bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Numbers 20
Numbers 20
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 21 →
1
Ndipo ana a Israele, ndilo khamu lonse, analowa m'chipululu cha Zini mwezi woyamba; ndipo anthu anakhala m'Kadesi; kumeneko anafa Miriyamu, naikidwa komweko.
2
Ndipo khamulo linasowa madzi; pamenepo anasonkhana kutsutsana nao Mose ndi Aroni.
3
Ndipo anthu anatsutsana ndi Mose, nanena, nati, Mwenzi titangomwalira muja abale athu anamwalira pamaso pa Yehova!
4
Mwalowa nao bwanji msonkhano wa Yehova m'chipululu muno, kuti tifere mommuno, ife ndi zoweta zathu?
5
Ndipo munatikwezeranji kutitulutsa m'Ejipito, kutilowetsa m'malo oipa ano? Si malo a mbeu awa, kapena mkuyu, kapena mpesa kapena makangaza; ngakhale madzi akumwa palibe.
6
Ndipo Mose ndi Aroni anachoka pamaso pa msonkhano kunka ku khomo la chihema chokomanako, nagwa nkhope zao pansi; ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera iwo.
7
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
8
Tenga ndodoyo, nusonkhanitse khamulo; iwe ndi Aroni mbale wako, munene ndi thanthwe pamaso pao, kuti liwapatse madzi; potero uwatulutsire madzi m'thanthwe, ndi kumwetsa khamu la anthu ndi zoweta zao.
9
Ndipo Mose anatenga ndodoyo kuichotsa pamaso pa Yehova, monga Iye anamuuza iye.
10
Ndipo Mose ndi Aroni anasonkhanitsa msonkhano pathanthwe, nanena nao iye, Tamvanitu, opikisana naye inu; kodi tikutulutsireni madzi m'thanthwe umu?
11
Ndipo Mose anasamula dzanja lake, napanda thanthwe kawiri ndi ndodo; ndipo madzi anatulukamo ochuluka, ndi khamulo linamwa, ndi zoweta zao zomwe.
12
Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Popeza simunandikhulupirira Ine, kundipatula Ine pamaso pa ana a Israele, chifukwa chake simudzalowetsa msonkhano uwu m'dziko ndinawapatsali.
13
Awa ndi madzi a Meriba; popeza ana a Israele anatsutsana ndi Yehova, ndipo anapatulidwa mwa iwowa.
14
Pamenepo Mose anatumiza amithenga ochokera ku Kadesi kumuka kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Atero mbale wanu Israele, Mudziwa zowawa zonse zinatigwera;
15
kuti makolo athu anatsikira kunka ku Ejipito, ndipo tinakhala m'Ejipito masiku ambiri; ndipo Aejipito anachitira zoipa ife, ndi makolo athu.
16
Pamenepo tinafuulira kwa Yehova, ndipo anamva mau athu, natuma mthenga, natitulutsa m'Ejipito; ndipo, taonani, tili m'Kadesi, ndiwo mudzi wa malekezero a malire anu.
17
Tipitetu pakati pa dziko lanu; sitidzapitira pamunda, kapena munda wampesa, sitidzamwa madzi a m'zitsime; tidzatsata mseu wachifumu; sitidzapatukira kulamanja kapena kulamanzere, mpaka titapitirira malire anu.
18
Koma Edomu ananena naye, Usapitire pakati pa ine, kuti ndingatuluke kukomana nawe ndi lupanga.
19
Ndipo ana a Israele ananena naye, Tidzatsata mseu; ndipo tikakamwa madzi ako, ine ndi zoweta zanga, pamenepo ndidzapatsa mtengo wake; sindifuna kanthu kena koma kungopitapo mwa njira.
20
Koma anati, Usapitirepo. Ndipo Edomu anatulukira kukumana naye ndi anthu ambiri, ndi dzanja lamphamvu.
21
Potero Edomu anakana kulola Israele kupitira pa malire ake; chifukwa chake Aisraele anampatukira.
22
Ndipo anayenda ulendo kuchokera ku Kadesi; ndi ana a Israele, ndilo khamu lonse, anadza kuphiri la Hori.
23
Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni m'phiri la Hori, pa malire a dziko la Edomu, ndi kuti,
24
Aroni adzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake; pakuti sadzalowa m'dziko limene ndapatsa ana a Israele, popeza munapikisana ndi mau anga ku madzi a Meriba.
25
Tenga Aroni ndi Eleazara mwana wake, nukwere nao m'phiri la Hori;
26
nuvule Aroni zovala zake, numveke Eleazara mwana wake; ndipo Aroni adzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake, nadzafa komweko.
27
Pamenepo Mose anachita monga adamulamula Yehova; ndipo anakwera m'phiri la Hori pamaso pa khamu lonse.
28
Ndipo Mose anavula Aroni zovala zake, naveka Eleazara mwana wake; ndipo Aroni anafa pomwepo pamwamba pa phiri. Pamenepo Mose ndi Eleazara anatsika m'phirimo.
29
Pamene khamu lonse linaona kuti Aroni adamwalira, anamlira Aroni masiku makumi atatu, ndiyo mbumba yonse ya Israele.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36