bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Kings 21
1 Kings 21
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 22 →
1
Panali munthu wina wa ku Yezireele dzina lake Naboti. Iyeyo anali ndi munda wamphesa ku Yezireele, pafupi ndi nyumba ya mfumu Ahabu.
2
Tsiku lina, Ahabu adauza Naboti kuti, “Tandipatsa munda wakowu kuti ukhale dimba langa, poti uli pafupi ndi nyumba yanga. M'malo mwake ndidzakupatsa wina wabwino koposa, kapena ngati ufuna, ndidzakupatsa ndalama pa mtengo wake wa mundawo.”
3
Koma Naboti adauza Ahabu kuti, “Ndithu, pali Chauta, sindingakupatseni choloŵa cha makolo anga.”
4
Apo Ahabu adakaloŵa m'nyumba mwake atakwiya, msunamo uli toloo chifukwa cha zimene Naboti wa ku Yezireele adaanena, pakuti adaati, “Sindingakupatseni choloŵa cha makolo anga.” Motero Ahabu adakagona pabedi pake atapenya ku khoma, osafuna ndi kudya komwe.
5
Koma Yezebele, mkazi wake uja, adabwera kwa iye namufunsa kuti, “Chifukwa chiyani nkhope yanu ikuwoneka yosakondwa, ndipo simukufuna chakudya?”
6
Ahabu adauza mkazi wakeyo kuti, “Chifukwa chake nchakuti ine ndinakamba ndi Naboti wa ku Yezireele ndi kumuuza kuti andipatse munda wake wamphesawu kuti ndigule, kapena ngati afuna, ndidzamupatse munda wina m'malo mwake. Koma iyeyo wayankha kuti, ‘Sindidzakupatsani munda wanga wamphesawu.’ ”
7
Apo Yezebele mkazi wakeyo adamufunsa kuti, “Kodi mfumu ya ku Israele sindinu? Dzukani, kadyeni, mtima wanu usangalale. Ine ndidzakutengerani munda wamphesawo kwa Naboti wa ku Yezireele.”
8
Tsono Yezebele adalemba makalata m'dzina la Ahabu, naŵasindikiza ndi chidindo cha mfumu. Adatumiza makalatawo kwa akuluakulu ndi kwa atsogoleri amene ankakhala ndi Naboti mumzinda mwake.
9
M'makalatamo adalembamo kuti, “Lalikani kuti anthu asale zakudya, ndipo Naboti amuike pa malo aulemu.
10
Mupeze anthu aŵiri oipa mtima kuti adzamneneze ndi mau akuti, ‘Iwe watemberera Mulungu ndiponso mfumu.’ Tsono mumtulutsire kunja, ndipo mumponye miyala kuti afe basi.”
11
Motero anthu a mumzinda m'mene ankakhala Nabotiyo, akuluakulu ndi atsogoleri amumzindamo, adachitadi monga momwe adaaŵauzira Yezebele. Potsata mau am'makalata omwe mkaziyo adaŵatumizira,
12
anthuwo adalengeza za kusala zakudya, ndipo adamuika Naboti pa malo aulemu.
13
Anthu aŵiri aja adaloŵa nakhala pamaso pa Nabotiyo. Adayamba akuchita umboni pakhamu pa anthu onse kuti, “Nabotiyu adatemberera Mulungu ndiponso mfumu.” Motero anthuwo adamtulutsira kunja kwa mzinda, namponya miyala mpaka kumupha.
14
Pambuyo pake adatumiza mau kwa Yezebele akuti, “Naboti uja takonza, moti wafa.”
15
Yezebele atangomva zakuti Naboti amponya miyala ndipo wafa, adakauza Ahabu kuti, “Dzukani, katengeni munda wamphesa uja umene Naboti Myezireele, ankakukanizani kugula. Nabotiyo sali moyonso ai, wafa.”
16
Ahabu atangomva kuti Naboti wafa, adanyamuka napita ku munda wamphesa wa Naboti Myezireele, nautenga kuti ukhale wake.
17
Pambuyo pake Chauta adauza Eliya wa ku Tisibe kuti,
18
“Nyamuka, pita ukakumane ndi Ahabu, mfumu ya ku Israele, amene akukhala ku Samariya. Iyeyu ali ku munda wamphesa wa Naboti. Wapita kumeneko kuti akatenge mundawo kuti ukhale wake.
19
Tsono ukamuuze kuti Chauta akukufunsa kuti, ‘Kodi wapha, ndipo walandanso?’ Ukamuuzenso kuti, ‘Chauta akunena kuti, pa malo amene agalu ankanyambita magazi a Naboti, pomweponso agalu adzanyambita magazi ako.’ ”
20
Apo Ahabu adafunsa Eliya kuti, “Kani wandipeza, iwe mdani wanga?” Eliya adayankha kuti, “Ee, ndakupezani, chifukwa inuyo mwadzigulitsa ndi kukhala ngati kapolo wa zoipa zochimwira Chauta.
21
Tsopano Chauta akuti, ‘Ndithu, ndidzakupasula. Ndidzakusesa kwathunthu, ndidzaononga mwamuna aliyense pa banja lako, kapolo kapena mfulu, m'dziko la Israele.
22
Ndipo banja lako ndidzalisandutsa kuti likhale ngati banja la Yerobowamu mwana wa Nebati, ndiponso ngati banja la Baasa mwana wa Ahiya. Nawenso wandikwiyitsa, chifukwa chakuti wachimwitsa anthu a ku Israele’
23
Tsono kunena za Yezebele, Chauta akuti agalu adzamudya Yezebele m'kati mwa malinga a Yezireele.
24
Munthu aliyense wa banja la Ahabu amene adzafere mu mzinda, agalu adzamudya. Ndipo aliyense wa banja limenelo wodzafera ku thengo, mbalame zamumlengalenga ndizo zidzamudye.”
25
Kunena zoona kunalibe ndi mmodzi yemwe amene adadzipereka ku zoipa kuchimwira Chauta ngati Ahabu, amene Yezebele mkazi wake adamkopa.
26
Iyeyo adachita zonyansa kwambiri popembedza mafano, monga m'mene ankachitira Aamori aja, amene Chauta adaŵachotsa pamene Aisraele ankafika.
27
Ahabu atamva mau amenewo, adang'amba zovala zake, navala ziguduli. Adasala zakudya nagona pa zigudulizo, ndipo adayamba kuyenda modzichepetsa.
28
Apo Chauta adauza Eliya wa ku Tisibe kuti,
29
“Kodi waona m'mene Ahabu wadzichepetsera pamaso panga? Popeza kuti wadzichepetsa pamaso panga, sindidzamlanga ndi zonse zija iyeyo ali moyo. Koma ndidzalanga banja lake, kuyambira mwana wake.”
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22