bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Kings 6
1 Kings 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 7 →
1
Pakutha pa zaka 480 Aisraele atatuluka ku Ejipito, chaka chachinai cha ufumu wa Solomoni wolamulira Aisraele, pa mwezi wa Zivi, umene uli mwezi wachiŵiri, Solomoni adayambapo kumanga Nyumba ya Chauta.
2
Nyumba imene mfumu Solomoni adamangira Chauta muutali mwake inali ya mamita 27, muufupi mwake inali ya mamita asanu ndi anai, ndipo msinkhu wake unali wa mamita pafupi 13 ndi theka.
3
Tsono chipinda chakubwalo m'mimba mwake munali mwa mamita asanu ndi anai, kulingana ndi muufupi mwa Nyumbayo. Kutalika kunali kwa mamita anai ndi theka.
4
Adaika mawindo amene mafuremu ake anali oloŵa m'kati mwa makoma.
5
Adamanganso zipinda zosanjikizana pafupi ndi khoma la Nyumba, kuzungulira makoma a Nyumba yaikuluyo ndi a malo opatulika a m'kati.
6
Chipinda chapansi m'mimba mwake chinali ngati mamita aŵiri, ndipo chipinda chapakati m'mimba mwake chinali ngati mamita aŵiri ndi theka. Chipinda cha pamwamba penipeni m'mimba mwake chinali mamita atatu. Kunja, pa makomawo adamangapo nsolomondo kuzungulira Nyumbayo, kuti asamapise mitanda m'makoma a Nyumbayo.
7
Nyumbayo poimanga, idamangidwa ndi miyala yosemeratu. Choncho pogwira ntchitoyo, sipadamveke nyundo, nkhwangwa kapena chipangizo chilichonse chachitsulo.
8
Chipata choloŵera ku chipinda chapansi chija chinali chakumwera kwa Nyumbayo. Anthu ankachita kukwera makwerero pochoka ku chipinda chapansi kupita ku chipinda chapakati, chimodzimodzi pochoka ku chipinda chapakati kupita ku chipinda chapamwamba.
9
Choncho adamanga Nyumbayo mpaka kuimaliza. Ndipo siling'i yake ya Nyumbayo adaipanga ndi mitanda ndi matabwa amkungudza.
10
Adatsirizanso zipinda zosanjikana kuzungulira Nyumbayo. Chipinda chilichonse msinkhu wake unali ngati mamita aŵiri, ndipo adazilumikiza ku Nyumbayo ndi mitanda yamkungudza.
11
Tsono Chauta adauza Solomoni kuti,
12
“Kunena za Nyumba ukumangayi, iwe ukamamvera mau anga ndi malangizo anga ndi kutsata malamulo anga onse, Ine ndidzakuchitiradi zimene ndidalonjeza kwa Davide bambo wako.
13
Ndiye kuti Ine ndidzakhala pakati pa Aisraele, Aisraele anthu anga sindidzaŵasiya.”
14
Choncho Solomoni adamanga Nyumba ya Chauta naimaliza.
15
Pambuyo pake makoma a Nyumba ya Chauta m'kati mwake Solomoni adaŵachinga ndi matabwa amkungudza, kuyambira pansi pa Nyumbayo mpaka ku siling'i. Pansi pake pa Nyumbayo adayalapo matabwa apaini.
16
Kumbuyo kwa Nyumbayo adadula chipinda kutalika kwake mamita asanu ndi anai. Adachimanga ndi matabwa amkungudza kuyambira pansi mpaka ku siling'i. Chipindachi adachimanga m'kati mwa Nyumbayo, kuti chikhale chipinda chopatulika cham'kati, malo opatulika kopambana.
17
Chigawo cha Nyumba chimene chinali patsogolo pa chipinda chopatulikacho, m'litali mwake chinali mamita 18.
18
M'kati mwa Nyumbayo pa matabwa amkungudza aja adajambulapo zithunzi za zikho ndi za maluŵa. Ponse panali mkungudza wokhawokha, miyala ya khoma osaoneka.
19
Chipinda chopatulika chija adachikonza m'kati mwenimweni mwa Nyumbayo, kuti aikemo Bokosi lachipangano la Chauta.
20
Chinali cha mamita asanu ndi anai ponseponse, m'litali mwake, m'mimba mwake ndiponso mumsinkhu mwake. Ndipo adachikuta ndi golide weniweni. Adapanganso guwa lansembe la matabwa amkungudza.
21
Tsono Solomoni adakuta golide weniweni m'kati mwake mwa Nyumbayo, ndipo adalambalika maunyolo agolide mopingasitsa kutsogolo kwa chipinda chopatulika cham'kati naŵakuta ndi golide. Chipinda chimenechinso chidakutidwa ndi golide.
22
Motero adaikuta Nyumba yonseyo ndi golide mpaka idatha. Guwa lansembe la m'chipinda chopatulika nalonso adalikuta ndi golide.
23
Adapanga akerubi aŵiri a mtengo wa olivi, msinkhu wa aliyense unali mamita anai ndi theka, ndipo adaŵaika m'chipinda chopatulika cham'kati chija.
24
Phiko limodzi la kerubi kutalika kwake kunali mamita aŵiri nkanthu, phiko linanso kutalika kwake mamita aŵiri nkanthu. Kufunyulula mapiko aŵiriwo, kuchokera nsonga ina mpaka nsonga ina, kutalika kwake kunali mamita anai ndi theka.
25
Kerubi winayo msinkhu wake unalinso mamita anai ndi theka. Akerubi aŵiri onsewo anali a misinkhu yofanana ndi a mapangidwe ofanananso.
26
Kerubi mmodzi msinkhu wake unali mamita anai ndi theka, kerubi winayo analinso chimodzimodzi.
27
Solomoni adaika akerubiwo m'chipinda cha m'kati mwenimweni mwa Nyumbayo. Ndipo mapiko ao adaŵatambalitsa kotero kuti phiko limodzi la kerubi mmodzi linkakhudza khoma lina, ndipo phiko limodzinso la kerubi winayo linkakhudza khoma lina. Mapiko enawo ankakhudzana pakati pa Nyumba.
28
Ndipo akerubiwo adaŵakuta ndi golide.
29
Adazokota zithunzi za akerubi, mitengo ya mgwalangwa ndi maluŵa, kuzungulira makoma onse a Nyumbayo, ndiponso m'zipinda zam'kati ndi zakunja zomwe.
30
Kenaka adayalanso golide pansi m'Nyumbamo m'zipinda zam'kati ndi zakunja zomwe.
31
Ndipo adapanga zitseko za mtengo wa olivi zoloŵera ku chipinda chopatulika chija. Lentulo pamodzi ndi mphuthu zake zinali ndi mbali zisanu.
32
Pa zitseko ziŵiri zija za mtengo wa olivi adazokotapo zithunzi za akerubi, za mitengo ya mgwalangwa ndi maluŵa. Tsono zitsekozo adazikuta ndi golide, ndipo adapaka golide pa akerubiwo ndi pa mitengo ya mgwalangwa ija.
33
Adapanganso chimodzimodzi mphuthu za mtengo wa olivi za pa khomo la Nyumbayo, zokhala ndi mbali zinai.
34
Ndipo adapanga zitseko ziŵiri za mtengo wa paini. Zigawo ziŵiri za chitseko chimodzi zinali zotha kupindapinda, zigawo ziŵiri za chitseko china zinalinso zotha kupindapinda.
35
Pa zitsekopo adazokotapo akerubi, mitengo ya mgwalangwa ndiponso maluŵa. Ndipo zozokotazo adazikuta ndi golide wopsapsalala.
36
Adamanganso bwalo lam'kati. Makoma ake adapanga ndi miyala yosema mizere itatu, mosinthanitsana ndi mzere umodzi wa matabwa amkungudza.
37
Maziko a Nyumba ya Chauta adamangidwa pa chaka chachinai, mwezi wa Zivi.
38
Tsono pa chaka cha 11 mwezi wa Buli, mwezi wachisanu ndi chitatu, madera onse a Nyumbayo adatha kumangidwa monga momwe kunkafunikira. Nyumbayo adaimanga pa zaka zisanu ndi ziŵiri.
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22