bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Acts 9
Acts 9
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 10 →
1
Koma Saulo, wosaleka kupumira pa ophunzira a Ambuye kuopsa ndi kupha, ananka kwa mkulu wa ansembe,
2
napempha kwa iye akalata akunka nao ku Damasiko ku masunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nao omangidwa ku Yerusalemu.
3
Ndipo poyenda ulendo wake, kunali kuti iye anayandikira Damasiko: ndipo mwadzidzidzi kudawala momzingira kuunika kochokera kumwamba;
4
ndipo anagwa pansi, namva mau akunena naye, Saulo, Saulo, Undilondalonderanji?
5
Koma anati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda;
6
komatu, uka, nulowe m'mudzi, ndipo kudzanenedwa kwa iwe chimene uyenera kuchita.
7
Ndipo amunawo akumperekeza iye anaima duu, atamvadi mau, koma osaona munthu.
8
Ndipo Saulo anauka; koma potseguka maso ake, sanapenya kanthu; ndipo anamgwira dzanja, namtenga nalowa naye m'Damasiko.
9
Ndipo anakhala masiku atatu wosaona, ndipo sanadya kapena kumwa.
10
Koma ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lake Ananiya; ndipo Ambuye anati kwa iye m'masomphenya, Ananiya. Ndipo anati, Ndili pano, Ambuye,
11
Ndipo Ambuye anati kwa iye, Tauka, pita ku khwalala lotchedwa Lolunjika, ndipo m'nyumba ya Yudasi ufunse za munthu dzina lake Saulo, wa ku Tariso: pakuti taona, alikupemphera
12
ndipo anaona mwamuna dzina lake Ananiya, alikulowa, namuika manja, kuti apenyenso.
13
Ndipo Ananiya anayankha nati, Ambuye, ndamva ndi ambiri za munthu uyu, kuti anachitiradi choipa oyera mtima anu m'Yerusalemu;
14
ndi kuti pano ali nao ulamuliro wa kwa ansembe aakulu wakumanga onse akuitana pa dzina lanu.
15
Koma Ambuye anati kwa iye, Pita; pakuti iye ndiye chotengera changa chosankhika, chakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israele;
16
pakuti Ine ndidzamuonetsa iye zinthu zambiri ayenera iye kuzimva kuwawa chifukwa cha dzina langa.
17
Ndipo anachoka Ananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ake pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani pa njira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.
18
Ndipo pomwepo padagwa kuchoka m'maso mwake ngati mamba, ndipo anapenyanso; ndipo ananyamuka nabatizidwa;
19
ndipo analandira chakudya, naona nacho mphamvu. Ndipo anakhala pamodzi ndi ophunzira a ku Damasiko masiku ena.
20
Ndipo pomwepo m'masunagoge analalikira Yesu, kuti Iye ndiye Mwana wa Mulungu.
21
Ndipo onse amene anamva anadabwa, nanena, Suyu iye amene anaononga m'Yerusalemu onse akuitana pa dzina ili? Ndipo wadza kuno kudzatero, kuti amuke nao omangidwa kwa ansembe aakulu.
22
Koma Saulo anakula makamaka mumphamvu, nadodometsa Ayuda akukhala m'Damasiko, nawatsimikizira kuti ameneyo ndi Khristu.
23
Ndipo atapita masiku ambiri, Ayuda anapangana kuti amuphe iye;
24
koma chiwembu chao chinadziwika ndi Saulo. Ndipo anadikiranso pazipata usana ndi usiku kuti amuphe;
25
koma ophunzira ake anamtenga usiku, nampyoletsa palinga, namtsitsa mu dengu.
26
Koma m'mene anafika ku Yerusalemu, anayesa kudziphatika kwa ophunzira; ndipo anamuopa iye onse, osakhulupirira kuti ali wophunzira.
27
Koma Barnabasi anamtenga, napita naye kwa atumwi, nawafotokozera umo adaonera Ambuye m'njira, ndi kuti analankhula naye, ndi kuti m'Damasiko adanena molimbika mtima m'dzina la Yesu.
28
Ndipo anali pamodzi nao, nalowa natuluka ku Yerusalemu,
29
nanena molimbika mtima m'dzina la Ambuye; ndipotu analankhula natsutsana ndi Agriki; koma anayesayesa kumupha iye.
30
Koma m'mene abale anachidziwa, anapita naye ku Kesareya, namtumiza achokeko kunka ku Tariso.
31
Pamenepo ndipo Mpingo wa m'Yudeya lonse ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'chitonthozo cha Mzimu Woyera, nuchuluka.
32
Koma kunali, pakupita Petro ponseponse, anatsikiranso kwa oyera mtima akukhala ku Lida.
33
Ndipo anapeza kumeneko munthu dzina lake Eneya, amene anagonera pamphasa zaka zisanu ndi zitatu; amene anagwidwa manjenje.
34
Ndipo Petro anati kwa iye, Eneya, Yesu Khristu akuchiritsa iwe; uka, yalula mphasa yako. Ndipo anauka pomwepo.
35
Ndipo anamuona iye onse akukhala ku Lida ndi ku Saroni, natembenukira kwa Ambuye amenewa.
36
Koma m'Yopa munali wophunzira dzina lake Tabita, ndilo kunena Dorika; mkazi ameneyo anadzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo zimene anazichita.
37
Ndipo kunali m'masiku awa, kuti anadwala iye, namwalira; ndipo atamsambitsa iye anamgoneka m'chipinda chapamwamba.
38
Ndipo popeza Lida ndi pafupi pa Yopa, m'mene anamva ophunzirawo kuti Petro anali pomwepo, anamtumizira anthu awiri, namdandaulira, Musachedwa mudze kwa ife.
39
Ndipo Petro ananyamuka, napita nao. M'mene anafikako, anapita naye kuchipinda chapamwamba; ndipo amasiye onse anaimirirapo pali iye, nalira, namuonetsa malaya ndi zovala zimene Dorika adasoka, pamene anali nao pamodzi.
40
Koma Petro anawatulutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ake; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.
41
Ndipo Petro anamgwira dzanja, namnyamutsa; ndipo m'mene adaitana oyera mtima ndi amasiye, anampereka iye wamoyo.
42
Ndipo kudadziwika ku Yopa konse: ndipo ambiri anakhulupirira Ambuye.
43
Ndipo kunali, kuti anakhala iye m'Yopa masiku ambiri ndi munthu Simoni wofufuta zikopa.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28