bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Numbers 7
Numbers 7
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 8 →
1
Ndipo kunali kuti tsiku lomwe Mose anatsiriza kumuutsa Kachisi, namdzoza ndi kumpatula, ndi zipangizo zake zonse, ndi guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, nazidzoza ndi kuzipatula;
2
akalonga a Israele, akulu a nyumba za makolo ao, anapereka nsembe, ndiwo akalonga a mafuko akuyang'anira owerengedwa;
3
anadza nacho chopereka chao pamaso pa Yehova, magaleta ophimbika asanu ndi mmodzi, ndi kalonga mmodzi ng'ombe imodzi; nabwera nazo pakhomo pa Kachisi.
4
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
5
Uzilandira kwa iwo, kuti zikhale zakuchitira ntchito ya chihema chokomanako; nuzipereke kwa Alevi, yense monga mwa ntchito yake.
6
Ndipo Mose analandira magaleta ndi ng'ombe, nazipereka kwa Alevi.
7
Anapatsa ana a Geresoni magaleta awiri ndi ng'ombe zinai, monga mwa ntchito yao;
8
napatsa ana a Merari magaleta anai ndi ng'ombe zisanu ndi zitatu, monga mwa ntchito yao; wakuziyang'anira ndiye Itamara mwana wa Aroni wansembe.
9
Koma sanapatse ana a Kohati kanthu; popeza ntchito yao ndiyo ya zinthu zopatulika, zimene amazisenza pa mapewa ao.
10
Ndipo akalonga anabwera nazo za kupereka chiperekere guwa la nsembe tsiku lodzozedwa ili; inde akalongawo anabwera nacho chopereka chao pa guwa la nsembelo.
11
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Akalonga onse, yense pa tsiku lake, apereke zopereka zao za kupereka chiperekere guwa la nsembe.
12
Wakubwera nacho chopereka chake tsiku loyamba ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu, wa fuko la Yuda:
13
chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake ndiko masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwirizo zodzala ndi ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta ukhale nsembe yaufa;
14
chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;
15
ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
16
tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;
17
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Nasoni mwana wa Aminadabu.
18
Tsiku lachiwiri Netanele mwana wa Zuwara, kalonga wa Isakara, anabwera nacho chake:
19
anabwera nacho chopereka chake mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
20
chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;
21
ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
22
tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;
23
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Netanele mwana wa Zuwara.
24
Tsiku lachitatu kalonga wa ana a Zebuloni, ndiye Eliyabu mwana wa Heloni:
25
chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzaza ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
26
chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;
27
ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
28
tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;
29
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Eliyabu mwana wa Heloni.
30
Tsiku lachinai Elizuri, mwana wa Sedeuri, kalonga wa ana a Rubeni:
31
chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika, zonse ziwiri zodzaza ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
32
chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;
33
ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
34
tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;
35
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Elizuri mwana wa Sedeuri.
36
Tsiku lachisanu kalonga wa ana a Simeoni, ndiye Selumiele, mwana wa Zurishadai:
37
chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
38
chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;
39
ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
40
tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;
41
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Selumiele mwana wa Zurishadai.
42
Tsiku lachisanu ndi chimodzi kalonga wa ana a Gadi, Eliyasafu mwana wa Deuwele:
43
chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu; mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
44
chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;
45
ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
46
tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;
47
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Eliyasafu mwana wa Deuwele.
48
Tsiku lachisanu ndi chiwiri kalonga wa ana a Efuremu Elisama mwana wa Amihudi:
49
chopereka chake mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
50
chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;
51
ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
52
tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;
53
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa za mphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Elisama mwana wa Amihudi.
54
Tsiku lachisanu ndi chitatu kalonga wa ana a Manase ndiye Gamaliele mwana wa Pedazuri:
55
chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
56
chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;
57
ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
58
tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;
59
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Gamaliele mwana wa Pedazuri.
60
Tsiku lachisanu ndi chinai kalonga wa ana a Benjamini, ndiye Abidani mwana wa Gideoni:
61
chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
62
chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;
63
ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
64
tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;
65
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Abidani mwana wa Gideoni.
66
Tsiku lakhumi kalonga wa ana a Dani, ndiye Ahiyezere mwana wa Amisadai:
67
chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta ukhale nsembe yaufa;
68
chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;
69
ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
70
tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;
71
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Ahiyezere mwana wa Amisadai.
72
Tsiku la khumi ndi limodzi kalonga wa ana a Asere, ndiye Pagiyele mwana wa Okarani;
73
chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
74
chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;
75
ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
76
tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;
77
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Pagiyele mwana wa Okarani.
78
Tsiku lakhumi ndi chiwiri kalonga wa ana a Nafutali, ndiye Ahira mwana wa Enani:
79
chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
80
chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;
81
ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
82
tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;
83
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ichi ndi chopereka cha Ahira mwana wa Enani.
84
Uku ndi kupereka chiperekere guwa la nsembe, ndi akalonga a Israele, tsiku la kudzoza kwake: mbale zasiliva khumi ndi ziwiri, mbale zowazira zasiliva khumi ndi ziwiri, zipande zagolide khumi ndi ziwiri;
85
mbale yasiliva yonse masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, ndi mbale yowazira yonse masekeli makumi asanu ndi awiri; siliva wonse wa zotengerazo ndizo masekeli zikwi ziwiri ndi mazana anai, kuyesa sekeli wa malo opatulika.
86
Zipande zagolide ndizo khumi ndi ziwiri, zodzala ndi chofukiza, chipande chonse masekeli khumi, kuyesa sekeli wa malo opatulika; golide wonse wa zipandezo ndiwo masekeli zana limodzi ndi makumi awiri;
87
ng'ombe zonse za nsembe yopsereza ndizo ng'ombe khumi ndi ziwiri, nkhosa zamphongo khumi ndi ziwiri, anaankhosa a chaka chimodzi khumi ndi awiri, pamodzi ndi nsembe yao yaufa; ndi atonde a nsembe zauchimo khumi ndi awiri;
88
ndi ng'ombe zonse za nsembe yoyamika ndizo ng'ombe makumi awiri ndi zinai, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi limodzi, atonde makumi asanu ndi limodzi, anaankhosa a chaka chimodzi makumi asanu ndi limodzi. Uku ndi kupereka chiperekere, litadzozedwa guwa la nsembe.
89
Ndipo polowa Mose ku chihema chokomanako, kunena ndi Iye, anamva mau akunena naye ochokera ku chotetezerapo chili pa likasa la mboni, ochokera pakati pa akerubi awiriwo; ndipo Iye ananena naye.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36