bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Corinthians 12
2 Corinthians 12
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 13 →
1
Ndiyenera kunyada, tsono kunyada kwake nkopanda phindu. Komabe ndimati ndikambe za zimene Ambuye adandiwonetsa m'masomphenya, ndiponso za zimene adandiwululira.
2
Ndikudziŵa mkhristu wina amene adaatengedwa mwadzidzidzi kupita Kumwambamwamba. Papita zaka khumi ndi zinai chichitikire cha zimenezi. Sindidziŵa ngati zidaachitika ali m'thupi kapena ali kunja kwa thupi. Akudziŵa ndi Mulungu zimenezi.
3
Ndikudziŵa kuti munthuyo adaatengedwa mwadzidzidzi kupita ku Paradizo. Sindikudziŵa ngati zimenezi zidaachitika ali m'thupi, kapena ali kunja kwa thupi. Akudziŵa ndi Mulungu zimenezi.
4
Kumeneko munthuyo adamva zinthu zosasimbika, zinthu zimene munthu sangazilankhule.
5
Munthu wotere ndidzamnyadira, koma kunena za ine ndekha, sindidzanyadira kanthu kena koma kufooka kwanga kokha.
6
Ndikadafuna kunyada, sindikadakhala ngati wopusa, chifukwa ndikadalankhula zoona zokha. Koma sindidzanyada, kuwopa kuti wina aliyense angandiyese wopambana, kusiyana ndi m'mene amandiwonera, ndiponso ndi m'mene amandimvera ndikamalankhula.
7
Koma kuwopa kuti ndingamadzitukumule chifukwa cha zazikulu kwambiri zimene Ambuye adandiwululira, Mulungu adandipatsa cholasa ngati minga m'thupi. Adalola wamthenga wa Satana kuti azindimenya, kuti ndingamanyade kwambiri.
8
Pamenepo ndidapempha Ambuye katatu kuti andichotsere chimenechi,
9
koma Iwo adandiwuza kuti, “Chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine.
10
Tsono ndimakondwera pamene ndili wofooka, pamene anthu andinyoza, namandizunza, ndiponso pamene ndimva zoŵaŵa ndi kusautsidwa chifukwa cha Khristu. Pakuti pamene ndili wofooka, mpamene ndili ndi mphamvu.
11
Ndasanduka wopusa, koma ndinu mwandichititsa zimenezi. Ndinu mukadayenera kundichitira umboni. Pakuti ngakhale sindili kanthu, atumwi anu apamwamba aja sandipambana pa kanthu kalikonse.
12
Ndidakutsimikizirani mopirira kwambiri kuti ndine mtumwi, pakuchita pakati panu zizindikiro, zozizwitsa ndi ntchito zina zamphamvu.
13
Kodi nchiyani chimene ndidachitira mipingo ina, inu osakuchitirani, kupatula chokhachi chakuti sindidakhale ngati katundu wokulemetsani? Ndikhululukireni kulakwa kwangaku.
14
Aka nkachitatu tsopano kukonzeka kuti ndibwere kwanuko, ndipo sindidzakhala ngati katundu wokulemetsani. Sindikufuna zinthu zanu, koma ndikufuna inuyo. Pakuti si udindo wa ana kusungira makolo ao chuma, koma ndi udindo wa makolo kusungira ana ao chuma.
15
Kunena za ine, ndidzakondwa kupereka zanga zonse, ndi kutaya ngakhale moyo wanga womwe chifukwa cha inu. Ine ndikamakukondani kwambiri chotere, kodi ndiye kuti inuyo muzingondikonda pang'ono?
16
Momwemo tsono, mudzandivomereza kuti ine sindidakhale ngati katundu wokulemetsani. Koma kapena wina adzati popeza kuti ndine wochenjera, ndidakuchenjeretsani.
17
Kodi kapena ndidakuchenjererani mwa aliyense amene ndidamtuma kwa inu?
18
Ndidapempha Tito kuti apite, kenaka ndidatuma mbale wathu wina pamodzi naye. Kodi Titoyo adakuchenjererani? Kodi suja iye ndi ine tinkachita zonse ndi mtima umodzi? Suja tinkatsata njira imodzimodzi?
19
Kapena mwakhala mukuganiza kuti tikuyesa kudziteteza pamaso panu. Iyai, koma pokhala pamaso pa Mulungu, timalankhula mwa Khristu, ndipo pa zonsezi, okondedwa anga, timangofuna kukulimbitsani mtima.
20
Ndikuwopa kuti ndikadzabwera kwanuko, mwina nkudzakupezani muli osiyana ndi m'mene ndikadafunira. Ndikuwopa kuti mwina inunso nkudzandipeza ine wosiyana ndi m'mene mukadafunira. Ndikuwopanso kuti mwina ine nkudzapeza kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusinjirirana, ugogodi, kudzitukumula, ndiponso chisokonezo.
21
Ndikuwopa kuti ndikadzabweranso kwanuko, mwina Mulungu wanga nkudzandinyazitsa pamaso panu, ineyo nkudzalira misozi chifukwa cha ambiri amene adachimwa kale, ndipo sadalape zonyansa zao, dama lao, ndi mayendedwe ao oipa.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13