bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Numbers 34
Numbers 34
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 35 →
1
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2
Uza ana a Israele, nunene nao, Mutalowa m'dziko la Kanani, ndilo dziko logwera inu, likhale cholowa chanu, dziko la Kanani monga mwa malire ake,
3
dera lanu la kumwera lidzakhala lochokera ku chipululu cha Zini, kutsata m'mphepete mwa Edomu, ndi malire anu a kumwera adzakhala ochokera ku malekezero a Nyanja ya Mchere kum'mawa;
4
ndi malire anu adzapinda kuchokera kumwera kunka pokwera Akarabimu, ndi kupitirira ku Zini; ndi kutuluka kwake adzachokera kumwera ku Kadesi-Baranea, nadzatuluka kunka ku Hazara-Adara, ndi kupita kunka ku Azimoni;
5
ndipo malirewo adzapinda ku Azimoni kunka ku mtsinje wa Ejipito, ndi kutuluka kwao adzatuluka kunyanja.
6
Kunena za malire a kumadzulo Nyanja Yaikulu ndiyo malire anu; ndiyo malire anu a kumadzulo.
7
Malire anu a kumpoto ndiwo: kuyambira ku Nyanja Yaikulu mulinge kuphiri la Hori:
8
kuchokera kuphiri la Hori mulinge polowera Hamati; ndipo kutuluka kwake kwa malire kudzakhala ku Zedadi.
9
Ndipo malirewo adzatuluka kunka ku Zifuroni, ndi kutuluka kwake kudzakhala ku Hazara-Enani; ndiwo malire anu a kumpoto.
10
Ndipo mudzilembere malire a kum'mawa ochokera ku Hazara-Enani kunka ku Sefamu;
11
ndi malire adzatsika ku Sefamu kunka ku Ribula, kum'mawa kwa Aini; ndipo malire adzatsika, nadzafikira mbali ya nyanja ya Kinereti kum'mawa,
12
ndi malire adzatsika ku Yordani, ndi kutuluka kwake kudzakhala ku Nyanja ya Mchere; ili ndili dziko lanu monga mwa malire ake polizinga.
13
Ndipo Mose anauza ana a Israele, nati, Ili ndi dzikoli mudzalandira ndi kuchita maere, limene Yehova analamulira awapatse mafuko asanu ndi anai ndi hafu;
14
popeza fuko la ana a Rubeni monga mwa nyumba za makolo ao, ndi fuko la ana a Gadi monga mwa nyumba za makolo ao, adalandira, ndi fuko la hafu la Manase lalandira cholowa chao;
15
mafuko awiriwa ndi hafu adalandira cholowa chao tsidya lija la Yordani ku Yeriko, kum'mawa, kotulukira dzuwa.
16
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
17
Maina a amunawo adzakugawirani dziko likhale cholowa chanu, ndi awa: Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni.
18
Muwatengenso akalonga, kalonga mmodzi ku fuko limodzi, agawe dziko likhale cholowa chao.
19
Maina a amunawo ndiwo: wa fuko la Yuda, Kalebe mwana wa Yefune.
20
Wa fuko la ana a Simeoni, Semuele mwana wa Amihudi.
21
Wa fuko la Benjamini, Elidadi mwana wa Kisiloni.
22
Wa fuko la ana a Dani, kalonga Buki mwana wa Yogili.
23
Wa ana a Yosefe; wa fuko la ana a Manase, kalonga Haniyele mwana wa Efodi.
24
Wa fuko la ana a Efuremu, kalonga Kemuwele mwana wa Sifutani.
25
Wa fuko la ana a Zebuloni, kalonga Elizafani mwana wa Paranaki.
26
Wa fuko la ana a Isakara, kalonga Palatiele mwana wa Azani.
27
Wa fuko la ana a Asere, kalonga Ahihudi mwana wa Selomi.
28
Wa fuko la ana a Nafutali, kalonga Pedahele mwana wa Amihudi.
29
Iwo ndiwo amene Yehova analamulira agawire ana a Israele cholowa chao m'dziko la Kanani.
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 35 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36