bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Corinthians 6
2 Corinthians 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 7 →
1
Tsono popeza kuti ndife ogwirizana ndi Mulungu pa ntchito yake, takupembani musaŵasandutse achabe madalitso amene Mulungu adakupatsani.
2
Paja Mulungu akuti, “Pa nthaŵi yanga yabwino ya kukomera anthu mtima, ndidakumvera, pa nyengo ya kupulumutsa anthu, ndidakuthandiza.” Mvetsani, ndi inotu nthaŵi yabwinoyo, imene Mulungu akukomera anthu mtima. Ndi Lerotu tsiku la chipulumutsolo.
3
Sitifuna kupatsa anthu chifukwa chonyozera ntchito yathu, nchifukwa chake sitikhumudwitsa munthu aliyense ndi kanthu kalikonse.
4
Koma pa zonse timasonyeza kuti ndife atumiki a Mulungu pakupirira kwambiri m'masautso, m'zoŵaŵa ndiponso m'nkhaŵa.
5
Tidakwapulidwa, tidaponyedwa m'ndende, ndipo anthu adatiwukira mwachipolowe. Tidagwira ntchito kwambiri, mwina osagona tulo, osaona chakudya.
6
Timatsimikiza kuti ndife atumiki a Mulungu pakuyera mtima, pakudziŵa zinthu mozama, pakuleza mtima, pakukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, mwa chikondi chosanyenga,
7
mwa mau oona, ndiponso mwa mphamvu ya Mulungu. Zida zimene zili m'dzanja lathu lamanja ndi lamanzere ndizo chilungamo.
8
Anthu amatilemekeza, komanso amatinyoza. Amatinenera zoipa, komanso zabwino. Anthu amatiyesa onyenga, komabe ndife oona.
9
Amatiyesa osadziŵika, komabe ndife odziŵika kwambiri. Amatiyesa anthu amene alikufa, komabe onani, tili moyo. Amatiyesa olangidwa, komabe sitidaphedwe.
10
Amatiyesa achisoni, komabe ndife okondwa masiku onse. Amatiyesa amphaŵi, komabe timalemeretsa anthu ambiri. Amatiyesa opanda kanthu, komabe tili ndi zonse.
11
Inu anthu a ku Korinto, talankhula nanu momasuka, ndipo tatsekula mtima wathu ndithu.
12
Malo sakusoŵani mumtima mwathu, koma mumtima mwanu ndimo mukusoŵa malo.
13
Ndikulankhula nanu ngati ana anga. Mutibwezere zomwezo zimene ifenso tidakuchitirani inu, pakutitsekulira mtima wanu.
14
Musamagwirizana ndi anthu akunja, monga ngati kuti iwo ndi inu mumafanana. Nanga kulungama kungagwirizane bwanji ndi kusalungama? Kapena kuŵala kungayanjane bwanji ndi mdima?
15
Kodi Khristu nkuvomerezana ndi Satana? Kodi mkhristu ndi mkunja angagaŵanenso chiyani pamodzi?
16
Kodi Nyumba ya Mulungu nkufanana bwanji ndi mafano? Pajatu ife ndife Nyumba ya Mulungu wamoyo, monga Mulungu mwini adanena kuti, “Ndidzakhazikika mwa iwo, ndi kukhala nawo. Ndidzakhala Mulungu wao, iwo adzakhala anthu angaanga.”
17
Nchifukwa chake Ambuye akuti, “Tulukani pakati pao, ndi kudzipatula. Musakhudze kanthu kosayera, ndipo ndidzakulandirani.
18
Ndidzakhala Atate anu, inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi, akutero Ambuye Mphambe.”
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13