bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Corinthians 7
2 Corinthians 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 8 →
1
Tsono, inu okondedwa, popeza kuti tili ndi malonjezo ameneŵa, tiyeni tidzichotsere zinthu zonse zodetsa thupi lathu kapena mtima wathu. Ndipo pakuwopa Mulungu tiziyesetsa ndithu kukhala oyera mtima.
2
Mutipatse malo m'mitima mwanu. Sitidalakwire munthu aliyense, kapena kumuipitsa, kapena kumchenjerera.
3
Sindikunena zimenezi kuti mupezeke olakwa. Paja monga ndanena kale, inu muli m'mitima mwathu ndithu, kotero kuti tili pamodzi, ngakhale tikhale moyo kapena timwalire.
4
Ndimakukhulupirirani kwambiri, ndipo ndimakunyadirani kwenikweni. Zondilimbitsa mtima zandichulukira, ndipo m'zovuta zathu zonse ndakondwa kopambana.
5
Ngakhale pamene tidafika ku Masedoniya sitidapeze mpumulo konse. Tidapeza zovuta ponseponse, popeza kuti panali kukangana ndi adani otizungulira, ndiponso mantha m'mitima mwathu.
6
Koma Mulungu amene amalimbitsa otaya mtima, adatilimbitsa ndi kufika kwa Tito.
7
Ndipo chimene chidatilimbitsa, si kufika kwake kokha, koma makamakanso mau ake onena za m'mene iyeyo mudamlimbitsira mtima. Adatiwuza kuti mukulakalaka kundiwona, kuti muli ndi chisoni, ndiponso kuti mukuchita changu kundithandiza. Nchifukwa chake ndakondwa koposa.
8
Kalata yanga ija idakupwetekani mtima, komabe sindikuchita chisoni kuti ndidailemba. Ndidaachita chisoni poyamba, ndipo ndikuwona kuti kalatayo idakupwetekanidi mtima, ngakhale kanthaŵi pang'ono chabe.
9
Koma tsopano ndakondwa, osati chifukwa ndidaakupwetekani mtima, koma chifukwa kuvutika kwanu kudakuthandizani kutembenuka mtima. Kuvutika kwanuko kunali kovomerezeka ndi Mulungu, motero sitidakutayitseni kanthu kabwino kalikonse.
10
Paja chisoni chokomera Mulungu chimamtembenuza munthu ndi kumpulumutsa, kotero kuti chisoni chake chimathera pomwepo. Koma kumva chisoni monga m'mene amachitira anthu odalira zapansipano, kumadzetsa imfa.
11
Onani zimene chisoni chanu chokomera Mulungu chija chakuchitirani: chakupatsani changu chachikulu, chakukakamizani kwambiri kutsimikiza kuti simudalakwe, chakukwiyitsani kwambiri, ndipo chakuchititsani mantha aakulu. Chakulakalakitsani kuti mundiwone, ndipo chakupatsani changu chonditchinjiriza, ndiponso cholanga olakwa. Pa nkhani yonseyi umboni ulipo wakuti inu simudalakwepo.
12
Motero, ngakhale ndidakulemberani kalata imene ija, sindidailembe chifukwa cha amene adalakwa uja, kapena chifukwa cha amene iyeyo adamlakwira. Koma ndidailemba kuti ndikuwonetseni pamaso pa Mulungu kuti changu chanu chotitchinjiriza nchachikulu ndithu.
13
Zimenezi zatilimbitsa mtima kwambiri. Kuwonjezera pa zotilimbitsa mtimazo, chimwemwe cha Tito chidatikondweretsa kopambana, popeza kuti nonsenu mudamsangulutsa.
14
Ndidamuuzadi kuti ndimakunyadirani, ndipo inu simudandichititse manyazi. Koma monga momwe zonse zimene tidaakuuzani zinali zoona, momwemonso kudaoneka kuti zimene ndidauza Tito mokunyadirani, zinali zoona.
15
Makamaka chikondi chake pa inu nchachikulu kopambana pamene akumbukira kuti nonsenu mudamvera mau anga, ndipo mudamlandira ndi mantha ndi monjenjemerera.
16
Ndikukondwa kuti ndingathe kukukhulupirirani pa zonse.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13