bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Acts 20
Acts 20
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 21 →
1
Ndipo litaleka phokoso, Paulo anaitana ophunzirawo, ndipo m'mene anawachenjeza, analawirana nao, natuluka kunka ku Masedoniya.
2
Ndipo m'mene atapitapita m'mbali zijazo, nawachenjeza, anadza ku Grisi.
3
Ndipo m'mene adakhalako miyezi itatu, ndipo atampangira chiwembu Ayuda, poti iye apite ndi ngalawa ku Siriya, anatsimikiza mtima abwerere popyola Masedoniya.
4
Ndipo anamperekeza kufikira ku Asiya Sopatere mwana wa Piro, wa ku Berea; ndipo a Atesalonika, Aristariko ndi Sekundo; ndi Gayo wa ku Deribe, ndi Timoteo; ndi a ku Asiya, Tikiko ndi Trofimo.
5
Koma iwowa adatitsogolera, natilinda ku Troasi.
6
Ndipo tinapita m'ngalawa kuchokera ku Filipi, atapita masiku a mkate wopanda chotupitsa, ndipo popita masiku asanu tinawapeza ku Troasi; pamenepo tinatsotsa masiku asanu ndi awiri.
7
Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo anawafotokozera mau, popeza anati achoke m'mawa mwake; ndipo ananena chinenere kufikira pakati pa usiku.
8
Ndipo munali nyali zambiri m'chipinda chapamwamba m'mene tinasonkhanamo.
9
Ndipo mnyamata dzina lake Yutiko anakhala pazenera, wogwidwa nato tulo tatikulu; ndipo pakukhala chifotokozere Paulo, ndipo pogwidwa nato tulo, anagwa posanja pachiwiri, ndipo anamtola wakufa.
10
Ndipo potsikirako Paulo, anamgwera namfungatira, nati, Musachite phokoso, pakuti moyo wake ulipo.
11
Ndipo m'mene adakwera, nanyema mkate, nadya, nakamba nao nthawi, kufikira kucha, anachokapo.
12
Ndipo anadza naye mnyamata ali wamoyo, natonthozedwa kwakukulu.
13
Koma ife tinatsogolera kunka kungalawa, ndipo tinapita ku Aso, pamenepo tinati timlandire Paulo; pakuti anatipangira chomwecho, koma anati ayenda pamtunda yekha.
14
Ndipo pamene anakomana ndi ife ku Aso, tinamlandira, ndipo tinafika ku Mitilene.
15
Ndipo m'mene tidachokerapo, m'mawa mwake tinafika pandunji pa Kiyo; ndi m'mawa mwake tinangokocheza ku Samo, ndi m'mawa mwake tinafika ku Mileto.
16
Pakuti Paulo adatsimikiza mtima apitirire pa Efeso, angataye nthawi m'Asiya; pakuti anafulumira, ngati kutheka, akhale ku Yerusalemu tsiku la Pentekoste.
17
Ndipo pokhala ku Mileto anatuma ku Efeso, naitana akulu a Mpingo.
18
Ndipo pamene anafika kuli iye, anati kwa iwo, Mudziwa inu kuyambira tsiku loyamba ndinafika ku Asiya, makhalidwe anga pamodzi ndi inu nthawi yonse,
19
wotumikira Ambuye ndi kudzichepetsa konse ndi misozi, ndi mayesero anandigwera ndi ziwembu za Ayuda;
20
kuti sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m'nyumba zanu,
21
ndi kuchitira umboni Ayuda ndi Agriki wa kutembenuka mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
22
Ndipo, taonani, ndipita ku Yerusalemu womangidwa mumzimu, wosadziwa zimene zidzandigwera ine kumeneko;
23
koma kuti Mzimu Woyera andichitira umboni m'midzi yonse, ndi kunena kuti nsinga ndi zisautso zindilindira.
24
Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.
25
Ndipo tsopano, taonani, ndidziwa ine kuti inu nonse amene ndinapitapita mwa inu kulalikira ufumuwo, simudzaonanso nkhope yanga.
26
Chifukwa chake ndikuchitirani umboni lero lomwe, kuti ndilibe kanthu ndi mwazi wa anthu onse.
27
Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.
28
Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa Iye yekha.
29
Ndidziwa ine kuti, nditachoka ine, adzalowa mimbulu yosautsa, yosalekerera gululo;
30
ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.
31
Chifukwa chake dikirani, nimukumbukire kuti zaka zitatu sindinaleka usiku ndi usana kuchenjeza yense wa inu ndi misozi.
32
Ndipo tsopano ndikuikizani kwa Mulungu, ndi kwa mau a chisomo chake, chimene chili ndi mphamvu yakumangirira ndi kupatsa inu cholowa mwa onse oyeretsedwa.
33
Sindinasirira siliva, kapena golide, kapena chovala cha munthu aliyense.
34
Mudziwa inu nokha kuti manja anga awa anatumikira zosowa zanga, ndi za iwo akukhala ndi ine.
35
M'zinthu zonse ndinakupatsani chitsanzo, chakuti pogwiritsa ntchito, kotero muyenera kuthandiza ofooka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.
36
Ndipo m'mene ananena izi, anagwada pansi, napemphera ndi iwo onse.
37
Ndipo onsewa analira kwambiri, namkupatira Paulo pakhosi pake, nampsompsona,
38
nalira makamaka chifukwa cha mau adanenawa, kuti sadzaonanso nkhope yake. Ndipo anamperekeza iye kungalawa.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28