bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Numbers 35
Numbers 35
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 34
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 36 →
1
Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'zidikha za Mowabu, pa Yordani, ku Yeriko, ndi kuti,
2
Uza ana a Israele, kuti apatseko Alevi cholowa chaochao, midzi yokhalamo; muwapatsenso Alevi mabusa akuzungulira midzi.
3
Ndipo midzi ndiyo yokhalamo iwowa; ndi mabusa akhale a ng'ombe zao, ndi zoweta zao, inde nyama zao zonse.
4
Ndipo mabusa a midziyo, imene muipereke kwa Alevi ndiwo a mikono chikwi chimodzi kuyambira kulinga kufikira kunja.
5
Ndipo muyese kunja kwa mudzi, mbali ya kum'mawa mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumwera mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumadzulo mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumpoto mikono zikwi ziwiri; ndi mudziwo pakati; ndiwo mabusa a kumidzi.
6
Ndipo midziyo muipereke kwa Alevi ndiyo midzi ija isanu ndi umodzi yopulumukirako; imene muipereke kuti wakupha mnzake athawireko; ndipo pamodzi ndi iyi muperekenso midzi makumi anai ndi iwiri.
7
Midzi yonse muipereke kwa Alevi ndiyo midzi makumi anai ndi isanu ndi itatu, iyo pamodzi ndi mabusa ao.
8
Ndipo kunena za midziyo muiperekeyo yaoyao ya ana a Israele, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang'ono mutengeko pang'ono; onse operekako midzi yao kwa Alevi monga mwa cholowa chao adachilandira.
9
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
10
Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Pakuoloka inu Yordani kulowa m'dziko la Kanani,
11
muikire midzi ikukhalireni midzi yopulumukirako; kuti wakupha mnzake wosati dala athawireko.
12
Ndipo midziyo ikukhalireni yakupulumuka wolipsa; kuti wakupha mnzake asafe, kufikira ataima pamaso pa msonkhano amweruze.
13
Ndipo midziyo muipereke ikukhalireni midzi isanu ndi umodzi yopulumukirako.
14
Mupereke midzi itatu tsidya lino la Yordani, ndi midzi itatu mupereke m'dziko la Kanani, ndiyo yopulumukirako.
15
Midzi isanu ndi umodzi imene ndiyo yopulumukirako ana a Israele, ndi mlendo, ndi wokhala pakati pao; kuti aliyense adamupha munthu osati dala athawireko.
16
Koma akamkantha ndi chipangizo chachitsulo, kuti wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.
17
Kapena akamkantha m'dzanja muli mwala, wakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.
18
Kapena akamkantha m'dzanja muli chipangizo chamtengo, chakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.
19
Wolipsa mwazi mwini wake aphe wakupha munthuyo; pakumpeza amuphe.
20
Ndipo akampyoza momkwiyira, kapena kumponyera kanthu momlalira, kuti wafa;
21
kapena kumpanda ndi dzanja lake momuda, kuti wafa, womkanthayo nayenso amuphe ndithu; ndiye wakupha munthu; wolipsa mwazi aphe wakupha munthuyo akampeza.
22
Koma akampyoza modzidzimuka, osamuda, kapena kumponyera kanthu osamlalira,
23
kapena kumponyera mwala wakufetsa munthu, osamuona, namgwetsera uwu, kuti wafa, koma sindiye mdani wake, kapena womfunira choipa;
24
pamenepo msonkhano uziweruza pakati pa wokantha mnzakeyo ndi wolipsa mwaziyo monga mwa maweruzo awa;
25
ndipo msonkhano umlanditse wakupha munthu m'dzanja la wolipsa mwazi, ndi msonkhanowo umbwezere kumudzi wake wopulumukirako, kumene adathawirako; ndipo azikhalamo kufikira atafa mkulu wa ansembe wodzozedwa ndi mafuta opatulika.
26
Koma wakupha munthu akatuluka nthawi iliyonse kulumpha malire a mudzi wake wopulumukirako kumene anathawirako;
27
nakampeza wolipsa mwazi kunja kwa malire a mudzi wake wothawirako, ndipo wolipsa mwazi akapha wakupha munthu, alibe kuchimwira mwazi;
28
popeza wakupha munthu akadakhala m'mudzi wake wopulumukirako kufikira atafa mkulu wa ansembe; koma atafa mkulu wa ansembe wakupha munthuyo abwere ku dziko lakelake.
29
Ndipo izi zikhale kwa inu lemba la chiweruzo mwa mibadwo yanu, m'nyumba zanu zonse.
30
Aliyense wakantha munthu, wakupha munthuyo aziphedwa pakamwa pa mboni; koma mboni ya munthu mmodzi isafikire kuti munthu afe.
31
Musamalandira dipo lakuombola moyo wa iye adapha munthu, napalamula imfa; koma aziphedwa ndithu.
32
Musamalandira dipo lakuombola iye amene adathawira kumudzi wake wopulumukirako, kuti abwerenso kukhala m'dziko, kufikira atafa mkulu wa ansembe.
33
Ndipo musamaipsa dziko muli m'mwemo; popeza mwazi uipsa dziko; pakuti kulibe kutetezera dziko chifukwa cha mwazi anaukhetsa m'mwemo, koma ndi mwazi wa iye anaukhetsa ndiwo.
34
Usamadetsa dziko ukhala m'mwemo, limene ndikhalitsa pakati pake; popeza Ine Yehova ndikhalitsa pakati pa ana a Israele.
← Chapter 34
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 36 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36