bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Kings 11
1 Kings 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 12 →
1
Mfumu Solomoni ankakonda akazi ambiri achilendo. Kuwonjezera pa mwana wamkazi wa Farao, adakwatiranso akazi a mitundu iyi: Amowabu, Aamoni, Aedomu, Asidoni ndi Ahiti.
2
Akazi ameneŵa anali a mitundu ija imene Chauta adaauza Aisraele kuti, “Musadzakwatire akazi a mitundu imeneyi, ndipo amuna amitunduyo asadzakwatire akazi a mtundu wanu, poti ndithudi iwowo adzatembenuza mitima yanu, kuti muzitsata milungu yao.” Koma Solomoni ankakondabe akazi a mitundu imeneyo.
3
Iyeyo adakwatira ana achifumu 700 ndipo anali ndi azikazi 300. Ndipo akaziwo adamsokoneza.
4
Solomoni atakalamba, akazi akewo adamnyengerera kuti azitsata milungu yachilendo. Choncho sadatsate Chauta, Mulungu wake, ndi mtima umodzi, monga ankachitira Davide bambo wake.
5
Solomoni ankapembedza Asitoreti, mulungu wachikazi wa Asidoni, ndiponso Milikomu, mulungu wonyansa uja wa Aamoni.
6
Motero Solomoni adachimwira Chauta, ndipo sadatsate Chauta ndi mtima wonse, monga ankachitira Davide, bambo wake.
7
Tsono Solomoni adamanga akachisi pa phiri la kuvuma kwa Yerusalemu, kumangira Kemosi, mulungu wonyansa wa Amowabu, ndiponso Moleki mulungu wonyansa wa Aamoni.
8
Akazi ake onse achilendo adaŵamangira malo ofukizirapo lubani ndi operekerapo nsembe kwa milungu yao.
9
Choncho Chauta adakwiyira Solomoni, chifukwa choti mtima wake udaasinthika ndi kusiya Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene adamuwonekera kaŵiri konse,
10
namulamula kuti asatsate milungu ina. Koma Solomoni sadamvere zimene Chauta adamlamulazo.
11
Nchifukwa chake Chauta adamuuza kuti, “Popeza kuti sudasunge chipangano changa ndi malamulo anga amene ndidakulamula, ndithudi ndidzakulanda ufumu, kuuchotsa m'manja mwako, ndi kuupereka kwa mmodzi mwa atumiki ako.
12
Koma chifukwa cha Davide bambo wako, sindidzachita zimenezi iwe uli moyo ai. Ndidzaulanda kwa mwana wako.
13
Komabe sindidzalanda ufumu wonse. Mwana wako ndidzamsiyirako fuko limodzi, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndiponso chifukwa cha mzinda wa Yerusalemu umene ndidausankha.”
14
Tsono Chauta adamuutsira Solomoni mdani dzina lake Hadadi, wa ku Edomu. Hadadiyo anali wa banja laufumu ku Edomuko.
15
Kale ndithu pamene Davide ankamenyana nkhondo ndi Aedomu, Yowabu mkulu wankhondo adaapita kukakwirira Aisraele ophedwa, ndipo adakapha mwamuna aliyense ku Edomuko.
16
Yowabu ndi ankhondo ake adaakhala kumeneko miyezi isanu ndi umodzi, mpaka adapha amuna onse a ku Edomu.
17
Koma Hadadi adaathaŵira ku Ejipito pamodzi ndi Aedomu ena, atumiki a bambo wake. Pamenepo nkuti Hadadiyo ali mwana wamng'ono.
18
Adanyamuka ku Midiyani, napita ku Parani, ndipo adatengako amuna ena ku Paraniko, nakafika ku Ejipito kwa mfumu Farao. Farao adapatsa Hadadi ndi anthu ake nyumba ndi chakudya, namninkhanso kadziko.
19
Tsono Farao adakomera mtima Hadadi, kotero kuti adampatsa mlamu wake kuti akhale mkazi wake. Mkaziyo anali mbale wake wa mfumukazi Tapenesi wa ku Ejipito.
20
Tsono mkazi wa Hadadiyo adabala mwana wamwamuna dzina lake Genubati, ndipo Tapenesi adalerera Genubati ku nyumba yaufumu. Genubatiyo ankakhala m'nyumba ya Farao pamodzi ndi ana a Farao.
21
Koma Hadadi atamva ku Ejipitoko kuti Davide adamwalira, ndiponso kuti Yowabu mtsogoleri wankhondo nayenso adafa, adauza Farao kuti, “Loleni ndichoke kuti ndipite ku dziko lakwathu.”
22
Koma Farao adati, “Chakusoŵa nchiyani kwathu kuno kuti uziti ukufuna kupita ku dziko lakwanu?” Hadadi adauza Farao kuti, “Iyai sizimenezo, mungondilola basi kuti ndizipita.”
23
Mulungu adautsiranso Solomoni mdani wina, dzina lake Rezoni, mwana wa Eliyada, amene anali atathaŵa kwa mbuyake Hadadezere, mfumu ya ku Zoba.
24
Munthu ameneyu adasonkhanitsa anthu, nakhala mtsogoleri wao wa gulu la achifwamba. Izi zidachitika pamene Davide adati atagonjetsa Hadadezere, adapha ankhondo a ku Zoba. Tsono Rezoni ndi gulu lake adapita ku Damasiko, nakakhala kumeneko, ndipo anthuwo adamlonga ufumu womalamulira dziko la Siriya.
25
Rezoni anali mdani wa Israele masiku onse a Solomoni, namamvuta Solomoniyo monga momwe Hadadi ankachitira.
26
Winanso woukira Solomoni anali Yerobowamu, mwana wa Nebati wa fuko la Efuremu, wa ku Zereda. Anali mmodzi mwa nduna za Solomoni, amene mai wake anali Zeruya, mkazi wamasiye.
27
Nkhani ya kuukira kwakeyo idaayenda motere: Solomoni adaamanga linga la Milo, nakonza khoma logumuka la mzinda wa Davide bambo wake.
28
Yerobowamu anali munthu wolimba mtima, ndipo Solomoni ataona kuti mnyamatayo ngwachangu, adamuika kuti akhale kapitao woyang'anira ntchito yathangata m'dziko la ana a Yosefe.
29
Ndiye tsiku lina pamene Yerobowamu anali pa ulendo kuchokera ku Yerusalemu, mneneri Ahiya wa ku Silo adampeza pa mseu. Ahiyayo anali atavala mwinjiro watsopano, ndipo aŵiriwo anali okha kuthengoko.
30
Tsono Ahiya adagwira mwinjiro watsopano adaavalawo, nkuung'amba m'zidutswa khumi ndi ziŵiri.
31
Ndipo adauza Yerobowamu kuti, “Iwe utengeko zidutswa khumi. Pakuti Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Ndithudi, Ine ndikuchotsa ufumu m'manja mwa Solomoni, ndipo iwe ndidzakupatsa mafuko khumi.
32
Solomoni ndidzamsiyira fuko limodzi, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndiponso chifukwa cha Yerusalemu, mzinda umene ndausankha pa mafuko onse a Aisraele.
33
Ndidzachita zimenezi chifukwa Solomoniyo wandisiya Ine, wayamba kupembedza Asitoreti, mulungu wamkazi wa Asidoni, Kemosi mulungu wa Amowabu, ndi Milikomu mulungu wa Aamoni. Choncho sadandimvere, sadachite zimene ine ndifuna, ndipo sadasunge malamulo anga ndi malangizo anga, monga momwe ankachitira Davide, bambo wake.
34
Komabe sindidzamlanda ufumu iyeyo. Adzakhalabe wolamulira masiku onse a moyo wake, chifukwa cha Davide mtumiki wanga amene ndidamsankha, amene ankasunga malamulo anga.
35
Tsono ufumuwo ndidzauchotsera m'manja mwa mwana wake, ndipo iwe ndidzakupatsa mafuko khumi.
36
Komabe mwana wake ndidzamsiyira fuko limodzi kuti pakhalebe Davide mtumiki wanga azidzakhala ndi nyale nthaŵi zonse pamaso panga ku Yerusalemu, mzinda umene ndausankha kuti azindipembedza kumeneko.
37
Ndidzatenga iweyo Yerobowamu, udzalamulira paliponse pamene mtima wako ufuna, ndipo udzakhala mfumu ya Israele.
38
Ukamamvera zonse zimene ndikukulamula, ndi kumayenda m'njira zanga, ndi kumachita zimene Ine ndifuna, posunga malamulo anga monga m'mene ankachitira Davide, mtumiki wanga, ndiye kuti Ine ndidzakhala nawe. Ndipo zidzukulu zako zidzalamulira monga m'mene ndidalonjezera Davide. Chigawo cha Israele ndidzachipereka kwa iwe.
39
Chifukwa cha kuchimwa kwa Solomoniku, ndidzazunza zidzukulu za Davide, koma osati nthaŵi zonse ai.’ ”
40
Nchifukwa chake Solomoni ankafunitsitsa kupha Yerobowamu. Koma Yerobowamu adachoka nathaŵira ku Ejipito, kwa Sisake mfumu yakumeneko. Adakhala kumeneko mpaka Solomoni atamwalira.
41
Tsono ntchito zina za Solomoni, ndi zonse zimene adachita, ndiponso nzeru zake, zidalembedwa m'buku la Ntchito za Solomoni.
42
Iye adalamulira Aisraele ku Yerusalemu zaka makumi anai.
43
Tsono Solomoni adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Davide, bambo wake. Ndipo Rehobowamu, mwana wake, adaloŵa ufumu m'malo mwake.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22