bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Corinthians 8
2 Corinthians 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 9 →
1
Abale, tifuna kuti mudziŵe za m'mene Mulungu adadalitsira mipingo ya ku Masedoniya.
2
Anthu a m'mipingoyo adayesedwa kwambiri ndi masautso, komabe adakondwa kwakukulu, kotero kuti adapereka moolowa manja kwenikweni, ngakhale anali amphaŵi.
3
Ine ndikuŵachitira umboni kuti adapereka monga adathera, ngakhalenso mopitirira pamenepo poyerekeza ndi chuma chao.
4
Popanda wina aliyense woŵakakamiza adatipempha, natiwumiriza kuti tiŵapatse mwai woti nawonso athandize anthu a Mulungu a ku Yudeya.
5
Ndipo adathandizadi mopitirira pa zimene tidaayembekeza, pakuti poyamba adadzipereka kwa Ambuye, kenaka mwa kufuna kwa Ambuye adadziperekanso kwa ife.
6
Nchifukwa chake tidaapempha Tito kuti akatsirizenso pakati panu ntchitoyi yakusonkhanitsa zopereka zachifundo imene iye anali atayamba kale.
7
Zonse mudalandira pakulu, monga kukhulupirira, kulankhula, kudziŵa zinthu, kuchita changu pa zonse, ndiponso kutikonda. Motero tifuna kuti muperekenso pakulu zachifundozi.
8
Pamene ndikunena zimenezi, sindikuchita kulamula ai. Pakukufotokozerani za changu cha ena, ndingofuna kuwona ngati chikondi chanu ndi chikondi chenicheni.
9
Mukudziŵa kukoma mtima kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Ngakhale anali wolemera, adakhala mmphaŵi chifukwa cha inu, kuti ndi umphaŵi wakewo inu mukhale olemera.
10
Pa nkhani imeneyi maganizo anga ndi akuti nkwabwino kuti mutsirize zimene mudayamba kale chaka chathachi, osati kungofuna kuzichita, komanso kuzichita kumene.
11
Tiyeni tsono muzitsirize. Paja munali ndi changu pofuna kuzichita, muchitenso changu tsopano kuzitsiriza molingana ndi zimene muli nazo.
12
Malinga munthu akakhala ndi changu cha kupereka, Mulungu amalandira mokondwa zimene munthuyo ali nazo, ndipo samkakamiza kuti apereke zimene alibe.
13
Sindikufuna kunena kuti inuyo muvutike, ena apepukidwe, ai, koma kuti pakhale kulingana.
14
Poti inu muli ndi zambiri tsopano, muyenera kumathandiza osoŵa, kuti m'tsogolomo nawonso akadzakhala ndi zochuluka, azidzakuthandizani pa zosoŵa zanu. Motero padzakhala kulingana.
15
Paja Malembo akuti, “Amene adapata zambiri, sizidamchulukire, amene adapata pang'ono, sizidamchepere.”
16
Tiyamike Mulungu kuti adaika mumtima mwa Tito changu chomwecho chimene ife tili nacho pokuthandizani.
17
Pakuti sadangochita zimene tidampempha, koma changu chake chinali chachikulu, kotero kuti adatsimikiza yekha zobwera kwanuko.
18
Pamodzi ndi iyeyo tikutuma mbale wathu uja, amene mipingo yonse ikumuyamika chifukwa cha ntchito yake yolalika Uthenga Wabwino.
19
Ndipo si pokhapo ai, komanso mipingo idamsankha kuti adzatiperekeze pokapereka zopereka zachifundozi. Tikukonza zimenezi kuti tichitire Ambuye ulemu, ndiponso kuti tiwonetse mtima wathu wofuna kuthandiza.
20
Sitikufuna kupatsa anthu chifukwa choti azitinenera zoipa pa mayendetsedwe athu a zopereka zachifundo zochulukazi.
21
Ifetu tikufuna kuchita zabwino, osati pamaso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu.
22
Pamodzi ndi iwowo tikutuma mbale wathu wina. Takhala tikumuyesa kaŵirikaŵiri, ndipo tampeza kuti ndi wachangu ndithu pa zinthu zambiri. Tsopano akufunitsitsa koposa kuti athandize, popeza kuti amakukhulupirirani kwambiri.
23
Kunena za Tito, iyeyu ndi wantchito mnzanga amene amagwirizana nane pokuthandizani. Kunenanso za abale athu enawo, ngotumidwa ndi mipingo, ndipo Khristu amalemekezedwa chifukwa cha iwo.
24
Tsono muŵatsimikizire chikondi chanu, kuti mipingo yonse ichiwone, ndi kudziŵa kuti sitikulakwa tikamakunyadirani.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13