bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Numbers 25
Numbers 25
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 26 →
1
Ndipo Israele anakhala m'Sitimu, ndipo anthu anayamba kuchita chigololo ndi ana akazi a Mowabu;
2
popeza anaitana anthuwo adze ku nsembe za milungu yao; ndipo anthuwo anadya, nagwadira milungu yao.
3
Pamene Israele anaphatikana ndi Baala-Peori, Yehova anapsa mtima pa Israele.
4
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Gwira akulu onse a anthu nuwapachikire Yehova, pali dzuwa poyera, kuti mkwiyo waukali wa Yehova uchoke kwa Israele.
5
Ndipo Mose anati kwa oweruza a Israele, Iphani, yense anthu ake adaphatikanawo ndi Baala-Peori.
6
Ndipo, taonani, anadza wina wa ana a Israele, nabwera naye mkazi Mmidiyani kudza naye kwa abale ake, pamaso pa Mose, ndi pamaso pa khamu lonse la ana a Israele, pakulira iwo pa khomo la chihema chokomanako.
7
Pamene Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, anachiona, anauka pakati pa khamu, natenga nthungo m'dzanja lake;
8
natsata munthu Mwisraele m'hema, nawamoza onse awiri, munthu Mwisraele ndi mkaziyo m'mimba mwake. Pamenepo mliri unaletseka kwa ana a Israele.
9
Ndipo akufa nao mliri ndiwo zikwi makumi awiri ndi zinai.
10
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
11
Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, wabweza kuzaza kwanga pa ana a Israele, popeza anachita nsanje ndi nsanje yanga pakati pao, kotero kuti sindinawatha ana a Israele m'nsanje yanga.
12
Chifukwa chake nena, Taonani, ndimpatsa iye pangano langa la mtendere;
13
ndipo lidzakhala kwa iye, ndi kwa mbeu zake zakumtsata pangano la unsembe wosatha, popeza anachita nsanje chifukwa cha Mulungu wake, anawachitira ana a Israele chowatetezera.
14
Koma dzina la Mwisraele adamuphayo, ndiye amene adamupha pamodzi ndi mkazi Mmidiyani, ndiye Zimiri mwana wa Salu, mfumu ya nyumba ya makolo mwa Asimeoni.
15
Ndi dzina la mkazi Mmidiyani adamuphayo ndiye Kozibi mwana wamkazi wa Zuri; ndiye mkulu wa anthu a nyumba ya makolo m'Midiyani.
16
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
17
Sautsa Amidiyani ndi kuwakantha;
18
popeza akusautsani ndi manyengo ao amene anakunyengani nao; m'chija cha Peori, ndi cha Kozibi, mwana wamkazi wa kalonga wa ku Midiyani, mlongo wao, amene adamupha tsiku la mliri, m'chija cha Peori.
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 26 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36