bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Corinthians 11
2 Corinthians 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 12 →
1
Ndikadakonda kuti mundilekerere pang'ono pa kupusa kwangaku. Tandilekereranipo ndithu.
2
Nsanje imene ndikukuchitirani ndi yonga ya Mulungu. Pakuti ndidakupalitsani ubwenzi ndi mwamuna mmodzi yekha, ngati namwali wangwiro ndi woyera mtima, kuti mukhale akeake a Khristu.
3
Njoka ndi kuchenjera kwake idanyenga Heva. Ndikuwopa kuti maganizo anu angaipitsidwe chimodzimodzi, ndipo mungaleke kudzipereka kwa Khristu ndi mtima wonse.
4
Wina amati akabwera kudzalalika Yesu wina wosiyana ndi amene tidamlalika ife, inu mumangomulekerera. Kapena mukalandira mzimu wina wosiyana ndi Mzimu Woyera amene mudamlandira kale, inu nkumaloladi. Mwinanso mukalandira Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene mudalandira kale, inu nkumauvomeradi msangamsanga.
5
Ndikuganiza kuti atumwi anu apamwambawo sandiposa ine pa kanthu kalikonse.
6
Ngakhale ndine mbuli pa luso lolankhula, koma pa nzeru ndiye ai. Zimenezi ndidakuwonetsani kaŵirikaŵiri pa zonse.
7
Ndidadzitsitsa ndekha ineyo, kuti inu mukule. Ndidakulalikirani mwaulere Uthenga Wabwino wa Mulungu. Kodi ndiye kuti pakutero ndidalakwa?
8
Pakulandira zondithandiza kuchokera ku mipingo ina, ndidachita ngati kuŵalanda zao kuti ndikutumikireni inu.
9
Ndipo pamene ndinali kwanuko, nditasoŵa kanthu, sindidavute aliyense, pakuti abale ena ochokera ku Masedoniya adaandipatsa zonse zimene ndinkasoŵa. Pa zonse ndinkasamala kwambiri kuti ndisakhale ngati katundu wokulemerani, ndipo ndidzapitirirabe kutero.
10
Malinga ndi choona cha Khristu chimene chili mwa ine, ndikunenetsa kuti palibe munthu amene adzandiletsa kunyadira zimenezi m'madera onse a ku Akaiya.
11
Ndikutero chifukwa chiyani? Kodi monga sindikukondani? Akudziŵa ndi Mulungu kuti ndimakukondani.
12
Zimene ndikuchita tsopano, ndidzazichitabe, kuti ndisaŵapatse mpata onyenga aja amene akufuna danga loti anyadire, ndi kumanena kuti iwonso akugwira ntchito molingana ndi ife.
13
Anthu otereŵa si atumwi oona, koma antchito onyenga, amene amadzizimbaitsa, naoneka ngati atumwi a Khristu.
14
Zimenezitu si zododometsa ai, pakuti Satana yemwe amadzizimbaitsa, naoneka ngati mngelo wounikira anthu.
15
Motero si chodabwitsa ngati atumiki ake omwe amadzizimbaitsa, naoneka ngati otumikira chilungamo. Potsiriza adzalandira molingana ndi zimene ankachita.
16
Ndikufuna kubwerezanso kuti munthu wina aliyense asandiyese wopusa. Koma ngati inuyo mukundiyesadi wopusa, chabwino mundilandire ngati chitsiru, kuti inenso ndinyadirepo.
17
Zimene ndimati ndinena panozi si zimene Ambuye afuna kuti ndinene, koma ndikungonyada, monga momwe amachitira wopusa.
18
Tsono popeza kuti ambiri akunyadira zapansipano, inenso ndidzatero.
19
Inu mumati ndinu anzeru kwambiri, nchifukwa chake anthu opusa mumangoŵalekerera mokondwa.
20
Mumangolekerera munthu akakuyesani akapolo, kapena akadya chuma chanu, kapena akakunyengani, kapena akakunyozani, kapena akakumenyani kumaso.
21
Ndikuvomera mwamanyazi kuti ife sitinali olimba mtima kuti nkuchita zotere. Tsopano ndilankhula ngati wopusa: zimene wina aliyense anganyadire, zomwezo inenso ndingathe kuzinyadira.
22
Kodi iwo ndi Ahebri? Inenso. Kodi iwo ndi Aisraele? Inenso. Kodi iwo ndi ana a Abrahamu? Inenso.
23
Kodi iwo ndi atumiki a Khristu? Ndikulankhula ngati wamisala, ndine mtumiki woposa iwowo. Ndidagwira ntchito kwambiri kopambana iwo, kaŵirikaŵiri ndinali pafupi kufa.
24
Kasanu Ayuda adandikwapula mikwapulo 39.
25
Katatu Aroma adandimenya ndi ndodo. Kamodzi anthu adandiponya miyala. Katatu pa maulendo athu apanyanja, chombo chathu chidasweka. Nthaŵi ina ndidayandama pakati pa nyanja tsiku lathunthu, usana ndi usiku.
26
Pa maulendo anga ochuluka ndidakumana ndi zoopsa za mitsinje, zoopsa za achifwamba, zoopsa zochokera kwa Ayuda anzanga, ndi zina zochokera kwa akunja. Ndidapeza zoopsa m'mizinda, m'thengo, ndi pakati pa abale onyenga.
27
Ndidagwira ntchito zolemetsa, ndipo kaŵirikaŵiri sindidalaŵe tulo. Ndidamva njala ndi ludzu, kaŵirikaŵiri osaona chakudya, ndipo kusoŵa zovala ndi kuzizidwa.
28
Kuwonjezera pa zonsezi, tsiku ndi tsiku ndimapsinjidwa ndi udindo wa kusamalira mipingo yonse.
29
Ndani ali wofooka, ine osakhala naye pamodzi m'kufooka kwakeko? Ndani amene mnzake amchimwitsa, ine osavutika mu mtima?
30
Ngati ndiyenera kunyada, ndidzanyadira kufooka kwanga.
31
Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu, amene tiyenera kumtamanda nthaŵi zonse, akudziŵa kuti sindikunama.
32
Pamene ndinali ku Damasiko, bwanamkubwa woimirira mfumu Areta, adaaika alonda kuzinga mzinda wonsewo kuti andigwire.
33
Koma anthu adandiika m'dengu nanditsitsira pa windo la m'lingalo, motero ndidamthaŵira.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13