bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Kings 10
1 Kings 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 11 →
1
Mfumukazi ya ku Sheba itamva za mbiri ya Solomoni yobukitsa dzina la Chauta, idadza ku Yerusalemu kudzamuyesa ndi mafunso apatali.
2
Idabwera ndi atumiki ambiri ndi ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri ndi miyala yamtengowapatali. Itafika kwa Solomoni, idamuuza zonse za kumtima kwake.
3
Solomoni adayankha mafunso ake onse. Panalibe kanthu kalikonse kobisika kwa Solomoniyo, kamene sadathe kuimasulira mfumukaziyo.
4
Tsono itaona nzeru zonse za Solomoni, nyumba imene adaamanga ija,
5
chakudya cha patebulo pake, m'mene zinkakhalira nduna zake, m'mene ankasungira mwambo atumiki ake ndi zovala zao, atumiki ake operekera zakumwa, ndiponso nsembe zake zopsereza zimene ankapereka ku Nyumba ya Chauta, mfumukaziyo idangoti kukamwa pululu, kusoŵa chonena.
6
Pamenepo idauza mfumu Solomoni kuti, “Zimene ndinkamva ndili ku dziko lakwathu, zonena za ntchito zanu ndi nzeru zanu, nzoonadi.
7
Zimenezo sindidazikhulupirire, mpaka nditafika ndi kuziwona chamaso. Ndipotu anthu sadaandiwuze zonse, ngakhale ndi theka lomwe. Nzeru zanu ndiponso zabwino zimene muli nazo zikuposa zimene ndinkazimva.
8
Ngodala anthu anu. Ngodala atumiki anuŵa, amene amaima pamaso panu nthaŵi zonse ndi kumamva nzeru zanu.
9
Atamandike Chauta, Mulungu wanu, amene wakondwera nanu, nakukhazikani pa mpando waufumu wa dziko la Israele. Chifukwa choti Chauta adakonda Israele mpaka muyaya, wakuikani kuti mukhale mfumu yolamulira moyenera ndi mwachilungamo.”
10
Itanena zimenezo mfumukaziyo idapatsa mfumu Solomoni golide wa makilogramu 4,000, zokometsera chakudya zambirimbiri, ndiponso miyala yamtengowapatali. Sikudafikenso konse zokometsera zakudya zochuluka chotere zonga zimene mfumukazi ya ku Sheba idapatsa mfumu Solomoni.
11
Zombo za mfumu Hiramu nazonso zidabwera ndi golide wa ku Ofiri. Zidatenganso mitengo yambiri ya alimugi ndi miyala yamtengowapatali.
12
Mitengo imeneyo mfumuyo idasemera mizati yochirikizira Nyumba ya Chauta ndi ina yochirikizira nyumba yachifumu. Adasemanso azeze ndi apangwe a anthu oimba. Panalibe mitengo yotere imene idabweranso kapena kuwonekanso mu Israele mpaka lero lino.
13
Mfumu Solomoni adapatsa mfumukazi ya ku Sheba ija zonse zimene inkafuna, ndiponso chilichonse chimene idaapempha, osaŵerengera mphatso zachifumu zimene anali ataipatsa kale. Tsono mfumukaziyo idabwerera ku dziko lakwao pamodzi ndi atumiki ake aja.
14
Golide amene ankabwera kwa Solomoni pa chaka chimodzi ankakwanira makilogramu 23,000,
15
osaŵerengera amene ankabwera ndi alendo ndi anthu amalonda, ndiponso wina wochokera kwa mafumu onse a ku Arabiya, ndi kwa nduna zam'dzikomo.
16
Mfumu Solomoni adapangitsa zishango 200 zazikulu za golide wonsansantha. M'chishango chilichonse munkaloŵa golide pafupi makilogramu asanu ndi awiri.
17
Adapanganso zishango 300 zazing'ono za golide wonsansantha. M'chishango chilichonse munkaloŵa golide wokwanira kilogramu limodzi ndi theka. Tsono mfumu idaika zishangozo m'Nyumba ya Nkhalango ya ku Lebanoni.
18
Mfumu idapangitsanso mpando waukulu waufumu wa minyanga yanjovu, niwukuta ndi golide wabwino kwambiri.
19
Mpando waufumuwo unali ndi makwerero asanu ndi limodzi okafikirapo, ndipo chosamira chake unali woulungika pamwamba. Mpandowo unali ndi chosanjikapo manja uku ndi uku, ndipo zifanizo ziŵiri za mikango itaima pambali pa zosanjikapo manjazo.
20
Panalinso mikango pa mbali zonse ziŵiri za khwerero lililonse, mikango khumi ndi iŵiri yonse pamodzi. Mpando wotere sudapezekepo mu ufumu wina uliwonse.
21
Zikho zonse zimene mfumu Solomoni ankamwera zinali zopangidwa ndi golide. Ziŵiya zonse za ku Nyumba ya Nkhalango ya Lebanoni nazonso zinali za golide weniweni. Panalibe zasiliva popeza kuti silivayo sanali kanthu pa nthaŵi ya Solomoni.
22
Mfumu inali ndi zombo zochokera ku Tarisisi zimene zinkayenda pa nyanja pamodzi ndi zombo za Hiramu; ndipo chaka chachitatu chilichonse zinkabwera zitanyamula golide, siliva, minyanga yanjovu, anyani ndi apusi.
23
Motero mfumu Solomoni adapambana mafumu onse a pa dziko lonse lapansi pa chuma ndi pa nzeru.
24
Ndipo anthu onse a pa dziko lapansi ankafunafuna kuti amuwone Solomoni ndi kumva nzeru zake zimene Mulungu adaaika mumtima mwake.
25
Aliyense mwa iwowo ankabwera ndi mphatso zake, zinthu zasiliva ndi zagolide, zovala, zida zankhondo, zokometsera chakudya, akavalo ndi abulu. Ndipo zimenezi zinkhachitika choncho chaka ndi chaka.
26
Choncho Solomoni adasonkhanitsa magaleta ndiponso anthu okwera pa akavalo. Magaletawo anali nawo 1,400, anthu okwera pa akavalo analipo 12,000. Adaŵakhazika ena ku mizinda yokhalako ankhondo, ena pafupi ndi mfumu ku Yerusalemu.
27
Tsono mu Yerusalemumo mfumu idasandutsa siliva kukhala wambiri ngati miyala wamba. Adasandutsanso mikungudza kukhala wochuluka ngati mikuyu ya m'zigwa.
28
Solomoni ankagula akavalo ku Ejipito ndi ku Kuwe. Anthu amalonda a mfumu ankalandirira akavalo ku Kuwe, atapereka ndalama.
29
Anthuwo ankagula galeta ku Ejipito pa mtengo wa masekeli asiliva okwana 600, ndipo kavalo pa mtengo wa masekeli asiliva 150. Momwemonso mafumu onse a Ahiti ndi a ku Siriya, nawonso ankhagula zinthuzo kudzera mwa anthu amalonda omwewo.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22