bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Acts 25
Acts 25
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 26 →
1
Pamenepo Fesito m'mene analowa dziko lake, ndipo atapita masiku atatu, anakwera kunka ku Yerusalemu kuchokera ku Kesareya.
2
Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a Ayuda ananenera Paulo kwa iye; ndipo iwo anamdandaulira,
3
nampempha kuti mlandu wake wa Paulo uipe, kuti amuitane iye adze ku Yerusalemu; iwo amchitira chifwamba kuti amuphe panjira.
4
Pamenepo Fesito anayankha, kuti Paulo asungike ku Kesareya, ndi kuti iye mwini adzapitako posachedwa.
5
Chifukwa chake, ati, iwo amene akhoza mwa inu amuke nane potsikirako, ndipo ngati kuli kanthu kosayenera mwa munthuyo amnenere iye.
6
Ndipo m'mene adatsotsa mwa iwo masiku asanu ndi atatu kapena khumi okha anatsikira ku Kesareya; ndipo m'mawa mwake anakhala pa mpando wachiweruziro, nalamulira kuti atenge Paulo.
7
Ndipo m'mene anafika iye, Ayuda adatsikawo ku Yerusalemu anaimirira pomzinga iye, namnenera zifukwa zambiri ndi zazikulu, zimene sanakhoza kuzitsimikiza;
8
koma Paulo podzikanira ananena, Sindinachimwa kanthu kapena pachilamulo cha Chiyuda, kapena pa Kachisi, kapena pa Kaisara.
9
Koma Fesito pofuna kuyesedwa wachisomo ndi Ayuda, anayankha kwa Paulo, nati, Kodi ufuna kukwera kunka ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa ndi ine pomwepo kunena za zinthu izi?
10
Koma Paulo anati, Ndilikuimirira pa mpando wachiweruziro wa Kaisara, pompano ndiyenera kuweruzidwa ine; Ayuda sindinawachitira kanthu koipa, monga mudziwanso nokha bwino.
11
Pamenepo ngati ndili wochita zoipa, ngati ndachita kanthu kakuyenera imfa, sindikana kufa; koma ngati zinthuzi awa andinenera nazo zili zachabe, palibe mmodzi akhoza kundipereka kwa iwo. Nditulukira kwa Kaisara.
12
Pamenepo Fesito, atakamba ndi aphungu ake, anayankha, Wanena, Nditulukira kwa Kaisara; kwa Kaisara udzapita.
13
Ndipo atapita masiku ena, Agripa mfumuyo, ndi Berenise anafika ku Kesareya, nalankhula Fesito.
14
Ndipo atatsotsako masiku ambiri, Fesito anafotokozera mfumuyo mlandu wake wa Paulo, nanena, Pali munthu adamsiya m'ndende Felikisi,
15
amene ansembe aakulu ndi akulu a Ayuda anamnenera kwa ine, ndili ku Yerusalemu, nandipempha ndiipitse mlandu wake.
16
Koma ndinawayankha, kuti machitidwe a Aroma satero, kupereka munthu asanayambe woneneredwayo kupenyana nao omnenera ndi kukhala napo podzikanira pa chomneneracho.
17
Potero, pamene adasonkhana pano, sindinachedwa, koma m'mawa mwake ndinakhala pa mpando wachiweruziro, ndipo ndinalamulira adze naye munthuyo.
18
Ndipo pamene anaimirira omneneza, sanamtchulira konse chifukwa cha zoipa zonga ndinazilingirira ine;
19
koma anali nao mafunso ena otsutsana naye a chipembedzero cha iwo okha, ndi mafunso a wina Yesu, amene adafa, amene Paulo anati kuti ali ndi moyo.
20
Ndipo ine posinkhasinkha za mafunso awa ndinamfunsa ngati afuna kupita ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa komweko za izi.
21
Koma pakunena Paulo ndi kuti, asungidwe, akatulukire kwa Augusto, ndinaweruza asungidwe iye kufikira ndikamtumiza kwa Kaisara.
22
Ndipo Agripa anati kwa Fesito, Ndifuna nanenso ndimve munthuyo. Anati, Mawa mudzamva iye.
23
M'mawa mwake tsono, atafika Agripa ndi Berenise ndi chifumu chachikulu, ndipo atalowa momvera milandu, pamodzi ndi akapitao akulu, ndi amuna omveka a mudziwo, ndipo pakulamulira Fesito, anadza naye Paulo.
24
Ndipo Fesito anati, Mfumu Agripa, ndi amuna inu nonse muli nafe pano pamodzi, muona uyu, amene unyinji wonse wa Ayuda anandiuza za iye, ku Yerusalemu ndi kunonso, ndi kufuula kuti sayeneranso kukhala ndi moyo.
25
Koma ndinapeza ine kuti sanachita kanthu koyenera imfa iye; ndipo popeza iye yekha anati akatulukire kwa Augusto, ndatsimikiza mtima kumtumizako.
26
Koma ndilibe ine kanthu koti ndinenetse za iye kakulembera kwa mbuye wanga. Chifukwa chake ndamtulutsira kwa inu, ndipo makamaka kwa inu, Mfumu Agripa, kuti, ndikatha kumfunsafunsa, ndikhale nako kanthu kakulembera.
27
Pakuti chindionekera chopanda nzeru, potumiza wam'nsinga, wosatchulanso zifukwa zoti amneneze.
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 26 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28