbi mumlengalenga,
24
kapitao wamkulu analamulira kuti amtenge iye kulowa naye kulinga, nati amfunsefunse ndi kumkwapula, kuti adziwe chifukwa chake nchiyani kuti amfuulira chomwecho.
25
Ndipo m'mene anammanga iye ndi nsingazo, Paulo anati kwa kenturiyo wakuimirirako, Kodi nkuloleka kwa inu kukwapula munthu Mroma, mlandu wake wosamveka?
26
Ndipo pakumva ichi kenturiyoyo, ananka kwa kapitao wamkulu, namuuza, nanena, Nchiyani ichi uti uchite? Pakuti munthuyo ndiye Mroma.
27
Ndipo kapitao wamkuluyo anadza, nati kwa iye, Ndiuze, iwe ndiwe Mroma kodi? Ndipo anati, Inde.
28
Ndipo kapitao wamkulu anayankha, Ine ndalandira ufulu umene ndi kuperekapo mtengo wake waukulu. Ndipo Paulo anati, Koma ine ndabadwa Mroma.
29
Pamenepo ndipo iwo amene anati amfunsefunse, anamsiya; ndipo kapitao wamkulunso anaopa, pozindikira kuti ndiye Mroma, ndiponso popeza adammanga iye.
30
Koma m'mawa mwake pofuna kuzindikira chifukwa chake chenicheni chakuti anamnenera Ayuda, anammasula iye, nalamulira asonkhane ansembe aakulu, ndi bwalo lonse la akulu, ndipo anatsika naye Paulo, namuika pamaso pao.
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28