bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Kings 18
1 Kings 18
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 19 →
1
Patapita nthaŵi yaitali, pa chaka chachitatu cha chilala, Chauta adauza Eliya kuti, “Pita ukadziwonetse kwa Ahabu. Ndidzagwetsa mvula pa dziko lapansi.”
2
Motero Eliya adapita kukadziwonetsa kwa Ahabu. Pamenepo nkuti njala itafika pake penipeni ku Samariya.
3
Mfumu Ahabu adaitana Obadiya, amene ankayang'anira zonse za ku nyumba yachifumu. (Ndiye kuti Obadiya ankatumikira Chauta.
4
Ndipo pamene Yezebele ankapha aneneri a Chauta, Obadiya adaabisa aneneri 100. Aneneri 50 adaŵabisa m'phanga lina, 50 ena m'phanga linanso, namaŵapatsa chakudya ndi madzi.)
5
Tsono Ahabu adauza Obadiya kuti, “Tiye tiyendere dziko lonse, tiwone akasupe onse a madzi, ndiponso tipite ku zigwa zonse. Mwina mwake tingapeze udzu womadyetsa akavalo ndi abulu kuti akhale moyo.”
6
Choncho Ahabu ndi Obadiya adagaŵana dzikolo kuti aliyendere. Ahabu adapita mbali ina, Obadiya mbali inanso.
7
Pamene Obadiya ankapita pa ulendo wake, adangoona mneneri Eliya akubwera kudzakumana naye. Obadiya adamzindikira Eliyayo, ndipo adamuŵeramira, namufunsa kuti, “Kodi ndinudi mbuyanga Eliya?”
8
Eliya adayankha kuti, “Ndine amene. Pita ukauze mbuyako kuti Eliya wabwera.”
9
Obadiya adamufunsa kuti, “Kodi ndachimwa chiyani kuti inu mundipereke ine mtumiki wanu m'manja mwa Ahabu kuti andiphe?
10
Pali Chauta, Mulungu wanu wamoyo, kulibe mtundu wa anthu kapena ufumu uliwonse kumene mbuyanga Ahabu sadatumeko anthu okakufunafunani. Anthu akamuuza kuti, ‘Eliya kulibe kuno,’ Ahabu ankaŵalumbiritsa anthuwo kuti atsimikizedi ngati inu kunalibe kumeneko.
11
Ndiye ine mukuti ndipite ndikamuuze mbuyanga kuti mwabwera?
12
Mwina ine ndikangochoka pano, pompo mzimu wa Chauta ukuchotsani kuno kunka nanu komwe ine sindidziŵa. Tsono ndikakamuuza Ahabu, iye osadzakupezani, adzandipha, ngakhale kuti mtumiki wanune ndakhala ndikutumikira Chauta kuyambira ubwana wanga.
13
Kodi inu mbuyanga simudamve zoti nthaŵi imene Yezebele ankapha aneneri a Chauta, ine ndidabisa aneneri 100 a Chauta, anthu 50 m'phanga limodzi, 50 ena m'phanga lina, ndipo kuti ndinkaŵadyetsa chakudya ndi kumaŵapatsa madzi akumwa?
14
Ndiye inu mukuti, ‘Pita, kamuuze mbuyako kuti, “Eliya wabwera?” ’ Ndithu iyeyo adzandipha ine!”
15
Koma Eliya adati, “Ndithudi, pali Chauta Wamphamvuzonse amene ndimamtumikira, ine lero ndikukaonekera pamaso pa Ahabu.”
16
Motero Obadiya adapita kwa Ahabu kukamuuza za Eliyayo. Ndipo Ahabu adapita kukakumana ndi Eliya.
17
Tsono Ahabu ataona Eliya, adamuuza kuti, “Ha, iwe munthu wovuta anthu a ku Israele, wabweradi?”
18
Eliya adayankha kuti, “Ameneyo sindine ai. Koma inuyo pamodzi ndi banja la bambo wanu, ndiye mwakhala mukuvuta anthu a ku Israele, chifukwa mwasiya malamulo a Chauta nkumatsata Abaala.
19
Nchifukwa chake tsopano tumizani mau kuti musonkhanitse onse a ku Israele, kuti abwere, ndikakumane nawo ku Phiri la Karimele. Abwere ndi aneneri a Baala 450, ndiponso aneneri a fano la Asera 400, amene amadya kwa Yezebele.”
20
Pamenepo Ahabu adatumiza mau kwa onse a ku Israele, ndipo adasonkhanitsa aneneri a Baala ku Phiri la Karimele.
21
Eliya adasendera pafupi ndi anthu onsewo, naŵafunsa kuti, “Kodi mudzakhala anthu a mitima iŵiri mpaka liti? Ngati Chauta ndiye Mulungu, mtsateni. Koma ngati Baala ndiye Mulungu, tsatani iyeyo.” Anthuwo sadamuyankhe ndi liwu limodzi lomwe.
22
Tsono Eliya adauza anthu aja kuti, “Ine ndatsala ndekha mwa aneneri a Chauta, koma aneneri a Baala alipo 450 pamodzi.
23
Bwerani ndi ng'ombe zamphongo ziŵiri. Iwo asankhepo okha ng'ombe imodzi ndipo aidule nthulinthuli ndi kuziika pa nkhuni nthulizo, koma asasonkhepo moto ai. Inenso ndidula ng'ombe inayo nthulinthuli, ndi kuikanso nthulizo pa nkhuni, koma osasonkhapo moto ai.
24
Inu mutame dzina la mulungu wanu mopemba, inenso nditana dzina la Chauta mopemba. Tsono Mulungu amene ayankhe potumiza moto, ameneyo ndiyedi Mulungu.” Pamenepo anthu onsewo adati, “Ai, mwanena bwino.”
25
Tsono Eliya adauza aneneri a Baala aja kuti, “Yambani ndinu. Sankhulani ng'ombe yamphongo imodzi, muikonze, poti mwachuluka. Tsono mutame dzina la mulungu wanu mopemba, koma musasonkhe moto ai.”
26
Iwowo adatenga ng'ombe yamphongo imene adaŵapatsa, naipha. Tsono adatama dzina la Baala mopemba, kuyambira m'maŵa mpaka masana, ponena kuti, “Inu a Baala, tiyankheni ife.” Aneneri a Baala aja ankalumphalumpha movina, kuzungulira guwa limene adaamangalo, koma sipadamveke ndi liwu lomwe, panalibe woyankha.
27
Tsono nthaŵi yamasana ndithu Eliya adayamba kuŵaseka, naŵauza kuti, “Fuulani kwambiri, suja mukuti iyeyo ndi mulungu! Mwina mwaketu watanganidwa, kapena wapita kwina kukadzithandiza, kapena ali pa ulendo, kaya kapena ali m'tulo, ndiye kamdzutsenitu.”
28
Aneneri a Baalawo ankafuula kwambiri, nadzichekacheka ndi malupanga ndi mipeni potsata miyambo yao, mpaka magazi chuchuchu m'mabalawo.
29
Dzuŵa litapendeka, adakhala akufuulabe mopenga kufikira nthaŵi yoperekera nsembe idakwana. Komabe kunali zii! Osamveka ndi liwu lomwe. Panalibe woyankha, panalibe ndi mmodzi yemwe wosamalako zimenezo.
30
Pamenepo Eliya adauza anthu onse aja kuti, “Senderani pafupi ndi ine.” Anthu onsewo adasenderadi kwa iyeyo. Tsono Eliya adakonza guwa la Chauta limene linali litagwetsedwa.
31
Adatenga miyala khumi ndi iŵiri potsata chiŵerengero cha mafuko a ana a Yakobe amene Chauta adaamuuza kuti dzina lake lidzakhala Israele.
32
Ndi miyalayo adamangira guwa lotamandirapo Chauta. Tsono adakumba ngalande kuzungulira guwalo. Kukula kwa ngalandeyo kunali ngati moloŵa mitsuko inai ya madzi.
33
Adaika nkhuni zija m'malo mwake, nadula ng'ombe ija nthulinthuli, nkuika nthulizo pankhunipo. Pambuyo pake adauza anthu kuti, “Dzazani mitsuko inai ndi madzi, muŵathire pa nyama yansembeyo, ndi pa nkhunizo.”
34
Ndipo adaŵauza kuti, “Bwerezaninso kachiŵiri.” Anthu aja adathiranso madziwo kachiŵiri. Adaŵauzanso kuti, “Thiraninso kachitatu,” nateronso kachitatu.
35
Madziwo adayenderera kuzungulira guwalo, nadzaza ngalande yonse.
36
Itakwana nthaŵi yake yopereka nsembe, mneneri Eliya adasendera pafupi ndi guwa nati, “Inu Chauta, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Israele, lero zidziŵike kuti Inuyo ndiye Mulungu m'dziko la Israele, ndipo kuti ine ndine mtumiki wanu, ndiponso kuti ndachita zonsezi chifukwa mwanena ndinu.
37
Mundiyankhe, Inu Chauta, mundiyankhe, kuti anthu aŵa adziŵe kuti Inu Chauta ndinu Mulungu, ndipo kuti atembenuke mtima.”
38
Pomwepo moto wa Chauta udagwa, nunyeketsa nsembe yopserezayo, nkhunizo, miyala ija ndi dothi lomwe. Motowo udaphwetsa ndi madzi omwe amene anali m'ngalande aja.
39
Tsono anthu onse ataona zimenezo, adadzigwetsa pansi nanena mokweza kuti, “Chauta ndiyedi Mulungu! Chauta ndiyedi Mulungu!”
40
Pamenepo Eliya adaŵauza kuti, “Gwirani aneneri onse a Baala. Asapulumukepo ndi mmodzi yemwe.” Motero adaŵagwira onsewo. Ndipo Eliya adatsikira nawo ku mtsinje wa Kisoni, nakaŵaphera kumeneko.
41
Pambuyo pake Eliya adauza Ahabu kuti, “Pitani mukadye ndi kumwa, pakuti kukumveka mkokomo wa mvula.”
42
Motero Ahabu adapita kukachita madyerero. Koma Eliya adakwera pamwamba pa Phiri la Karimele, ndipo adazyolikira pansi naika mutu wake pakati pa maondo ake.
43
Tsono adauza mtumiki wake kuti, “Pita ukayang'ane ku nyanja.” Mtumikiyo adapita kukayang'ana, nati, “Kulibe kanthu.” Eliya adamuuza kuti, “Pitanso kasanunkaŵiri.”
44
Mtumikiyo atapita kachisanu ndi chiŵiri adati, “Pali kamtambo kakang'ono konga dzanja la munthu, kakutuluka kunyanjako.” Pompo Eliya adati, “Pita kamuuze Ahabu kuti akonze galeta lake, ndipo azipita, kuti mvula ingamtsekereze.”
45
Posachedwa kuthambo kudangoti bii ndi mitambo, mphepo idaomba ndipo padagwa mvula yaikulu. Ahabu adakwera galeta napita ku Yezireele.
46
Mphamvu za Chauta zinali naye Eliya. Iyeyo adakwinda chovala chake, nathamanga mwaliŵiro, nkupitirira Ahabu mpaka adayambira ndiye kukafika ku chipata cha ku Yezireele.
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22