bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Zechariah 10
Zechariah 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 11 →
1
Pemphani Chauta kuti akupatseni mvula pa nyengo yobzala. Ndiye amene amapanga mitambo yamvula. Ndiye amene amagwetsera anthu mvula yamvumbi, ndiye amene amameretsera aliyense mbeu m'munda.
2
Paja mafano am'nyumba amalankhula zonama, ndipo oombeza maula amaona zabodza. Olota maloto amalota zabodza, ndipo mau ao othuzitsa mtima ndi nkhambakamwa chabe. Motero anthu amangoyenda uku ndi uku ngati nkhosa, amazunzika chifukwa chosoŵa mbusa.
3
Chauta akuti, “Ndaŵakwiyira kwambiri abusa, ndipo atsogoleri a m'dzikomo ndidzaŵalanga. Koma Ine Chauta Wamphamvuzonse ndidzasamala nkhosa zanga, ndiye kuti banja la Yuda, ndipo ndidzazisandutsa ngati akavalo ankhondo amphamvu.
4
Mwa iwo mudzatuluka mtsogoleri amene adzakhala ngati mwala wapangodya, ngati uta wankhondo. Ndipo atsogoleri onse olamulira adzachokeranso mwa iyeyo.
5
Ayuda onse pamodzi adzakhala ngati ngwazi zankhondo, zopondereza adani m'matope am'miseu nthaŵi yankhondo. Adzamenya nkhondo chifukwa choti Chauta ali nawo, ndipo adzagonjetsa adani okwera pa akavalo.
6
“Banja la Yuda ndidzalilimbitsa, banja la Yosefe ndidzalipambanitsa. Anthuwo ndidzaŵabwezanso kwao chifukwa choti ndaŵamvera chifundo. Tsono adzakhala ngati kuti sindidaŵataye, pakuti Ine ndine Chauta, Mulungu wao, ndipo ndidzayankha zopempha zao.
7
Pamenepo Aefuremu adzakhala ngati ankhondo amphamvu, adzasangalala ngati anthu okhuta vinyo. Ana ao adzaziwona zimenezi, nawonso nkusangalala, mumtima mwao mudzadzaza chimwemwe, chifukwa cha zimene Chauta wachita.
8
“Ndidzaliza mluzu kuti anthu anga asonkhane pamodzi. Ndidaŵapulumutsa, ndipo adzachuluka monga momwe adaaliri masiku amakedzana.
9
Ngakhale ndidaŵabalalitsira pakati pa mitundu ya anthu, komabe ku maiko akutaliwo adzandikumbukira. Iwowo pamodzi ndi ana ao adzakhala moyo nadzabwerera.
10
Ndidzaŵatulutsa ku Ejipito ndi kupita nawo kwao, ndipo ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera ku Asiriya. Ndidzaŵafikitsa ku dziko la Giliyadi ndi la Lebanoni mpaka kudzaza dziko lonse.
11
Pamene azidzaoloka nyanja ya ku Ejipito, ndidzathetsa mafunde a pa nyanjayo, madzi onse a mtsinje wa Nailo adzaphweratu. Kudzikuza kwa Asiriya kudzatha, ndipo ndodo yaufumu ya Ejipito idzathyoka.
12
Ineyo ndidzalimbitsa anthu anga, ndipo adzakhala onyadira dzina la Chauta.” Ndikutero Ine Chauta.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14