bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Kings 4
1 Kings 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 5 →
1
Mfumu Solomoni ankalamulira dziko lonse la Israele,
2
ndipo nduna zake zikuluzikulu zinali izi: Azariya mwana wa Zadoki anali wansembe.
3
Elihorefe ndi Ahiya ana a Sisa, anali alembi. Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri.
4
Benaya mwana wa Yehoyada anali mtsogoleri wankhondo. Zadoki ndi Abiyatara anali ansembe.
5
Azariya mwana wa Natani ankayang'anira nduna zam'zigawo. Zabudi mwana wa Natani anali wansembe ndi mlangizi wapadera wa mfumu.
6
Ahisara anali mkulu woyang'anira nyumba ya mfumu. Ndipo Adoniramu, mwana wa Abida, anali mkulu woyang'anira ntchito zathangata.
7
Solomoni anali ndi nduna khumi ndi ziŵiri zimene adaziika m'zigawo zonse za dziko la Israele. Nduna zimenezi zinkapereka chakudya kwa mfumu ndi banja lake lonse. Nduna iliyonse inkapereka chakudya mwezi umodzi pa chaka.
8
Maina ndi aŵa: Benihuri, ku dziko lamapiri la Efuremu.
9
Benedekere ku mizinda iyi: Makazi, Salabimu, Betesemesi, Etoni ndi Betehanani.
10
Benihesedi ankayang'anira ku mzinda wa Aruboti. Ankayang'aniranso Soko ndi dziko lonse la Hefere.
11
Benabidanabu ankayang'anira dziko lonse la mapiri la Dori. Iyeyo anali atakwatira Tafati mwana wa Solomoni.
12
Baana mwana wa Ahiludi ankayang'anira ku Tanaki, Megido ndi ku Beteseani konse, pafupi ndi Zaretani kunsi kwake kwa Yezireele, ndiponso kuyambira ku Beteseani mpaka ku Abele-Mehola kukafika mpaka ku Yokomeamu.
13
Benigebere ankayang'anira ku Ramoti-Giliyadi ndi midzi ya Yairo mwana wa Manase, imene ili ku Giliyadi. Analinso ndi chigawo cha Aigobu, chimene chili ku Basani, mizinda yaikulu 60 yokhala ndi malinga ndiponso zitseko zamkuŵa.
14
Abinadabu mwana wa Ido ankayang'anira ku Mahanaimu.
15
Ahimaazi ankayang'anira ku Nafutali. Iyeyu adaakwatira Basemati mwana wa Solomoni.
16
Baana, mwana wa Husai ankayang'anira ku Asere ndi ku Bealoti.
17
Yehosafati, mwana wa Paruwa, ankayang'anira ku Isakara.
18
Simei mwana wa Ela ankayang'anira ku Benjamini.
19
Gebere, mwana wa Uri, ankayang'anira ku dziko la Giliyadi kuphatikizapo dziko limene lidaali la Sihoni mfumu ya Aamori, ndiponso la Ogi mfumu ya ku Basani. Panalinso nduna yaikulu imodzi yoyang'anira dziko lonse la Yuda.
20
Ayuda ndi Aisraele anali ochuluka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Anali okondwa chifukwa anali ndi zakudya ndi zakumwa zambiri.
21
Solomoni ankalamulira maiko onse kuyambira ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku dziko la Afilisti, kukafika mpaka ku malire a Ejipito. Maikowo ankakhoma msonkho ndi kumatumikira Solomoni pa masiku onse a moyo wake.
22
Chakudya chofunika ku nyumba ya mfumu pa tsiku limodzi chinkakwanira madengu 150 a ufa wosalala ndi madengu 300 a mgaiwa,
23
ng'ombe khumi zonenepa zodyetsera m'khola, ng'ombe zakubusa makumi aŵiri, nkhosa 100, osaŵerengera ngondo, nswala, mphoyo ndiponso mbalame zonona zoŵeta.
24
Solomoni ankalamulira dziko lonse la kuzambwe kwa mtsinje wa Yufurate, kuyambira ku Tifisa mpaka ku Gaza. Mafumu onse akumeneko adamgonjera, choncho Solomoni anali pamtendere ndi maiko ozungulira.
25
Choncho nthaŵi yonse Solomoni ali moyo anthu a ku Yuda ndi a ku Israele anali paufulu, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba. Munthu aliyense ankangodzikhalira pamtendere, osasoŵa kanthu kalikonse.
26
Ndipo Solomoni anali ndi zipinda 40,000 zosungiramo akavalo okoka magareta ake, analinso ndi anthu 12,000 okwera pa akavalo.
27
Tsono nduna khumi ndi ziŵiri zija zinkapereka chakudya cha mfumu Solomoni ndi cha anthu onse amene ankadzadya nao kunyumba kwa mfumu, nduna iliyonse mwezi wake. Ndunazo sizinkalola kuti kanthu kalikonse kasoŵe.
28
Barele nayenso ndi udzu wodyetsa akavalo okoka magareta ndiponso akavalo enanso, zonsezo ankabwera nazo kumalo kumene zinkafunika, nduna iliyonse monga m'mene ankaiwuzira.
29
Mulungu adapatsa Solomoni nzeru ndi luntha losaneneka, nzeru zake zinali zopanda malire.
30
Motero nzeru za Solomoni zidapambaniratu nzeru za anthu onse akuvuma, ndiponso za anthu onse a ku Ejipito.
31
Iyeyo anali wanzeru kuposa anthu ena onse, kuposa ngakhale Etani wa ku Ezara, kuposanso Hemani, Kalikoli ndi Darida, ana a Maholi. Ndipo mbiri yake idamveka kwa anthu a mitundu yonse yozungulira dziko lake.
32
Solomoniyo adapeka miyambi 3,000, ndiponso nyimbo zokwanira 1,005.
33
Ankaphunzitsa za mitengo, kuyambira mkungudza wa ku Lebanoni mpaka kachitsamba ka hisope komera pa khoma. Ankaphunzitsanso za nyama, mbalame, zinthu zokwawa pansi ndiponso za nsomba.
34
Motero anthu ankabwera kwa Solomoni kuchokera ku maiko onse, kuti adzamve nzeru zake. Ankatumizidwa ndi mafumu onse a pa dziko lapansi amene anali atamva mbiri ya nzeru zake.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22