bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Kings 17
1 Kings 17
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 18 →
1
Mneneri Eliya wa ku Tisibe ku Giliyadi, adauza Ahabu kuti, “Pali Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene ndimamtumikira, sipakhala mame kapena mvula zaka zikubwerazi, mpaka ine ntanena.”
2
Kenaka Chauta adauza Eliyayo kuti,
3
“Chokako kuno, upite chakuvuma, ukabisale ku mtsinje wa Keriti, kuvuma kwa Yordani.
4
Uzikamwa mumtsinjemo, ndipo ndalamula makwangwala kuti azikakudyetsa kumeneko.”
5
Choncho Eliyayo adapita nakachita monga momwe Chauta adaanenera. Adapita nakakhala m'mbali mwa mtsinje wa Keriti kuvuma kwa Yordani.
6
Tsono makwangwala ankadzampatsa buledi ndi nyama m'maŵa ndi madzulo. Ndipo ankamwa madzi kumtsinjeko.
7
Patangopita kanthaŵi, mtsinjewo udaphwa, poti kunalibe mvula m'dzikomo.
8
Tsono Chauta adauzanso Eliya kuti,
9
“Nyamuka upite ku Zarefati, mudzi wa ku Sidoni, ndipo ukakhale kumeneko. Ndalamula mai wamasiye wakumeneko kuti azikakudyetsa.”
10
Choncho Eliya adanyamuka napita ku Zarefati. Atafika pa chipata cha mzindawo, adangoona mai wamasiye akutola nkhuni. Tsono adaitana maiyo namuuza kuti, “Patseniko madzi pang'ono, ndimwe.”
11
Pamene mai uja ankapita kukatunga madziwo, Eliya adamuitananso namuuza kuti, “Munditengerekonso kabuledi.”
12
Apo maiyo adati, “Pali Chauta, Mulungu wanu, ine sindidaphike kanthu kalikonse, koma ndili ndi ufa pang'ono m'mbiya, ndi mafuta pang'ono m'nsupa. Tsono ndikutola nkhuni zoti ndikaphikire kaufako, kuti ndikadye ine ndi mwana wanga, kenaka kufa kukhala komweko.”
13
Koma Eliya adauza maiyo kuti, “Musade nkhaŵa. Pitani, mukachite monga mwaneneramo. Koma poyamba mutapeko kaufa pang'ono, mundiphikire kakeke, mubwere nako kuno. Pambuyo pake mukaphikenso kuti mudye inuyo ndi mwana wanu.
14
Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Ufa umene uli m'mbiyawo sudzatha, mafutanso amene ali m'nsupawo sadzatha, mpaka tsiku limene Chauta adzagwetse mvula pa dziko lapansi.’ ”
15
Tsono maiyo adapita, nakachitadi monga momwe adaanenera Eliya. Maiyo ndi Eliya ndiponso onse a pa banja la maiyo adadya ufawo masiku ambiri.
16
Ufa umene unali m'mbiyamo sudathe, mafuta amene anali m'nsupawo sadathenso, monga momwe Chauta adaalankhulira kudzera mwa Eliya.
17
Tsiku lina mwana wa mkazi wamasiye uja, mwini wake nyumba, adadwala. Matenda adakula kwambiri, kotero kuti mwanayo adamwalira.
18
Mkazi uja adafunsa Eliya kuti, “Kodi ndakulakwirani chiyani, inu mneneri wa Mulungu? Kodi mwadza kwa ine kuno kudzakumbutsa Mulungu machimo anga ndi kundiphera mwana wanga?”
19
Eliya adauza maiyo kuti, “Tandipatsani mwanayo.” Pompo Eliya adatenga mwanayo pa mfukato ya mai uja, napita naye ku chipinda chapamwamba, kumene ankagona, ndipo adakamgoneka pa bedi lake.
20
Kenaka Eliya adatama Chauta mopemba kuti, “Inu Chauta, Mulungu wanga, kodi mai wamasiyeyu, amene akundisunga, mwamchitiranji choipa chotere, pomuphera mwana wake?”
21
Tsono adafungatira mwanayo katatu, natamanso Chauta mopemba kuti, “Inu Chauta, Mulungu wanga, mubwezereni moyo wake mwanayu.”
22
Ndipo Chauta adamumvera Eliyayo. Pomwepo moyo wa mwana uja udabwereranso mwa iye natsitsimuka.
23
Eliya adatenga mwanayo, natsika naye kuchoka m'chipinda chapamwamba chija, ndipo adampereka kwa mai wake. Tsono adauza maiyo kuti, “Onani, mwana wanu ali moyo.”
24
Ndipo mai uja adauza Eliya kuti, “Tsopano ndikudziŵa kuti ndinu munthu wa Mulungu, ndipo Chauta walankhula kudzera mwa inu.”
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22