bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Kings 14
1 Kings 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 15 →
1
Pa nthaŵi imeneyo Abiya, mwana wa Yerobowamu, adayamba kudwala.
2
Ndiye Yerobowamu adauza mkazi wake kuti, “Tiye udzizimbaitse, munthu asakudziŵe kuti ndiwe mkazi wa Yerobowamu, ndipo upite ku Silo kwa mneneri Ahiya, amene adanena za ine, kuti ndidzakhala mfumu yolamulira anthu aŵa.
3
Utenge mitanda khumi yabuledi, makeke ndiponso botolo la uchi, upite kwa iyeyo. Iye adzakuuza zimene zidzamuwonekere mwanayu.”
4
Mkazi wa Yerobowamu adadzizimbaitsadi, ndipo adapita ku Silo, nakafika ku nyumba ya Ahiya. Ahiya sankatha kupenya bwino, ankangoona ngati nkhungu, chifukwa cha ukalamba.
5
Chauta adauza Ahiya kuti, “Taona, mkazi wa Yerobowamu akubwera kudzafunsa iwe za mwana wake, pakuti akudwala. Ndiye iwe udzamuuze zakutizakuti mkaziyo. Akafika adzadzibisa, nkukhala ngati mkazi wina.”
6
Tsono Ahiya atangomva mgugu wa mapazi ake akuloŵa pa khomo, adati “Loŵa, iwe mkazi wa Yerobowamu, bwanji ukudzibisa? Ndakutengera mau oŵaŵa.
7
Pita, kamuuze Yerobowamu kuti Chauta, Mulungu wa Israele, akuti, ‘Ine ndidakukweza pakati pa anthu, ndipo ndidakusandutsa mtsogoleri wa anthu anga a ku Israele.
8
Ndidachotsa ufumu ku banja la Davide ndi kuupereka kwa iwe. Komabe iwe sudafanefane ndi Davide mtumiki wanga, amene ankamvera malamulo anga, ndipo ankanditsata ndi mtima wake wonse, namachita zimene Ine ndimafuna.
9
Koma iwe wachita zoipa kupambana onse amene analipo kale, iwe usanakhale pa mpando waufumu, pakuti wadzipangira milungu ina ndiponso mafano osungunula. Pakutero wandipsetsa mtima kwabasi. Ineyo wanditayiratu kumbuyo.
10
Nchifukwa chake ndidzagwetsa mavuto pa banja lako, iwe Yerobowamu. Ndidzaononga mwamuna aliyense wa pa banja lako, kapolo pamodzi ndi mfulu yomwe, m'dziko la Israele. Ndidzaononga kwathunthu banja la Yerobowamu monga m'mene munthu amachotsera ndoŵe pa bwalo mpaka yonse itatha.
11
Aliyense m'banja la Yerobowamu, amene adzafere mu mzinda, agalu adzamudya. Aliyense amene adzafere ku thengo, mbalame zidzamudya. Ndatero Ine Chauta.’
12
Nchifukwa chake tsono nyamuka, upite kunyumba kwako. Phazi lako likangoponda mumzindamo, mwanayo adzafa.
13
Aisraele onse adzalira maliro ake, ndipo adzamuika, pakuti iye yekhayo mwa anthu a m'banja la Yerobowamu ndiye adzaikidwe ku manda, chifukwa Chauta, Mulungu wa Aisraele, wakondwa ndi iye yekha pa banja lonse la Yerobowamu.
14
Kuwonjezera pamenepo, Chauta adzadzisankhira mfumu yolamulira a ku Israele, imene idzaonongeretu banja la Yerobowamu. Tsiku lake ndi lero, wamvatu!
15
Chauta adzagwedeza Israele ngati bango lapamadzi, ndipo adzachotsa anthu a ku Israele m'dziko labwinoli, limene Iye adapatsa makolo ao. Adzaŵamwazira kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate, chifukwa choti iwo adadzipangira mafano a Asera, mulungu wachikazi, nakwiyitsa Chauta pakutero.
16
Choncho Chauta adzaŵataya a ku Israele chifukwa cha zoipa za Yerobowamu, zimene adachita iye mwini ndi kuŵachimwitsanso Aisraelewo.”
17
Tsono mkazi wa Yerobowamu adachoka napita ku Tiriza. Atangofika pa khomo la nyumba yake, mwana uja adamwalira.
18
Aisraele adamuika, nalira maliro ake, monga momwe Chauta adaanenera kudzera mwa mneneri Ahiya.
19
Tsono ntchito zonse za Yerobowamu, m'mene ankamenyera nkhondo ndi m'mene ankalamulira, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a Aisraele.
20
Nthaŵi imene Yerobowamu adakhala mfumu idakwana zaka makumi aŵiri. Ndipo adamwalira, naikidwa m'manda. Pambuyo pake Nadabu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
21
Rehobowamu, mwana wa Solomoni, anali mfumu ya ku Yuda. Anali wa zaka 41 nthaŵi imene ankaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 17 ku Yerusalemu, mzinda umene Chauta adaausankha pakati pa mafuko onse a Aisraele, kuti anthu azimpembedzerako. Mai wake anali Naama, wa kwa Aamoni.
22
Masiku amenewo anthu a ku Yuda ankachita zoipa, ankachimwira Chauta kupambana m'mene adaachitira makolo ao onse, nakwiyitsa Mulungu.
23
Pakuti iwonso adadzimangira akachisi opembedzerapo mafano pa zitunda zina, ndi kuimika miyala ndi mitengo yachipembedzo pa phiri lalitali lililonse, ndiponso patsinde pa mtengo uliwonse wogudira.
24
Kuwonjezera pamenepo, m'dzikomo munkapezeka anthu ena ochitana zadama potsata chipembedzo chao. Anthu ankachita zonyansa zonse zimene inkachita mitundu ya anthu amene Chauta adaaipirikitsa pofika Aisraele.
25
Chaka chachisanu cha ufumu wa Rehobowamu, Sisake, mfumu ya ku Ejipito, adabwera kudzathira Yerusalemu nkhondo.
26
Adalanda chuma cha ku Nyumba ya Chauta pamodzi ndi chuma cha ku nyumba ya mfumu. Adatenga zonse, ngakhalenso zishango zomwe zagolide zimene Solomoni adaapanga.
27
Pambuyo pake mfumu Rehobowamu adapanga zishango zamkuŵa m'malo mwake, nazipereka m'manja mwa akapitao a alonda amene ankalonda pakhomo pa nyumba ya mfumu.
28
Tsono nthaŵi zonse mfumu ikamaloŵa m'Nyumba ya Chauta, alondawo ankatenga zishangozo, kenaka nkumazibwezera ku chipinda cha alonda.
29
Tsono ntchito zina za Mfumu Rehobowamu, ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.
30
Panali nkhondo zosalekeza pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu.
31
Ndipo Rehobowamu adamwalira, naikidwa mu mzinda wa Davide m'manda momwe adaikidwa makolo ake. Mai wake uja anali Naama, wa mtundu wa Aamoni. Ndipo Abiya, mwana wa Rehobowamu, adaloŵa ufumu m'malo mwa bambo wake.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22