bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Corinthians 4
2 Corinthians 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 5 →
1
Mulungu mwa chifundo chake adatipatsa ntchitoyi, nchifukwa chake sititaya mtima.
2
Takaniratu njira zonse zochititsa manyazi zimene anthu amatsata mobisika. Sitichita kanthu monyenga kapena kupotoza mau a Mulungu; koma pakulankhula zoona poyera pamaso pa Mulungu, tifuna kuti anthu onse ativomereze m'mitima mwao.
3
Koma ngakhale Uthenga Wabwino umene timalalika uli wophimbika, ngwophimbika kwa okhawo amene akutayika.
4
Iwoŵa sakhulupirira, popeza kuti Satana, amene ali mulungu wa dziko lino lapansi, adachititsa khungu maganizo ao, kuwopa kuti angaone kuŵala kwa Uthenga Wabwino. Kuŵalako kumaonetsa ulemerero wa Khristu, ndipo mwa Iyeyu Mulungu mwini amaoneka.
5
Motero polalika sitidzilalika tokha, koma timalalika Yesu Khristu, kuti ndiye Ambuye. Ife ndife atumiki anu chabe chifukwa cha Yesuyo.
6
Paja ndi Mulungu amene adaati, “Kuŵala kuunike kuchokera mu mdima.” Mulungu yemweyo ndiye adatiwunikiranso m'mitima mwathu, kuti anthu adziŵe ulemerero wa Mulungu umene ukuŵala pa nkhope ya Khristu.
7
Koma ife ndife mbiya zadothi chabe zosungiramo chumachi, kuti padziŵike kuti mphamvu zazikulu zoterezi ndi za Mulungu, osati zathu ai.
8
Tikuwona masautso a mtundu uliwonse, koma osapsinjidwa. Tikuthedwa nzeru, koma osataya mtima.
9
Adani akutizunza, koma sitisoŵa wotithandiza. Akutigwetsa pansi, koma sitikugonja.
10
Nthaŵi zonse tikuyenda nayo imfa ya Yesu m'thupi mwathu, kuti moyo wake uwonekenso m'thupi mwathu.
11
Pakuti nthaŵi zonse, ngakhale tili ndi moyo, tikuperekedwa ku imfa chifukwa cha Yesu, kuti moyo wake uwonekenso m'matupi athu amene amafa.
12
Motero ife timaperekedwa ku imfa, koma chimenechi chimakupatsani moyo.
13
Malembo akuti, “Ndidakhulupirira, nchifukwa chake ndidalankhula.” Tsono popeza kuti ife tili ndi mtima womwewo wokhulupirira, ifenso timalankhula.
14
Pakuti tikudziŵa kuti Mulungu amene adaukitsa Ambuye Yesu kwa akufa, adzatiwukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatifikitsa pamodzi nanu pamaso pake.
15
Cholinga cha zonsezi nchakuti inu mupindule, ndipo kuti monga momwe anthu olandira madalitso a Mulungu akunka nachulukirachulukira, momwemonso othokoza Mulungu achulukirechulukire ndi kumchitira ulemu.
16
Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku.
17
Masautso athu ndi opepuka, a nthaŵi yochepa, komabe akutitengera ulemerero umene uli waukulu kopambana, ndiponso wamuyaya.
18
Mitima yathu siili pa zinthu zooneka, koma pa zinthu zosaoneka. Paja zooneka nzosakhalitsa, koma zosaoneka ndiye zamuyaya.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13