bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Corinthians 1
2 Corinthians 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 2 →
1
Ndine, Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu. Ndili limodzi ndi mbale wathu Timoteo. Tikulembera mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, ndiponso anthu onse a Mulungu okhala m'dziko lonse la Akaiya.
2
Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.
3
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu.
4
Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.
5
Pakuti monga tikumva zoŵaŵa kwambiri pamodzi ndi Khristu, momwemonso Khristu amatilimbitsa mtima kwambiri.
6
Ngati tikuzunzika, nkuti inu mupeze chokulimbitsani mtima ndiponso chipulumutso. Ngati ife atilimbitsa mtima, nkuti inunso mulimbitsidwe mtima ndi kulandira mphamvu za kupirira pamene mulikumva zoŵaŵa zomwezo zimene ifenso timamva.
7
Chikhulupiriro chathu pa inu ncholimba. Tikudziŵa kuti monga mulikumva zoŵaŵa pamodzi nafe, momwemonso mudzapeza chokulimbitsani mtima pamodzi nafe.
8
Tsono abale, tifuna kuti mudziŵe, masautso amene tidakumana nawo ku dziko la Asiya, adatipsinja koopsa, kopitirira mphamvu zathu, kotero kuti sitinkayembekezanso kuti nkukhala ndi moyo.
9
Ndithu m'mitima mwathu tinkangoganiza kuti basi talandira chilango chokaphedwa. Zimenezi zidachitika kuti tisamadzikhulupirire, koma kuti tizikhulupirira Mulungu amene amaukitsa akufa.
10
Ndiye amene adatipulumutsa ku zoopsa zotere za imfa, ndipo adzatipulumutsanso. Taika ndithu chikhulupiriro chathu pa Iyeyo choti adzatipulumutsanso.
11
Inu nomwe muthandizane nafe pakutipempherera. Pamenepo anthu ambiri adzathokoza Mulungu m'malo mwathu, chifukwa cha zimene Iye adatichitira mwa kukoma mtima kwake.
12
Chimene timanyadira nchakuti mtima wathu umatichitira umboni kuti ponseponse pamene tidapita, koma makamakanso pakati panu, mayendedwe athu anali oyera ndi opanda chinyengo. Zinali choncho osati chifukwa chotsata nzeru za anthu ai, koma chifukwa Mulungu adatikomera mtima.
13
Timakulemberani zokhazokha zimene mungathe kuziŵerenga ndi kuzimvetsa bwino. Ndikhulupirira kuti,
14
monga mwayamba kale kutidziŵa pang'ono, mudzatidziŵa kwenikweni, ndiye kuti pa tsiku la Ambuye Yesu mudzatha kutinyadira ife, monga momwe ifenso tidzakunyadirani inu.
15
Popeza kuti pa zimenezi ndinali wotsimikiza ndithu, ndidaaganiza zoti ndiyambe ndafika kwanuko. Ndidaafuna kuti mulandire madalitso paŵiri:
16
ndidaakonza ulendo wanga kuti ndidzere kwanu popita ku Masedoniya, ndi kuti ndidzerenso kwanu pochokera ku Masedoniyako. Ndinkafuna kuti potero mudzandithandize kupitiriza ulendo wanga wopita ku Yudeya.
17
Kodi pamene ndidaaganiza kuchita zimenezi, inu mukuyesa kuti ndidaachita zinthu mwachibwana? Kaya zimene ndimaganiza kuzichita, kodi ndimangoziganiza mwaukapsala, kotero kuti ndingathe kunena kuti, “Inde, inde” ndiponso “Ai, ai” pa nthaŵi imodzi?
18
Pali Mulungu woona, ndikulumbira kuti mau athu amene timakuuzani sali “Inde” ndiponso “Ai”.
19
Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, amene ine ndi Silivano ndi Timoteo tidakulalikirani, sanali “Inde” ndiponso “Ai” pa nthaŵi imodzi, koma nthaŵi zonse anali “Inde” wa Mulungu.
20
Ndipo zonse zimene Mulungu adalonjeza zidachitika ndi “Inde” ameneyu. Nchifukwa chake mwa Yesu Khristuyo timanena kuti, “Amen” kulemekeza Mulungu.
21
Mulungu ndi amene amatikhazikitsa pamodzi nanu mwa Khristu. Ndiye amene adatidzoza,
22
natisindikiza chizindikiro chake, ndi kuika Mzimu Woyera m'mitima mwathu ngati chikole.
23
Mulungu akhale mboni yanga, chifukwa chenicheni chimene sindidafikirenso ku Korinto chinali chakuti ndisakumvetseni chisoni.
24
Sikuti tikufuna kuchita ngati kukulamulirani pa zoti muzikhulupirira, pakuti pa mbali ya chikhulupiriro chanu, ndinu okhazikika ndithu. Makamaka tingofuna kugwirizana nanu kuti mukhale okondwa.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13