bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Numbers 10
Numbers 10
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 11 →
1
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2
Dzipangire malipenga awiri asiliva; uwasule mapangidwe ake; uchite nao poitana khamu, ndi poyendetsa a m'zigono.
3
Akaliza, khamu lonse lisonkhane kuli iwe ku khomo la chihema chokomanako.
4
Akaliza limodzi, pamenepo akalonga, akulu a zikwi a m'Israele, azisonkhana kuli iwe.
5
Mukaliza chokweza ayende a m'zigono za kum'mawa.
6
Mukalizanso chokweza, a m'zigono za kumwera ayende; alize chokweza pakumuka.
7
Pomemeza msonkhano mulize, wosati chokweza ai.
8
Ana amuna a Aroni, ansembe, ndiwo aziliza malipenga; ndipo akhale kwa inu lemba losatha ku mibadwo yanu.
9
Ndipo pamene mupita kunkhondo m'dziko lanu kuchita nkhondo pa mdani wakusautsa inu, mulize chokweza ndi malipenga; ndipo Yehova Mulungu wanu adzakumbukira inu, nadzakupulumutsani kwa adani anu.
10
Momwemo tsiku lakukondwera inu, ndi nyengo zoikidwa zanu, ndi poyamba miyezi yanu, muziliza malipenga pa nsembe zanu zopsereza, ndi pa nsembe zanu zoyamika; ndipo akhale kwa inu chikumbutso pamaso pa Mulungu wanu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
11
Ndipo kunachitika, chaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, tsiku la makumi awiri la mweziwo, kuti mtambo unakwera kuchokera kwa Kachisi wa mboni.
12
Ndipo ana a Israele anayenda monga mwa maulendo ao, kuchokera m'chipululu cha Sinai; ndi mtambo unakhala m'chipululu cha Parani.
13
Potero anayamba ulendo wao monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose.
14
Ndipo anayamba kuyenda ambendera ya chigono cha ana a Yuda monga mwa magulu ao; woyang'anira gulu lake ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu.
15
Ndi pa gulu la fuko la ana a Isakara panali Netanele mwana wa Zuwara.
16
Ndi gulu la fuko la ana a Zebuloni panali Eliyabu mwana wa Heloni.
17
Ndipo anagwetsa Kachisi; ndi ana a Geresoni, ndi ana a Merari, akunyamula Kachisi, anamuka naye.
18
Ndi a mbendera ya chigono cha Rubeni, anayenda monga mwa magulu ao; ndipo pa gulu lake anayang'anira Elizuri mwana wa Sedeuri.
19
Ndi pa gulu la fuko la ana a Simeoni anayang'anira Selumiele mwana wa Zurishadai.
20
Ndi pa gulu la fuko la ana a Gadi anayang'anira Eliyasafu mwana wa Deuwele.
21
Pamenepo Akohati anayenda, ndi kunyamula zopatulika, ndi enawo anautsiratu Kachisi asanafike iwowa.
22
Ndipo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Efuremu, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang'anira Elisama mwana wa Amihudi.
23
Ndi pa gulu la fuko la ana a Manase anayang'anira Gamaliele mwana wa Pedazuri.
24
Ndi pa gulu la fuko la ana a Benjamini anayang'anira Abidani mwana wa Gideoni.
25
Pamenepo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Dani, ndiwo a m'mbuyombuyo a zigono zonse, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang'anira Ahiyezere mwana wa Amisadai.
26
Ndi pa gulu la fuko la ana a Asere anayang'anira Pagiyele mwana wa Okarani.
27
Ndi pa gulu la fuko la ana a Nafutali anayang'anira Ahira mwana wa Enani.
28
Potero maulendo a ana a Israele anakhala monga mwa magulu ao; nayenda ulendo wao.
29
Ndipo Mose anati kwa Hobabu mwana wa Reuwele Mmidiyani mpongozi wa Mose, Ife tili kuyenda kunka ku malo amene Yehova anati, Ndidzakupatsani awa; umuke nafe, tidzakuchitira zokoma; popeza Yehova wanenera Israele zokoma.
30
Koma anati kwa iye, Sindidzamuka nanu; koma ndipita ku dziko langa, ndi kwa abale anga.
31
Koma anati, Usatisiyetu; popeza udziwa poyenera kumanga ife m'chipululu, ndipo udzakhala maso athu.
32
Ndipo kudzatero, ukamuka nafe, inde, kudzali kuti zokoma zilizonse Yehova atichitira ife, zomwezo tidzakuchitira iwe.
33
Ndipo anayenda kuchokera kuphiri la Yehova ulendo wa masiku atatu; ndipo likasa la chipangano cha Yehova, linawatsogolera ulendo wa masiku atatu kuwafunira popumulira.
34
Ndipo mtambo wa Yehova unali pamwamba pao msana, pakuyenda iwo kuchokera kuchigono.
35
Ndipo kunali pakuchokera kunka nalo likasa, Mose anati, Ukani Yehova, abalalike adani anu; akuda Inu athawe pamaso panu.
36
Ndi pakupumula ili anati, Bwerani Yehova kwa zikwizikwi za Israele.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36