bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Kings 5
1 Kings 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 6 →
1
Tsono Hiramu mfumu ya ku Tiro adatuma akazembe ake kwa Solomoni, atamva kuti adamdzoza ufumu m'malo mwa bambo wake, poti Hiramuyo ankakondana ndi Davide nthaŵi zonse.
2
Ndipo Solomoni adabweza mau kwa Hiramu akuti,
3
“Mukudziŵa kuti Davide, bambo wanga, sadathe kumangira nyumba Chauta Mulungu wake, chifukwa cha nkhondo zomwe adani ake adaamzinga nazo mbali zonse. Koma potsiriza Chauta adapereka adani akewo mu ulamuliro wake.
4
Tsopano Chauta Mulungu wanga wandipatsa mtendere mbali zonse za dziko, kotero kuti ndilibe mdani kapena chovuta chilichonse.
5
Choncho ndikufuna kumangira nyumba Chauta Mulungu wanga, monga momwe Iye adaauzira bambo wanga Davide kuti, ‘Mwana wako amene ndidzamukhazike pa mpando wako waufumu m'malo mwako, ndiye amene adzandimangire nyumba.’
6
Nchifukwa chake tsono, mulamule anthu anu kuti andidulire mikungudza ya ku Lebanoni. Tsono anthu anga adzagwira ntchito pamodzi ndi anthu anuwo, ndipo ine ndidzakulipirani chifukwa cha anthu anu malipiro amene mungatchule. Inu mukudziŵa kuti pakati pathupa, palibe munthu wodziŵa kudula mitengo ngati Asidoni.”
7
Tsono Hiramu atamva mau a Solomoniwo, adakondwa kwambiri, ndipo adati, “Lero Chauta atamandike chifukwa adapatsa Davide mwana wanzeru kuti alamulire mtundu wotchukawu.”
8
Ndipo adabweza mau kwa Solomoni akuti, “Ndamva zimene mwandipempha. Ndili wokonzeka kuchita zonse zimene mukufunazo, zoti anthu anga akudulireni mitengo ya mkungudza ndi ya paini.
9
Anthu anga adzatsika nayo kuchokera kuno ku Lebanoni mpaka ku nyanja. Ndipo adzaiyandamitsa pa madzi pa phaka, kuti apite nayo ku malo amene munene. Tsono adzaimasulira kumeneko, ndipo inu mudzailandira. Chofuna ine nchongoti inuyo mudzandipatse chakudya chodyetsa anthu anga.”
10
Choncho Hiramu adapereka kwa Solomoni mitengo yonse ya mkungudza ndi ya paini imene ankakhumbayo.
11
Ndipo Solomoni adapatsa Hiramu tirigu wokwanira mitanga 20,000 kuti akhale chakudya cha anthu ake, ndiponso mafuta oyenga bwino okwanira mbiya zikuluzikulu 20,000. Ankapereka zimenezi kwa Hiramu chaka ndi chaka.
12
Tsono Chauta adampatsa Solomoni nzeru monga momwe adaalonjezera. Choncho panali mtendere pakati pa Hiramu ndi Solomoni, ndipo aŵiriwo adachita chipangano cha ubwenzi.
13
Mfumu Solomoni adayambitsa ntchito yathangata m'dziko lonse la Israele. Ndipo anthu athangatawo analipo 30,000.
14
Ankaŵatuma ku Lebanoni anthu 10,000 pamwezi, mosinthanasinthana. Ku Lebanoni ankakhalako mwezi umodzi, ndipo kwao ankakhalako miyezi iŵiri. Adoniramu ndiye amene ankayang'anira ntchito yathangatayo.
15
Solomoni analinso ndi anthu amtengatenga 70,000, ndi anthu 80,000 osema miyala ku dziko lamapiri.
16
Analinso ndi akapitao 3,300 amene ankayang'anira anthu ogwira ntchito.
17
Mfumu idalamula kuti anthuwo akumbe ndi kusema miyala ikuluikulu yabwino kwabasi, yoti akamangire maziko a Nyumba ya Chauta.
18
Amisiri omanga a Solomoni, pamodzi ndi a Hiramu, ndiponso anthu a ku Gebala, ndiwo amene ankasema miyala, ndi kukonza mitengo ndi miyala yomangira Nyumbayo.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22