bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Numbers 1
Numbers 1
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 2 →
1
Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, m'chihema chokomanako, tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, chaka chachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito, ndi kuti,
2
Werenga khamu lonse la ana a Israele, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba ya makolo ao ndi kuwerenga maina ao, amuna onse mmodzimmodzi.
3
Iwe ndi Aroni muwawerenge monga mwa magulu ao, onse m'Israele akutuluka ku nkhondo, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.
4
Ndipo pamodzi ndi inu pakhale munthu mmodzi wa mafuko onse; yense mkulu wa nyumba ya kholo lake.
5
Ndipo maina a amuna amene aime nanu ndi awa: wa Rubeni, Elizuri mwana wa Sedeuri.
6
Wa Simeoni, Selumiele mwana wa Zurishadai.
7
Wa Yuda, Nasoni mwana wa Aminadabu.
8
Wa Isakara, Netanele mwana wa Zuwara.
9
Wa Zebuloni, Eliyabu mwana wa Heloni.
10
Wa ana a Yosefe: wa Efuremu, Elisama mwana wa Amihudi; wa Manase, Gamaliele mwana wa Pedazuri.
11
Wa Benjamini, Abidani mwana wa Gideoni.
12
Wa Dani, Ahiyezere mwana wa Amisadai.
13
Wa Asere, Pagiyele mwana wa Okarani.
14
Wa Gadi, Eliyasafu mwana wa Deuwele.
15
Wa Nafutali, Ahira mwana wa Enani.
16
Iwo ndiwo oitanidwa a khamu, akalonga a mafuko a makolo ao; ndiwo akulu a zikwizo za Israele.
17
Ndipo Mose ndi Aroni anatenga anthu awa, onenedwa maina ao;
18
nasonkhanitsa khamu lonse tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, ndipo iwo anawakumbira magwero ao kutchula mabanja ao, ndi nyumba za makolo ao, ndi kuwerenga maina kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu mmodzimmodzi.
19
Monga Yehova anauza Mose, momwemo anawawerenga m'chipululu cha Sinai.
20
Ndipo ana a Rubeni, mwana woyamba wa Israele, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina mmodzimmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
21
owerengedwa ao a fuko la Rubeni, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu ndi chimodzi kudza mazana asanu.
22
A ana a Simeoni, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, owerengedwa ao, powerenga maina mmodzimmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
23
owerengedwa ao a fuko la Simeoni, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi zinai kudza mazana atatu.
24
A ana a Gadi, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
25
owerengedwa ao a fuko la Gadi, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu.
26
A ana a Yuda, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
27
owerengedwa ao a fuko la Yuda, ndiwo zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zinai kudza mazana asanu ndi limodzi.
28
A ana a Isakara, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
29
owerengedwa ao a fuko la Isakara, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zinai kudza mazana anai.
30
A ana a Zebuloni, kubadwa kwao, monga nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
31
owerengedwa ao a fuko la Zebuloni, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana anai.
32
A ana a Yosefe, ndiwo a ana a Efuremu, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
33
owerengedwa ao a fuko la Efuremu, ndiwo zikwi makumi anai mphambu mazana asanu.
34
A ana a Manase, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
35
owerengedwa ao a fuko la Manase, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana awiri.
36
A ana a Benjamini, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
37
owerengedwa ao a fuko la Benjamini, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu zisanu kudza mazana anai.
38
A ana a Dani, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
39
owerengedwa ao a fuko la Dani, ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri.
40
A ana a Asere, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
41
owerengedwa ao a fuko la Asere, ndiwo zikwi makumi anai mphambu chimodzi kudza mazana asanu.
42
A ana a Nafutali, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
43
owerengedwa ao a fuko la Nafutali, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai.
44
Iwo ndiwo amene anawerengedwa, amene Mose anawerenga pamodzi ndi Aroni, ndi akalonga a Israele, ndiwo amuna khumi ndi awiri; yense kunenera nyumba ya kholo lake.
45
Potero owerengedwa onse a ana a Israele monga mwa nyumba za makolo ao, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo m'Israele;
46
inde owerengedwa onse ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu.
47
Koma Alevi monga mwa fuko la makolo ao sanawerengedwe mwa iwo.
48
Popeza Yehova adalankhula ndi Mose, ndi kuti,
49
Fuko la Levi lokha usaliwerenge, kapena kuona kufikira kwao mwa ana a Israele;
50
koma iwe, uike Alevi asunge Kachisi wa mboni, ndi zipangizo zake zonse, ndi zonse ali nazo; azinyamula Kachisi, ndi zipangizo zake zonse; namtumikire, namange mahema ao pozungulira pa Kachisi.
51
Ndipo akati amuke naye Kachisiyo, Alevi amgwetse, ndipo akati ammange, Alevi amuimike; ndipo mlendo akayandikizako amuphe.
52
Ndipo ana a Israele amange mahema ao, yense ku chigono chake, ndi yense ku mbendera yake, monga mwa makamu ao.
53
Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa Kachisi wa mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira Kachisi wa mboni.
54
Momwemo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose; anachita momwemo.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36