bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Acts 24
Acts 24
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 25 →
1
Ndipo atapita masiku asanu anatsika mkulu wa ansembe Ananiya pamodzi ndi akulu ena, ndi wogwira moyo dzina lake Tertulo; ndipo anafotokozera kazembeyo za kunenera Paulo.
2
Ndipo pamene adamuitana, Tertulo anayamba kumnenera ndi kunena, Popeza tili nao mtendere wambiri mwa inu, ndipo mwa kuganiziratu kwanu muukonzera mtundu wathu zotiipsa,
3
tizilandira ndi chiyamiko chonse, monsemo ndi ponsepo, Felikisi womveka inu.
4
Koma kuti ndingaonjeze kukulemetsani ndikupemphani mutimvere mwachidule ndi chifatso chanu.
5
Pakuti tapeza munthuyu ali ngati mliri, ndi woutsa mapanduko kwa Ayuda onse m'dziko lonse lokhalamo anthu, ndi mtsogoleri wa mpanduko wa Anazarene;
6
amenenso anayesa kuipsa Kachisi; amene tamgwira.
8
Ndipo kwa iye mudzakhoza kuzindikira pomfunsa nokha, za izi zonse timnenerazi.
9
Ndipo Ayudanso anavomerezana naye, natsimikiza kuti izi zitero.
10
Ndipo pamene kazembe anamkodola kuti anene, Paulo anayankha, Podziwa ine kuti mwakhala woweruza wa mtundu uwu zaka zambiri, ndidzikanira mokondwera;
11
popeza mukhoza kuzindikira kuti apita masiku khumi ndi awiri okha chikwerere ine ku Yerusalemu kukalambira;
12
ndipo sanandipeza m'Kachisi wotsutsana ndi munthu, kapena kuutsa khamu la anthu, kapena m'sunagoge kapena m'mzinda.
13
Ndipo sangathe kukutsimikizirani zimene andinenera ine tsopano.
14
Koma ichi ndivomera kwa inu, kuti monga mwa Njira yonenedwa mpatuko, momwemo nditumikira Mulungu wa makolo athu, ndi kukhulupirira zonse zili monga mwa chilamulo, ndi zolembedwa mwa aneneri;
15
ndi kukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu chimene iwo okhanso achilandira, kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.
16
M'menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbu mtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.
17
Ndipo zitapita zaka zambiri ndinadza kutengera mtundu wanga zachifundo, ndi zopereka;
18
popereka izi anandipeza woyeretsedwa m'Kachisi, wopanda khamu la anthu, kapena phokoso;
19
koma panali Ayuda ena a ku Asiya, ndiwo mwenzi atakhala pano pamaso panu ndi kundinenera, ngati ali nako kanthu kotsutsa ine.
20
Kapena iwo amene ali kunowa anene anapeza chosalungama chotani, poimirira ine pamaso pa bwalo la akulu,
21
koma mau awa amodzi okha, amene ndinafuula poimirira pakati pao, Kunena za kuuka kwa akufa ndiweruzidwa ndi inu lero lino.
22
Koma Felikisi anawalinditsa, popeza anadziwitsadi Njirayo, nati, Pamene Lisiasi kapitao wamkulu akatsika ndidzazindikiritsa konse za kwa inu.
23
Ndipo analamulira kenturiyo amsunge iye, koma akhale nao ufulu, ndipo asaletse anthu ake kumtumikira.
24
Koma atapita masiku ena, anadza Felikisi ndi Durusila mkazi wake, ndiye Myuda, naitana Paulo, ndipo anamva iye za chikhulupiriro cha Khristu Yesu.
25
Ndipo m'mene anamfotokozera za chilungamo, ndi chidziletso, ndi chiweruziro chilinkudza, Felikisi anagwidwa ndi mantha, nayankha, Pita tsopano; ndipo ndikaona nthawi, ndidzakuitana iwe.
26
Anayembekezanso kuti Paulo adzampatsa ndalama; chifukwa chakenso anamuitana iye kawirikawiri, nakamba naye.
27
Koma zitapita zaka ziwiri Porkio Fesito analowa m'malo a Felikisi; ndipo Felikisi pofuna kukonda Ayuda anamsiya Paulo m'nsinga.
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28