bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Numbers 21
Numbers 21
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 22 →
1
Pamene Mkanani, mfumu ya Aradi, wokhala kumwera, anamva kuti Israele anadzera njira ya Atarimu, anathira nkhondo pa Israele, nagwira ena akhale ansinga.
2
Ndipo Israele analonjeza chowinda kwa Yehova, nati, Mukadzaperekatu anthu awa m'dzanja langa, ndidzaononga midzi yao konse.
3
Ndipo Yehova anamvera mau a Israele, napereka Akanani; ndipo anawaononga konse ndi midzi yao yomwe; natcha dzina lake la malowo Horoma.
4
Ndipo anayenda ulendo kuchokera kuphiri la Hori, nadzera njira ya Nyanja Yofiira, kupaza ku dziko la Edomu; ndi mtima wa anthu unada chifukwa cha njirayo.
5
Ndipo anthu ananena motsutsana ndi Mulungu, ndi Mose, ndi kuti, Mwatikwezeranji kutichotsa ku Ejipito kuti tifere m'chipululu? Pakuti mkate ndi madzi palibe, ndi mtima wathu walema nao mkate wachabe uwu.
6
Pamenepo Yehova anatumiza njoka zamoto pakati pa anthu, ndipo zinaluma anthu; nafapo anthu ambiri a Israele.
7
Ndipo anthu anadza kwa Mose, nati, Tachimwa, popeza tinanena motsutsana ndi Yehova, ndi inu; pempherani kwa Yehova kuti atichotsere njokazi. Ndipo Mose anawapempherera anthu.
8
Pamenepo Yehova anati kwa Mose, Upange njoka yamoto, nuiike pa mtengo wake; ndipo kudzali, kuti onse olumwa, akuipenya njokayo, adzakhala ndi moyo.
9
Ndipo Mose anapanga njoka yamkuwa, naiika pamtengo; ndipo kunali, njoka itamluma munthu aliyense, nakapenyetsetsa iye pa njoka yamkuwa, nakhala ndi moyo.
10
Pamenepo ana a Israele anayenda ulendo, namanga mahema m'Oboti.
11
Ndipo anachoka ku Oboti, namanga mahema ku Iyeabarimu, m'chipululu chakuno cha Mowabu, kotulukira dzuwa.
12
Pochokapo anayenda ulendo, namanga mahema m'chigwa cha Zeredi.
13
Atachokako anayenda ulendo, namanga mahema tsidya lina la Arinoni, wokhala m'chipululu, wogwera ku malire a Aamori; popeza Arinoni ndiwo malire a Mowabu, pakati pa Mowabu ndi Aamori.
14
Chifukwa chake, ananena m'buku la Nkhondo za Yehova, Waheba m'Sufa, ndi miyendo ya Arinoni;
15
ndi zigwa za miyendoyo zakutsikira kwao kwa Ari, ndi kuyandikizana ndi malire a Mowabu.
16
Ndipo atachokapo anamuka ku Beere, ndicho chitsime chimene Yehova anachinena kwa Mose, Sonkhanitsa anthu, ndipo ndidzawapatsa madzi.
17
Pamenepo Israele anaimba nyimbo iyi, Tumphuka chitsime iwe; muchithirire mang'ombe;
18
chitsime adakumba mafumu, adachikonza omveka a anthu; atanena mlamuli, ndi ndodo zao. Ndipo atachoka kuchipululu anamuka ku Matana;
19
atachoka ku Matana ku Nahaliyele; atachoka ku Nahaliyele ku Bamoti;
20
atachoka ku Bamoti ku chigwa chili m'dziko la Mowabu, ku mutu wa Pisiga, popenyana ndi chipululu.
21
Ndipo Israele anatuma amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, ndi kuti,
22
Ndipitire pakati pa dziko lako; sitidzapatuka kulowa m'munda, kapena m'munda wampesa, sitidzamwako madzi a m'zitsime; tidzatsata mseu wachifumu, kufikira tapitirira malire ako.
23
Ndipo Sihoni sanalole Israele apitire m'malire ake; koma Sihoni anamemeza anthu ake onse, nadzakomana naye Israele m'chipululu, nafika ku Yahazi, nathira nkhondo pa Israele.
24
Ndipo Israele anamkantha ndi lupanga lakuthwa, nalanda dziko lake likhale laolao, kuyambira Arinoni kufikira Yaboki, kufikira ana a Amoni; popeza malire a ana a Amoni ndiwo olimba.
25
Ndipo Israele analanda midzi iyi yonse; nakhala Israele m'midzi yonse ya Aamori; m'Hesiboni ndi milaga yake yonse.
26
Popeza Hesiboni ndiwo mudzi wa Sihoni mfumu ya Aamori, imene idathira nkhondo pa mfumu idafayo ya Mowabu, nilanda dziko lake m'dzanja lake kufikira Arinoni.
27
Chifukwa chake iwo akunena mophiphiritsa akuti, Idzani ku Hesiboni, mudzi wa Sihoni umangike, nukhazikike.
28
Popeza moto unatuluka m'Hesiboni, chirangali cha moto m'mudzi wa Sihoni; chatha Ari wa Mowabu, eni misanje ya Arinoni.
29
Tsoka kwa iwe, Mowabu! Mwaonongeka, anthu a Kemosi inu, anapereka ana ake amuna opulumuka, ndi ana ake akazi akhale ansinga, kwa Sihoni mfumu ya Aamori.
30
Tinawagwetsa; Hesiboni waonongeka kufikira ku Diboni, ndipo tinawapululutsa kufikira ku Nofa. Ndiwo wakufikira ku Medeba.
31
Chomwecho Israele anakhala m'dziko la Aamori.
32
Ndipo Mose anatumiza anthu akazonde Yazere, nalanda milaga yake, napirikitsa Aamori a komweko.
33
Ndipo anatembenuka nakwera kudzera njira ya ku Basani; ndipo Ogi mfumu ya ku Basani anatuluka kukumana nao, iye ndi anthu ake onse, kudzachita nao nkhondo ku Ederei.
34
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Usamuopa; popeza ndampereka m'manja mwako, iye ndi anthu ake onse, ndi dziko lake; umchitire monga umo unachitira Sihoni mfumu ya Aamori anakhalayo ku Hesiboni.
35
Ndipo anamkantha iye, ndi ana ake amuna ndi anthu ake onse, kufikira sanatsale ndi mmodzi yense; nalanda dziko lake likhale laolao.
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36