bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Corinthians 10
2 Corinthians 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 11 →
1
M'dzina la Yesu Khristu wa mtima woleza ndi wofatsa, ine Paulo mwiniwake, amene anthu ena amati ndine wamantha pamene ndili pamaso panu, koma wosaopa konse pamene ndili nanu kutali, ndikuti mundimve.
2
Ndikukupemphani kuti ndikadzafika kwanuko ndisadzakakamizidwe kudzudzula mosaopa konse anthu amene akuti machitidwe athu ndi otsata za anthu chabe.
3
Ndi zoona kuti ndife anthu, koma sitimenya nkhondo motsata za anthu chabe.
4
Pakuti zida zathu zakhondo si za anthu chabe, koma ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu zotha kuwononga malinga. Timagonjetsa maganizo onyenga,
5
ndiponso kudzikuza kulikonse koletsa anthu kudziŵa Mulungu. Timagonjetsa ganizo lililonse kuti limvere Khristu.
6
Ndipo inu mutakhala omvera kwenikweni, tili okonzeka kulanga aliyense amene samvera.
7
Ganizani bwino pa zimene mukuwona ndi maso anu. Kodi pali wina amene amakhulupirira kuti ndi wake wa Khristu? Chabwino, koma akumbukire kuti monga iye ali wake wa Khristu, ifenso ndife ake a Khristu.
8
Ndipotu ngakhale mwina ndikunyadira mokakata ulamuliro umene Ambuye adatipatsa woti tikulimbitse nawoni, osati kukuwonongani ai, ndithu sindidzachita manyazi.
9
Tsono musayese kuti ndikungokuwopsezani ndi makalata anga.
10
Paja ena amati, “Makalata a Paulo ngaukali ndi amphamvu, koma mwiniwake akakhala pakati pathu, iyeyo ngwofooka ndipo mau ake ndi achabe.”
11
Anthu oganiza zotere, adziŵe kuti palibe kusiyana pakati pa zimene timanena m'makalata pamene tili nanu kutali ndi zimene timachita tikakhala nanu pamodzi.
12
Sikuti timayesa kudzilinga kapena kudziyerekeza ndi ena amene amadzichitira okha umboni. Amapusa chabe pakungodziyesa ndi muyeso waowao, ndi kudzilinganiza ndi anzao a m'gulu lao lomwe.
13
Kunena za ife, sitinganyade mopitirira malire. Tidzasamala malire omwe Mulungu adatiikira potifikitsa mpaka kwa inu.
14
Sitidabzole malire athu, monga ngati sitidakafike kwanu. Tinali oyamba ndife kukafika kwanu ndi kulalika Uthenga Wabwino wonena za Khristu.
15
Motero sitinyadira ntchito zimene anthu ena adazigwira m'dera limene Mulungu adatiikira ife. Kwenikweni tikuyembekeza kuti chikhulupiriro chanu chidzakula, ndipo kuti ntchito yathunso pakati panu idzakula, koma osabzola malire a dera lathu.
16
Pambuyo pake tingathe kukubzolani nkukalalika Uthenga Wabwino ku maiko enanso, osanyadira ntchito imene munthu wina wachita kale m'dera lake.
17
Paja Malembo akuti, “Wofuna kunyada, anyadire Ambuye.”
18
Pakuti munthu wovomerezeka, si amene amadzichitira yekha umboni, koma amene Ambuye amamchitira umboni.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13