bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Corinthians 2
2 Corinthians 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 3 →
1
Nchifukwa chake ndidatsimikiza kuti ndisachite ulendo winanso wopweteka wobwera kwanuko.
2
Ngati ndine amene ndikukupweteketsani mtima, nanga ineyo adzandisangalatsa ndani, kodi si yemweyo amene ndidampweteketsa mtima.
3
Nchifukwa chake ndidakulemberani kalata ija. Sindidafune kudza kwanuko, kuwopa kuti inuyo oyenera kundisangalatsanu mungandipweteketse mtima. Ndidaadziŵiratu kuti ine ndikamakondwa, nonsenunso mumakondwa.
4
Pamene ndidakulemberani kalata ija, mtima wanga unali wovutika ndi wopsinjika ndithu, ndipo ndinkalira misozi. Sindidafune kukupweteketsani mtima, koma makamaka ndinkafuna kuti mudziŵe kuti ndimakukondani kwambiri.
5
Ngati wina aliyense adachita kanthu kolasa mtima, si ineyo amene adalasa mtima, koma pang'ono ponse adalasako nonsenu, kunenatu mosakulitsa nkhani.
6
Munthu woteroyo, pafupi nonse mwamtsutsa, choncho chilangocho nchokwanira.
7
Tsono makamaka nkwabwino mumkhululukire ndi kumlimbitsa mtima, kuwopa kuti angamve chisoni chachikulu chomtayitsa mtima kotheratu.
8
Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mumtsimikizirenso kuti mumamkonda ndithu.
9
Pamene ndinkakulemberani kalata ija, cholinga changa chinali chakuti ndikuyeseni, ndi kuwona ngati mudzandimvera pa zonse.
10
Mukakhululukira munthu, inenso ndimkhululukira. Ngati ine ndakhululukira, patakhala kanthu koti ndakhululukira, ndiye kuti ndakhululukira chifukwa cha inu pamaso pa Khristu.
11
Cholinga chake nkuti Satana asatichenjerere, paja tikudziŵa njira zake.
12
Pamene ndidafika ku Troasi kuti ndikalalike Uthenga Wabwino wonena za Khristu, ndidapeza Ambuye atanditsekulira kale pa khomo kuti ndikagwire ntchito kumeneko.
13
Komabe mumtima mwanga munalibe mtendere, chifukwa sindidampeze Tito, mbale wanga. Tsono ndidatsazikana ndi anthu akumeneko nkupita ku Masedoniya.
14
Tithokoze Mulungu amene mwa Khristu amatitsogolera nthaŵi zonse m'kupambana kwake. Kudzera mwa ife Mulungu akupatsa anthu onse nzeru zodziŵira Khristu, ndipo nzeruzo zikuwanda ponseponse ngati fungo labwino.
15
Zoonadi tili ngati fungo labwino la Khristu lokomera Mulungu, pakati pa anthu amene akupulumuka ndi amene akutayika.
16
Kwa amene akutayika, fungoli ndi la imfa, ndipo limaŵapha. Koma kwa amene akupulumuka, fungoli ndi la moyo, ndipo limaŵapatsa moyo. Nanga ndani angaithe ntchito yotere?
17
Ifetu sitili ngati anthu ena ambiri amene amangochita malonda ndi mau a Mulungu. Koma, popeza kuti tili mwa Khristu, ngati anthu otumidwa ndi Mulungu, timalankhula moona, molingana ndi kufuna kwake.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13