bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Numbers 32
Numbers 32
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 33 →
1
Koma ana a Rubeni ndi ana Gadi anali nazo zoweta zambirimbiri; ndipo anapenyerera dziko la Yazere, ndi dziko la Giliyadi, ndipo taonani, malowo ndiwo malo a zoweta.
2
Pamenepo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anadza nanena ndi Mose, ndi Eleazara wansembe, ndi akalonga a khamulo, nati,
3
Ataroti, ndi Diboni, ndi Yazere, ndi Nimira, ndi Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Sibima, ndi Nebo, ndi Beoni,
4
dzikoli Yehova analikantha pamaso pa khamu la Israele, ndilo dziko la zoweta ndipo anyamata anu ali nazo zoweta.
5
Ndipo anati, Ngati tapeza ufulu pamaso panu, mupatse anyamata anu dziko ili likhale laolao; tisaoloke Yordani.
6
Ndipo Mose anati kwa ana a Gadi ndi ana a Rubeni, Kodi abale anu apite kunkhondo, ndi inu mukhale pansi kuno?
7
Ndipo mufoketseranji mtima wa ana a Israele kuti asaoloke ndi kulowa dzikoli Yehova anawapatsa?
8
Anatero makolo anu, muja ndinawatumiza achoke ku Kadesi-Baranea kukaona dziko.
9
Popeza atakwera kunka ku chigwa cha Esikolo, naona dziko, anafoketsa mtima wa ana a Israele, kuti asalowe dzikoli Yehova adawapatsa.
10
Ndipo Yehova anapsa mtima tsiku lija, nalumbira Iye, nati,
11
Anthu adakwerawo kutuluka m'Ejipito, kuyambira wa zaka makumi awiri ndi mphambu sadzaona dziko limene ndinalumbirira Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo; popeza sananditsate Ine ndi mtima wonse;
12
koma Kalebe mwana wa Yefune, Mkenizi, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo; popeza anatsata Yehova ndi mtima wonse.
13
Ndipo Yehova anapsa mtima pa Israele, nawayendetsayendetsa m'chipululu zaka makumi anai, kufikira utatha mbadwo wonsewo udachita choipa pamaso pa Yehova.
14
Ndipo taonani, mwauka m'malo mwa makolo anu, gulu la anthu ochimwa, kuonjezanso mkwiyo waukali wa Yehova pa Israele.
15
Pakuti mukabwerera m'mbuyo kusamtsata Iye, adzawasiyanso m'chipululu, ndipo mudzaononga anthu awa onse.
16
Ndipo anayandikiza, nati Tidzamangira zoweta zathu makola kuno, ndi ana athu midzi;
17
koma ife tidzakhala okonzeka ndi kufulumira pamaso pa ana a Israele, kufikira tidawafikitsa kumalo kwao; ndi ang'ono athu adzakhala m'midzi ya malinga chifukwa cha okhala m'dzikomo.
18
Sitidzabwerera kwathu, kufikira ana a Israele atalandira yense cholowa chake.
19
Pakuti sitidzalandira pamodzi nao tsidya la Yordani, ndi m'tsogolo mwake; popeza cholowa chathu tachilandira tsidya lino la Yordani kum'mawa.
20
Ndipo Mose anati nao, Ngati mudzachita ichi, ndi kudzikonza kunkhondo pamaso pa Yehova,
21
ndi kuoloka Yordani pamaso pa Yehova okonzeka onse mwa inu, kufikira atapirikitsa adani ake pamaso pake,
22
ndi dziko lagonjera Yehova; mutatero mudzabwerere, ndi kukhala osachimwira Yehova ndi Israele; ndipo dziko ili lidzakhala lanulanu pamaso pa Yehova.
23
Koma mukapanda kutero, taonani, mwachimwira Yehova; ndipo zindikirani kuti tchimo lanu lidzakupezani.
24
Dzimangireni midzi ya ana anu, ndi makola a zoweta zanu; ndipo muzichite zotuluka m'kamwa mwanu.
25
Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni ananena ndi Mose, nati, Anyamata anu adzachita monga mbuyanga alamulira.
26
Ana athu, akazi athu, zoweta zathu, ndi ng'ombe zathu zonse, zidzakhala komweko m'midzi ya ku Giliyadi;
27
koma anyamata anu adzaoloka, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova kunkhondo, monga wanena mbuyanga.
28
Pamenepo Mose anamuuza Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a makolo a mafuko a ana a Israele za iwo.
29
Ndipo Mose anati kwa iwo, Ngati ana a Gadi ndi ana a Rubeni aoloka nanu Yordani, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova, ndi dziko lagonjera inu; pamenepo muwapatse dziko la Giliyadi likhale laolao;
30
koma akapanda kuoloka nanu okonzeka, akhale nao maiko aoao pakati pa inu m'dziko la Kanani.
31
Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anayankha, nati, Monga Yehova anati kwa anyamata anu momwemo tidzachita.
32
Tidzaoloka okonzeka pamaso pa Yehova ku dziko la Kanani, koma cholowa chathuchathu chikhale tsidya lino la Yordani.
33
Ndipo Mose anawapatsa, ndiwo ana a Gadi, ndi ana a Rubeni ndi fuko la hafu la Manase mwana wa Yosefe, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, dzikoli ndi midzi yake m'malire mwao, ndiyo midzi ya dziko lozungulirako.
34
Ndipo ana a Gadi anamanga Diboni, ndi Ataroti, ndi Aroere;
35
Ataroti-Sofani, Yazere, ndi Yogobeha;
36
ndi Betenimura, ndi Beteharani: midzi ya m'malinga, ndi makola a zoweta.
37
Ndipo ana a Rubeni anamanga Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Kiriyataimu;
38
ndi Nebo, ndi Baala-Meoni (anasintha maina ao), ndi Sibima; ndipo anaitcha midzi adaimanga ndi maina ena.
39
Ndipo ana a Makiri mwana wa Manase ananka ku Giliyadi, naulanda, napirikitsa Aamori anali m'mwemo.
40
Ndipo Mose anapatsa Makiri mwana wa Manase Giliyadi; ndipo anakhala m'menemo.
41
Ndipo Yairi mwana wa Manase ananka nalanda midzi yao, naitcha Havoti-Yairi.
42
Ndipo Noba ananka nalanda Kenati, ndi milaga yake, nautcha Noba, dzina lake.
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 33 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36