bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Acts 14
Acts 14
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 15 →
1
Ndipo kunali pa Ikonio kuti analowa pamodzi m'sunagoge wa Ayuda, nalankhula kotero, kuti khamu lalikulu la Ayuda ndi Agriki anakhulupirira.
2
Koma Ayuda osamvera anautsa mitima ya Agriki kuti aipse abale athu.
3
Chifukwa chake anakhala nthawi yaikulu nanenetsa zolimba mtima mwa Ambuye, amene anachitira umboni mau a chisomo chake, napatsa zizindikiro ndi zozizwa kuti zichitidwe ndi manja ao.
4
Ndipo khamu la mudziwo linagawikana; ena anali ndi Ayuda, koma ena anali ndi atumwi.
5
Ndipo pamene panakhala chigumukiro cha Agriki ndi cha Ayuda ndi akulu ao, cha kuwachitira chipongwe ndi kuwaponya miyala,
6
iwo anamva, nathawira kumidzi ya Likaoniya, Listara ndi Deribe, ndi dziko lozungulirapo:
7
kumeneko ndiko Uthenga Wabwino.
8
Ndipo pa Listara panakhala munthu wina wopanda mphamvu ya m'mapazi mwake, wopunduka chibadwire, amene sanayenda nthawi zonse.
9
Ameneyo anamva Paulo alinkulankhula; ndipo Paulo pomyang'anitsa, ndi kuona kuti anali ndi chikhulupiriro cholandira nacho moyo,
10
anati ndi mau akulu, Taimirira. Ndipo iyeyu anazunzuka, nayenda.
11
Pamene makamu anaona chimene anachita Paulo, anakweza mau ao, nati m'chinenero cha Likaoniya, Milungu yatsikira kwa ife monga anthu.
12
Ndipo anamutcha Barnabasi, Zeusi; ndi Paulo, Heremesi, chifukwa anali wotsogola kunena.
13
Koma wansembe wa Zeusi wa kumaso kwa mudzi, anadza nazo ng'ombe ndi maluwa kuzipata, nafuna kupereka nsembe pamodzi ndi makamu.
14
Pamene anamva atumwi Paulo ndi Barnabasi, anang'amba zofunda zao, natumphira m'khamu,
15
nafuula nati, Anthuni, bwanji muchita zimenezi? Ifenso tili anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zachabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse zili momwemo:
16
m'mibadwo yakale Iye adaleka mitundu yonse iyende m'njira mwao.
17
Koma sanadzisiyira Iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.
18
Pakunena izo, anavutika pakuletsa makamu kuti asapereke nsembe kwa iwo.
19
Ndipo anafika kumeneko Ayuda kuchokera ku Antiokeya ndi Ikonio; nakopa makamu, ndipo anamponya Paulo miyala, namguzira kunja kwa mudzi; namuyesa kuti wafa.
20
Koma pamene anamzinga ophunzirawo, anauka iye, nalowa m'mudzi; m'mawa mwake anatuluka ndi Barnabasi kunka ku Deribe.
21
Pamene analalikira Uthenga Wabwino pamudzipo, nayesa ambiri ophunzira, anabwera ku Listara ndi Ikonio ndi Antiokeya,
22
nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m'chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa m'ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.
23
Ndipo pamene anawaikira akulu mosankha mu Mpingo uliwonse, ndi kupemphera pamodzi ndi kusala kudya, naikiza iwo kwa Ambuye amene anamkhulupirirayo.
24
Ndipo anapitirira pa Pisidiya, nafika ku Pamfiliya.
25
Ndipo atalankhula mau m'Perga, anatsikira ku Ataliya;
26
komweko anachoka m'ngalawa kunka ku Antiokeya, kumene anaikizidwa ku chisomo cha Mulungu ku ntchito imene adaimalizayo.
27
Pamene anafika nasonkhanitsa Mpingo anabwerezanso zomwe Mulungu anachita nao, kuti anatsegulira amitundu pa khomo la chikhulupiriro.
28
Ndipo anakhala pamenepo ndi ophunzira nthawi yaikulu.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28