bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Acts 15
Acts 15
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 16 →
1
Ndipo anadza ena akutsika ku Yudeya, nawaphunzitsa abale, nati, Mukapanda kudulidwa monga mwambo wa Mose, simungathe kupulumuka.
2
Ndipo pamene Paulo ndi Barnabasi anachitana nao makani ndi mafunsano, abale anapatula Paulo ndi Barnabasi, ndi ena a iwo, kuti akwere kunka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akulu kukanena za funsolo.
3
Ndipo iwo anaperekezedwa ndi Mpingo, napita pa Fenisiya ndi Samariya, nafotokozera chisanduliko cha amitundu; nakondweretsa kwambiri abale onse.
4
Pamene anafika ku Yerusalemu, analandiridwa ndi Mpingo, ndi atumwi ndi akulu, ndipo anabwerezanso zonse zimene Mulungu anachita nao.
5
Koma anauka ena a mpatuko wa Afarisi okhulupirira, nati, Kuyenera kuwadula iwo, ndi kuwauza kuti asunge chilamulo cha Mose.
6
Ndipo anasonkhana atumwi ndi akulu kuti anene za mlanduwo.
7
Ndipo pamene panali mafunsano ambiri, Petro anaimirira, nati kwa iwo, Abale, mudziwa kuti poyamba Mulungu anasankha mwa inu, kuti m'kamwa mwanga amitundu amve mau a Uthenga Wabwino, nakhulupirire.
8
Ndipo Mulungu, amene adziwa mtima, anawachitira umboni; nawapatsa Mzimu Woyera, monga anatipatsa ife;
9
ndipo sanalekanitsa ife ndi iwo, nayeretsa mitima yao m'chikhulupiriro.
10
Nanga bwanji tsopano mulikumuyesa Mulungu, kuti muike pa khosi la ophunzira goli, limene sanatha kunyamula kapena makolo athu kapena ife?
11
Koma tikhulupirira tidzapulumuka mwa chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, monga iwo omwe.
12
Ndipo khamu lonse linatonthola; ndipo anamvera Barnabasi ndi Paulo alikubwerezanso zizindikiro ndi zozizwitsa zimene Mulungu anachita nao pa amitundu.
13
Pamene iwo anatonthola Yakobo anayankha, nati, Abale, mverani ine:
14
Simoni wabwereza kuti poyamba Mulungu anayang'anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake.
15
Ndipo mau a aneneri avomereza pamenepo; monga kunalembedwa,
16
Zikatha izo ndidzabwera, ndidzamanganso chihema cha Davide, chimene chinagwa; ndidzamanganso zopasuka zake, ndipo ndidzachiimikanso:
17
Kuti anthu otsalira afunefune Ambuye, ndi amitundu onse amene dzina langa linatchulidwa pa iwo,
18
ati Ambuye, amene azidziwitsa zinthu zonsezo chiyambire dziko lapansi.
19
Chifukwa chake ine ndiweruza, kuti tisavute a mwa amitundu amene anatembenukira kwa Mulungu,
20
koma kuti tilembere kwa iwo, kuti asale zonyansa za mafano, ndi dama, ndi zopotola, ndi mwazi.
21
Pakuti Mose, kuyambira pa mibadwo yakale ali nao m'midzi yonse amene amlalikira, akuwerenga mau ake m'masunagoge masabata onse.
22
Pamenepo chinakomera atumwi ndi akulu ndi Mpingo wonse kusankha anthu a m'gulu lao, ndi kuwatumiza ku Antiokeya ndi Paulo ndi Barnabasi; ndiwo Yudasi wotchedwa Barsabasi, ndi Silasi, akulu a mwa abale; ndipo analembera mau natumiza ndi iwo:
23
Atumwi ndi abale akulu kwa abale a mwa amitundu a m'Antiokeya, ndi Siriya, ndi Silisiya, tikulankhulani:
24
Popeza tamva kuti ena amene anatuluka mwa ife anakuvutani ndi mau, nasocheretsa mitima yanu; amenewo sitinawalamulira;
25
chinatikomera ndi mtima umodzi, tisankhe anthu, ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi okondedwa anthu Barnabasi ndi Paulo,
26
anthu amene anapereka moyo wao chifukwa cha dzina la Yesu Khristu Ambuye wathu.
27
Tatumiza tsono Yudasi ndi Silasi, omwenso adzakuuzani ndi mau zinthu zomwezo.
28
Pakuti chinakomera Mzimu Woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa chachikulu china choposa izi zoyenerazi;
29
kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama; ngati mudzisungitsa pa zimenezi, kudzakhala bwino kwa inu. Tsalani bwino.
30
Tsono pamene iwo anamuka anatsikira ku Antiokeya; ndipo anasonkhanitsa khamu, napereka kalatayo.
31
Pamene anawerenga, anakondwera chifukwa cha chisangalatso chake.
32
Ndipo Yudasi ndi Silasi, okhala eni okha aneneri, anasangalatsa abale ndi mau ambiri, nawalimbikitsa.
33
Pamene anakhala nthawi, abale analawirana nao ndi mtendere amuke kwa iwo amene anawatumiza.
35
Koma Paulo ndi Barnabasi anakhalabe m'Antiokeya, nalinkuphunzitsa, ndi kulalikira mau a Ambuye pamodzi ndi ena ambiri.
36
Patapita masiku, Paulo anati kwa Barnabasi, Tibwerenso, tizonde abale m'midzi yonse m'mene tinalalikiramo mau a Ambuye, tione mkhalidwe wao.
37
Ndipo Barnabasi anafuna kumtenga Yohane uja, wotchedwa Marko
38
Koma sikunamkomera Paulo kumtenga iye amene anawasiya nabwerera pa Pamfiliya paja osamuka nao kuntchito.
39
Ndipo panali kupsetsana mtima, kotero kuti analekana wina ndi mnzake; ndipo Barnabasi anatenga Marko, nalowa m'ngalawa, nanka ku Kipro.
40
Koma Paulo anasankha Silasi, namuka, woikizidwa ndi abale ku chisomo cha Ambuye.
41
Ndipo iye anapita kupyola pa Siriya ndi Silisiya, nakhazikitsa Mipingo.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28