bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Numbers 8
Numbers 8
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 9 →
1
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2
Nena kwa Aroni, nuti naye, Pamene uyatsa nyalizo, nyali zisanu ndi ziwirizo ziwale pandunji pake pa choikapo nyalicho.
3
Ndipo Aroni anachita chotero; anayatsa nyalizo kuti ziwale pandunji pake pa choikapo nyali, monga Yehova adauza Mose.
4
Ndipo mapangidwe ake a choikapo nyali ndiwo golide wosula; kuyambira tsinde lake kufikira maluwa ake anachisula; monga mwa maonekedwe ake Yehova anaonetsa Mose, momwemo anachipanga choikapo nyali.
5
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
6
Uwatenge Alevi pakati pa ana a Israele, nuwayeretse.
7
Ndipo utere nao kuwayeretsa: uwawaze madzi akuchotsa zoipa, ndipo apititse lumo pa thupi lao lonse, natsuke zovala zao, nadziyeretse.
8
Pamenepo atenge ng'ombe yamphongo ndi nsembe yake yaufa, ufa wosanganiza ndi mafuta; utengenso ng'ombe yamphongo ina ikhale nsembe yauchimo.
9
Ndipo ubwere nao Alevi pakhomo pa chihema chokomanako; nuwasonkhanitse khamu lonse la ana a Israele;
10
nubwere nao Alevi pamaso pa Yehova; ndi ana a Israele aike manja ao pa Alevi;
11
ndi Aroni apereke Alevi ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, yochokera kwa ana a Israele, kuti akhale akuchita ntchito ya Yehova,
12
Ndipo Alevi aike manja ao pa mitu ya ng'ombezo; pamenepo ukonze imodzi ikhale nsembe yauchimo, ndi inzake, nsembe yopsereza za Yehova, kuchita chotetezera Alevi.
13
Ndipo uimike Alevi pamaso pa Aroni, ndi pamaso pa ana ake, ndi kuwapereka ngati nsembe yoweyula kwa Yehova.
14
Momwemo upatule Alevi mwa ana a Israele; kuti Alevi akhale anga.
15
Ndipo atatero alowe Alevi kuchita ntchito ya chihema chokomanako; ndipo uwayeretse, ndi kuwapereka ngati nsembe yoweyula.
16
Pakuti aperekedwa konse kwa Ine ochokera mwa ana a Israele; ndadzitengera iwo m'malo mwa onse akutsegula m'mimba, ndiwo oyamba kubadwa a ana a Israele.
17
Pakuti oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele ndi anga, mwa anthu ndi zoweta; tsiku lija ndinakantha oyamba kubadwa onse m'dziko la Ejipito, ndinadzipatulira iwo akhale anga.
18
Ndipo ndatenga Alevi m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele.
19
Ndipo ndapereka Alevi akhale mphatso ya kwa Aroni ndi ana ake amuna yochokera mwa ana a Israele, kuchita ntchito ya ana a Israele, m'chihema chokomanako ndi kuchita chotetezera ana a Israele; kuti pasakhale mliri pakati pa ana a Israele, pakuyandikiza ana a Israele ku malo opatulika.
20
Ndipo Mose ndi Aroni ndi khamu lonse la ana a Israele anachitira Alevi monga mwa zonse Yehova adauza Mose kunena za Alevi; momwemo ana a Israele anawachitira.
21
Ndipo Alevi anadziyeretsa, natsuka zovala zao; ndi Aroni anawapereka ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndi Aroni anawachitira chotetezera kuwayeretsa.
22
Ndipo atatero, Alevi analowa kuchita ntchito yao m'chihema chokomanako pamaso pa Aroni, ndi pamaso pa ana ake amuna; monga Yehova anauza Mose kunena za Alevi, momwemo anawachitira.
23
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
24
Ichi ndi cha Alevi: kuyambira ali wa zaka makumi awiri ndi zisanu ndi mphambu azilowa kutumikira utumikiwu mu ntchito ya chihema chokomanako;
25
ndipo kuyambira zaka makumi asanu azileka kutumikira utumikiwu, osachitanso ntchitoyi;
26
koma atumikire pamodzi ndi abale ao m'chihema chokomanako, kusunga udikirowo, koma osagwira ntchito. Utere nao Alevi kunena za udikiro wao.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36