bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Corinthians 3
2 Corinthians 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 4 →
1
Kodi ponena izi ndiye kuti tikuyamba kudzichitira umboni tokha? Kodi kapena nkofunika kuti ifenso, monga anthu ena, tikhale ndi makalata otichitira umboni kwa inu, kapena makalata aumboni ochokera kwa inu?
2
Kalata yotichitira umboniyo ndinu nomwe. Idalembedwa m'mitima mwathu, kuti anthu onse aidziŵe ndi kumaiŵerenga.
3
Anthu onse angathe kuwona kuti ndinu kalata yochokera kwa Khristu, yolembedwa kudzera mwa ife, osati ndi inki koma ndi mzimu wa Mulungu wamoyo, osati pa zolembapo zamiyala koma m'mitima mwa anthu.
4
Mulungu akudziŵa kuti tikunena zimenezi chifukwa Khristu ndiye amatipatsa kulimba mtima kotere.
5
Pakuti mwa ife tokha mulibe kanthu kamene kangatiganizitse kuti tingathe kuchita ntchitoyi patokha. Amene amatipatsa mphamvu ndi Mulungu kuti tithe kuichita.
6
Ndiye amene adatipatsa mphamvu kuti tikhale otumikira chipangano chatsopano, osati mwa malamulo olembedwa, koma mwa Mzimu Woyera. Paja malamulo olembedwa amadzetsa imfa, koma Mzimu Woyera amapatsa moyo.
7
Malamulo ongolembedwa pa miyala aja adaperekedwa ndi ulemerero waukulu, kotero kuti Aisraele sankatha kuyang'anitsitsa nkhope ya Mose chifukwa cha kuŵala kwake. Komabe kuŵala kwakeko kunali kosakhalitsa. Tsono ngati malamulowo, amene ali odzetsa imfa, adaperekedwa ndi ulemerero wotere,
8
nanji ntchito ya Mzimu Woyera, kodi siidzakhala ndi ulemerero wopambana pamenepo?
9
Ngati ntchito yoweruza anthu kuti alangidwe inali yaulemerero, ndiye kuti ntchito yoti anthu apezeke olungama pamaso pa Mulungu idzakhala yaulemerero koposa.
10
Chifukwa cha ulemerero wopambanawu umene waoneka tsopano, zinthu zimene kale zidaali ndi ulemerero, masiku ano zilibenso ulemerero konse.
11
Tsono ngati zinthu zosakhalitsa zidaafika ndi ulemerero, ndiye kuti zinthu zokhala mpaka muyaya zidzakhala ndi ulemerero wopambana.
12
Popeza kuti timayembekeza zimenezi, timalimba mtima kwambiri.
13
Sitichita ngati Mose amene ankaphimba nkhope yake ndi nsalu, kuwopa kuti Aisraele angamapenye kutha kwake kwa kuŵala kosakhalitsa kuja.
14
Koma iwo nzeru zao zidauma, pakuti mpaka lero lino chophimba chomwe chija chimakhalapobe akamaŵerenga mabuku a m'Chipangano Chakale. Pajatu chophimbacho chimachotsedwa pokhapokha munthu akakhala mwa Khristu.
15
Ndithu, mpaka lero lino nthaŵi zonse akamaŵerenga Malamulo a Mose, chophimba chija chimaphimbabe mitima yao.
16
Koma munthu akatembenukira kwa Ambuye, chophimbacho chimachotsedwa.
17
Tsono tikamati, “Ambuye,” tikunena Mzimu Woyera. Ndipo kumene kuli Mzimu wa Ambuye, kuli ufulu.
18
Tonsefe, opanda chophimba nkhope yathu, timaonetsa ulemerero wa Ambuye, monga momwe galasi limaonetsera nkhope ya munthu. Monsemo Ambuye, amene ali Mzimu, amatisandutsa kuti tifanefane naye, ndi kukhala nawo ulemerero wake mochulukirachulukira.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13