bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Kings 2
1 Kings 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 3 →
1
Nthaŵi yoti Davide amwalire itayandikira, adauza mwana wake Solomoni kuti,
2
“Ine ndi ulendo uno, nchifukwa chake tsono khala wamphamvu ndipo ulimbike mtima.
3
Uzichita zimene Chauta Mulungu wako akulamula. Uziyenda m'njira za Chauta, uzimvera mau, malangizo ndi malamulo a Mulungu, monga momwe adalembedwera m'malamulo a Mose, kuti zonse zizikuyendera bwino kulikonse kumene ungapite.
4
Uzitero kuti Chauta achitedi zimene adalankhula za ine kuti, ‘Ana ako aamuna akamasamala makhalidwe ao ndi kukhala okhulupirika kwa Ine ndi mtima wao wonse ndi mzimu wao wonse, sipadzasoŵa munthu pa banja lako wolamulira Israele.’
5
“Kuwonjezera pamenepo, ukudziŵanso zoipa zimene Yowabu mwana wa Zeruya adandichita, pakupha atsogoleri aŵiri a ankhondo a Aisraele aja, Abinere mwana wa Nere, ndi Amasa mwana wa Yetere. Kuteroko kunali kulipsira pa nthaŵi yamtendere magazi amene anthuwo adaakhetsa pa nthaŵi yankhondo. Koma tsopano ine pokhala mfumu, ndikusenza kuchimwa kwake ndi kuvala mlandu chifukwa cha magazi osachimwawo.
6
Tsono iwe uchite potsata nzeru zako, koma ndithu usalole kuti afe ndi ukalamba ndi kupita ku manda mwamtendere.
7
“Koma ana a Barizilai wa ku Giliyadi, uŵachitire zabwino ndi kuŵalola kuti azidya pamodzi nawe, poti adandichitira chifundo pamene adakumana nane nthaŵi imene ndinkathaŵa Abisalomu mbale wako.
8
“Palinso Simei, mwana wa Gera, Mbenjamini wa ku Bahurimu, amene adaanditukwana momvetsa chisoni, tsiku limene ndinkapita ku Mahanaimu. Koma pamene adadza kudzakumana nane ku Yordani, ndidalumbira m'dzina la Chauta kuti sindidzamupha.
9
Nchifukwa chake tsono usamuyese wosalakwa, poti iwe ndiwe munthu wanzeru. Udzadziŵa wekha choyenera kumchita. Ngakhale ndi nkhalamba, aphedwe ndithu.”
10
Tsono Davide adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wake wa Davideyo.
11
Apo nkuti atalamulira Israele zaka makumi anai. Ku Hebroni adalamulira zaka zisanu ndi ziŵiri, ndipo ku Yerusalemu zaka 33.
12
Choncho Solomoni adakhala pa mpando waufumu wa Davide atate ake. Ndipo ufumu wake unali wokhazikika kwambiri.
13
Tsiku lina Adoniya, mwana wa Hagiti, adafika kwa Bateseba, mai wake wa Solomoni. Bateseba adamufunsa kuti, “Kodi wadzera mtendere?” Iye adati, “Ai, ndi zamtendere ndithu.”
14
Tsono adati, “Koma ndili ndi mau oti ndilankhule nanu.” Bateseba adati, “Lankhula.”
15
Adoniya adati, “Mukudziŵa kuti ufumuwu udaali wanga, ndipo Aisraele onse ankayembekeza kuti ndidzalamulira ndine. Koma zinthu zatembenuka, ufumuwo wapita kwa mbale wanga, popeza kuti adampatsa ndi Chauta.
16
Tsopano ndikukupemphani chinthu chimodzi. Musandikanize ai.” Bateseba adati, “Nena.”
17
Iyeyo adati, “Inuyo mfumu Solomoni sakukanizani, ndiye chonde ndimati mumpemphe kuti andipatse Abisagi, mtsikana wa ku Sunamu uja, kuti akhale mkazi wanga.”
18
Bateseba adati, “Chabwino. Ndikulankhulira kwa mfumu.”
19
Choncho Bateseba adapita kwa mfumu Solomoni kukalankhula naye m'malo mwa Adoniya. Solomoni adanyamuka kuti akumane naye, ndipo adaŵeramira mai wakeyo. Adakhala pa mpando wake waufumu, ndipo adaitanitsa mpando wina kuti mai wake akhalepo. Tsono mai uja adakhala ku dzanja lamanja la mfumuyo.
20
Ndipo maiyo adati, “Ndikufuna kukupemphani kanthu kakang'ono. Chonde musandikanize.” Tsono mfumu idauza mai wakeyo kuti, “Pemphani chimene mukufuna, mai wanga, sindikukanizani.”
21
Maiyo adati, “Mulole kuti Abisagi Msunamu uja apatsidwe kwa Adoniya mbale wanu, kuti akhale mkazi wake.”
22
Mfumu Solomoni adafunsa mai wakeyo kuti, “Chifukwa chiyani mukumpemphera Abisagi Msunamu Adoniyayu? Mpemphereninso ndi ufumu womwe, poti iyeyu ndi mkulu wanga, ndipo akugwirizana ndi wansembe Abiyatara ndiponso Yowabu mwana wa Zeruya.”
23
Pomwepo mfumu Solomoni adalumbira m'dzina la Chauta kuti, “Mulungu andilange koopsa ngati Adoniya saphedwa chifukwa cha zimenezi.
24
Nchifukwa chake, pali Chauta wamoyo, amene adandisankhula ndi kundikhazika pa mpando waufumu wa Davide bambo wanga, nandipatsa ufumuwu monga momwe adalonjezera, Adoniya aphedwa ndithu lero lomwe lino.”
25
Choncho mfumu Solomoni adatuma Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo iye adakamkantha Adoniyayo, naafa.
26
Tsono mfumu idauza wansembe Abiyatara kuti, “Pita ku Anatoti ku minda yako. Uyenera kufa ndithu, koma sindikupha tsopano lino ai, chifukwa udasunga Bokosi lachipangano la Chauta pamaso pa Davide bambo wanga, ndiponso poti udazunzika naye limodzi bambo wanga.”
27
Choncho Solomoni adachotsa Abiyatara pa ntchito yokhala wansembe wa Chauta. Motero zidachitikadi zija adaanena Chautazi za banja la Eli ku Silo.
28
Pamene Yowabu adamva zimenezi, adathaŵira ku hema lopatulika la Chauta nakagwira nsonga za guwa lansembe. Yowabu ndiye uja ankathandiza Adoniya koma osati Abisalomu.
29
Tsono Mfumu Solomoni atamva kuti Yowabu wathaŵira ku hema la Chauta, ndipo kuti wakhala pambali pa guwa lansembe, adatuma Benaya mwana wa Yehoyada namuuza kuti, “Pita, ukamuphe.”
30
Choncho Benaya adapita ku hema la Chauta lija, ndipo adauza Yowabuyo kuti, “Mfumu ikukulamula kuti utuluke.” Koma Yowabuyo adati, “Iyai, ine ndifera pompano.” Apo Benaya adakauzanso mfumu zimene Yowabu adaanena.
31
Mfumu idamuyankha kuti, “Kachite monga momwe iye waneneramo. Ukamuphe, ndipo ukamuike m'manda. Motero udzandichotsera ine pamodzi ndi banja la bambo wanga mlandu wa imfa ya anthu amene Yowabu adaŵapha popanda chifukwa.
32
Chauta adzambwezera ntchito zake zokhetsa magazi chifukwa choti iye adapha ndi lupanga anthu abwino aŵiri aja amene anali osalakwa kupambana iyeyo, bambo wanga Davide osadziŵa. Anthu aŵiriwo ndiwo Abinere mwana wa Nere ndi mtsogoleri wa ankhondo a ku Israele, ndiponso Amasa mwana wa Yetere mtsogoleri wa ankhondo a ku Yuda.
33
Choncho chilango cha magazi omwe adakhetsa aja chibwerere pa Yowabu ndiponso pa zidzukulu zake mpaka muyaya. Koma mtendere wochokera kwa Chauta ukhale pa Davide ndi zidzukulu zake, pa banja lake ndi pa mpando wake waufumu, mpaka muyaya.”
34
Pamenepo Benaya mwana wa Yehoyada adapita nakamkantha Yowabu, nkumupha, ndipo adamuika m'manda ku nyumba yake ku chipululu.
35
Tsono mfumu idaika Benaya mwana wa Yehoyada kuti aziyang'anira gulu lankhondo m'malo mwa Yowabu, ndipo idaika wansembe Zadoki m'malo mwa Abiyatara.
36
Pambuyo pake mfumu idatuma anthu kukaitana Simei, ndipo atabwera, idamuuza kuti, “Umange nyumba yako muno mu Yerusalemu, ndipo uzikhala mommuno, osamatuluka kukayenda kwina kulikonse.
37
Ukadzatuluka ndi kuwoloka mtsinje wa Kidroni, mosapeneka konse udzaphedwa. Magazi ako adzakhala pamutu pako.”
38
Simei adauza mfumu kuti, “Zimene mukunenazi nzabwino. Ine kapolo wanu ndidzachita monga momwe mwaneneramu, mbuyanga mfumu.” Choncho Simei adakhala mu Yerusalemu masiku ambiri.
39
Koma zidangotere kuti patapita zaka zitatu, akapolo aŵiri a Simei adaathaŵira kwa Akisi, mwana wa Maaka, mfumu ya ku Gati. Simei atamva kuti akapolo ake ali ku Gati,
40
adanyamuka pa bulu, napita ku Gati kwa Akisi, kukafunafuna akapolo ake. Simeiyo adapita, ndipo adakaŵatenga akapolo ake aja ku Gati.
41
Tsono Solomoni atamva kuti Simei adaapita ku Gati kuchoka ku Yerusalemu, ndipo kuti adabwerako,
42
adamuitanitsa Simeiyo namufunsa kuti, “Kodi sindidakulumbiritse iwe m'dzina la Chauta ndi kukuchenjeza kwathunthu kuti tsiku limene udzatuluke ndi kupita kwina kulikonse, udzaphedwa? Ndipo iwe udaandiwuza kuti, ‘Zimene mwanenazi nzabwino, ndimvera.’
43
Nanga chifukwa chiyani tsono sudasunge zimene udalumbira kwa Chauta, ndiponso sudasunge lamulo limene ndidakulamula?”
44
Mfumu idauzanso Simei kuti, “Ukudziŵa mumtima mwakomo zoipa zonse zimene udamchita Davide, bambo wanga. Tsopano Chauta akubwezera zoipa zako pa iwe.
45
Koma Chauta adzandidalitsa ine mfumu Solomoni, ndipo mpando waufumu wa Davide adzaukhazikitsa mpaka muyaya.”
46
Pamenepo mfumuyo idalamula Benaya mwana wa Yehoyada. Ndipo iye adatuluka nakamupha Simeiyo. Motero ufumu wa Solomoni udakhazikikadi.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22