bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Numbers 33
Numbers 33
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 34 →
1
Maulendo a ana a Israele amene anatuluka m'dziko la Ejipito monga mwa makamu ao, ndi dzanja la Mose ndi Aroni, ndi awa.
2
Ndipo Mose analembera matulukidwe ao monga mwa maulendo ao, monga mwa mau a Yehova; ndipo maulendo ao ndi awa monga mwa matulukidwe ao.
3
Ndipo anachokera ku Ramsesi mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi woyamba; atachita Paska m'mawa mwake ana a Israele, anatuluka ndi dzanja lokwezeka pamaso pa Aejipito onse,
4
pamene Aejipito analikuika oyamba kubadwa ao onse, amene Yehova adawakantha; Yehova adaweruzanso milungu yao.
5
Ndipo ana a Israele anachokera ku Ramsesi, nayenda namanga ku Sukoti.
6
Nachokera ku Sukoti, nayenda namanga m'Etamu, ndiko ku malekezero a chipululu.
7
Ndipo anachokera ku Etamu, nayenda nabwerera ku Pihahiroti, ndiko kutsogolo kwake kwa Baala-Zefoni; namanga iwo patsogolo pa Migidoli.
8
Ndipo anachokera ku Pihahiroti, naoloka pakati pa nyanja nalowa m'chipululu; nayenda ulendo wa masiku atatu m'chipululu cha Etamu, namanga m'Mara.
9
Ndipo anachokera ku Mara, nayenda nafika ku Elimu, ku Elimu ndiko kuli akasupe khumi ndi awiri a madzi, ndi akanjedza makumi asanu ndi awiri; namanga iwo komweko.
10
Ndipo anachokera ku Elimu, nayenda namanga ku Nyanja Yofiira.
11
Nachokera ku Nyanja Yofiira, nayenda namanga m'chipululu cha Sini.
12
Nachokera ku chipululu cha Sini, nayenda namanga m'Dofika.
13
Nachokera ku Dofika, nayenda namanga m'Alusi.
14
Nachokera ku Alusi, nayenda namanga m'Refidimu; kumeneko kunalibe madzi kuti anthu amwe.
15
Ndipo anachokera ku Refidimu, nayenda namanga m'chipululu cha Sinai.
16
Nachokera ku chipululu cha Sinai, nayenda namanga m'Kibroti-Hatava.
17
Nachokera ku Kibroti-Hatava, nayenda namanga m'Hazeroti.
18
Nachokera ku Hazeroti, nayenda namanga m'Ritima.
19
Nachokera ku Ritima, nayenda namanga m'Rimoni-Perezi.
20
Nachokera ku Rimoni-Perezi, nayenda namanga m'Libina.
21
Nachokera ku Libina, nayenda namanga m'Risa.
22
Nachokera Risa, nayenda namanga m'Kehelata.
23
Nachokera ku Kehelata, nayenda namanga m'phiri la Sefera.
24
Nachokera kuphiri la Sefera, nayenda namanga m'Harada.
25
Nachokera ku Harada, nayenda namanga m'Makeloti.
26
Nachokera ku Makeloti, nayenda namanga m'Tahata.
27
Nachokera ku Tahata, nayenda namanga m'Tera.
28
Nachokera ku Tera, nayenda namanga m'Mitika.
29
Nachokera ku Mitika, nayenda namanga m'Hasimona.
30
Nachokera ku Hasimona, nayenda namanga m'Meseroti.
31
Nachokera ku Meseroti, nayenda namanga m'Bene-Yaakani.
32
Nachokera ku Bene-Yaakani, nayenda namanga m'Hori Hagidigadi.
33
Nachokera ku Hori Hagidigadi, nayenda namanga m'Yotibata.
34
Nachokera ku Yotibata, nayenda namanga m'Aborona.
35
Nachokera ku Aborona, nayenda namanga m'Eziyoni-Gebere.
36
Nachokera ku Eziyoni-Gebere, nayenda namanga m'chipululu cha Zini (ndiko Kadesi).
37
Nachokera ku Kadesi, nayenda namanga m'phiri la Hori, ku malekezero a dziko la Edomu.
38
Ndipo Aroni wansembe anakwera m'phiri la Hori pa mau a Yehova, nafa komweko, atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito zaka makumi anai, mwezi wachisanu, tsiku loyamba la mwezi.
39
Ndipo Aroni ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi awiri kudza zitatu pakufa iye m'phiri la Hori.
40
Ndipo Mkanani, mfumu ya Aradi, wakukhala kumwera m'dziko la Kanani, anamva za kudza kwao kwa ana a Israele.
41
Ndipo anachokera kuphiri la Hori, nayenda namanga m'Zalimona.
42
Nachokera ku Zalimona, nayenda namanga m'Punoni.
43
Nachokera ku Punoni, nayenda namanga m'Oboti.
44
Nachokera ku Oboti, nayenda namanga m'Iyeabarimu, m'malire a Mowabu.
45
Nachokera ku Iyimu, nayenda namanga m'Diboni Gadi.
46
Nachokera ku Diboni Gadi, nayenda namanga m'Alimoni-Dibulataimu.
47
Nachokera ku Alimoni-Dibulataimu, nayenda namanga m'mapiri a Abarimu, chakuno cha Nebo.
48
Nachokera ku mapiri a Abarimu, nayenda namanga m'zidikha za Mowabu pa Yordani ku Yeriko.
49
Ndipo anamanga pa Yordani, kuyambira ku Beteyesimoti kufikira ku Abele-Sitimu m'zidikha za Mowabu.
50
Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'zidikha za Mowabu pa Yordani ku Yeriko, nati,
51
Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutaoloka Yordani kulowa m'dziko la Kanani,
52
mupirikitse onse okhala m'dziko pamaso panu, ndi kuononga mafano ao onse a miyala, ndi kuononga mafano ao onse oyenga, ndi kupasula misanje yao yonse;
53
ndipo mulande dziko, ndi kukhala m'mwemo, pakuti ndinakupatsani inu dzikoli likhale lanulanu.
54
Ndipo mulandire dzikoli ndi kuchita maere monga mwa mabanja anu; cholowa chao chichulukire ochulukawo, cholowa chao chichepere ochepawo; kumene maere amgwera munthu, kumeneko nkwake; mulandire cholowa chanu monga mwa mafuko a makolo anu.
55
Koma mukapanda kupirikitsa okhala m'dziko pamaso panu, pamenepo iwo amene muwalola atsale adzakhala ngati zotwikira m'maso mwanu, ndi minga m'mbali zanu, nadzakuvutani m'dziko limene mukhalamo.
56
Ndipo kudzakhala kuti monga ndinayesa kuchitira iwowa, ndidzakuchitirani inu.
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 34 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36