bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Corinthians 13
2 Corinthians 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
1
Aka nkachitatu tsopano kuti ndibwere kwanuko. Mau a Mulungu akuti, “Mlandu uliwonse uzitsimikizika ndi umboni wa anthu aŵiri kapena atatu.”
2
Inu amene mudaachimwa kale, ndiponso ena onse, paja ndidaakuuzani pamene ndinali kwanuko kachiŵiri kaja ndipo ndikubwereza kukuuziranitu tsopano ndisanafike, kuti ndikadzabweranso, sindidzamchitira chifundo wina aliyense.
3
Pamenepo mudzaona chitsimikizo chimene mukufuna chakuti Khristu amalankhula kudzera mwa ine. Iyeyu sali wofooka pa zimene amachita nanu, koma amaonetsa mphamvu zake pakati panu.
4
Anali wofooka pamene adapachikidwa pa mtanda, komabe tsopano ali moyo mwa mphamvu ya Mulungu. Ifenso ndife ofooka mwa Iye, koma tidzakhala amoyo pamodzi naye ndi mphamvu ya Mulungu, pogwira ntchito yathu pakati panu.
5
Muzidziyesa nokha inuyo kuti mutsimikize ngati mukusungadi chikhulupiriro chanu. Muzidzifunsitsa nokha. Simudziŵa nanga kuti Yesu Khristu ali mwa inu? Ngati si choncho, mwalephereratu.
6
Koma ndikhulupirira kuti mudzazindikira kuti ife sitidalephere.
7
Tikupempha Mulungu kuti musachite choipa chilichonse. Osati kuti ife tiwoneke ngati opambana, koma kuti inu muchite zimene zili zoyenera, ngakhale ife tiwoneke ngati talephera.
8
Pakuti sitingathe kuchita chilichonse chotsutsana ndi choona, koma zokhazokha zothandizira choonacho.
9
Timakondwa pamene ife tili ofooka koma inu muli amphamvu. Chimene tikupempha Mulungu nchakuti mudzasanduke angwiro.
10
Ndikulemba zimenezi ndisanafike kwanu, kuti ndikadzafika, pasadzakhale chifukwa choti ndidzagwiritse ntchito ulamuliro wanga mwaukali. Ambuye adandipatsa ulamulirowo kuti ndilimbitse mpingo, osati kuti ndiupasule.
11
Tsono abale, kondwani. Mverani zimene ndikukulangizani, ndipo mukonze zimene zidalakwika. Muzimvana ndi kukhala mu mtendere. Pamenepo Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu.
12
Mupatsane moni mwa chikondi choona.
13
Anthu onse a Mulungu akukupatsani moni.
14
Madalitso a Ambuye Yesu Khristu ndi chikondi cha Mulungu ndiponso chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13