bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Zechariah 7
Zechariah 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 8 →
1
Pa chaka chachinai cha ufumu wa Dariusi, tsiku lachinai la Kisilevi, mwezi wachisanu ndi chinai, Chauta adapatsa Zekariya uthenga.
2
Anthu a ku Betele anali atatuma Sarezere ndi Regemumeleki ndi anthu ao, kuti akapemphe chifundo kwa Chauta.
3
Kwinanso adaati akafunse ansembe a ku Nyumba ya Chauta Wamphamvuzonse ndiponso aneneri kuti, “Kodi ifeyo tizilira ndi kusala chakudya pa mwezi wachisanu monga m'mene takhala tikuchitira pa zaka zambiri?”
4
Tsono Chauta Wamphamvuzonse adandipatsa uthenga uwu wakuti:
5
“Funsa anthu onse a m'dziko ndi ansembe kuti, ‘Pamene munkasala zakudya ndi kulira pa mwezi wachisanu ndi pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri zaka makumi asanu ndi aŵiri zapitazi, kodi munkalemekezadi Ine pochita zimenezo?
6
Kodi pamene munkadya ndi kumwa, suja munkangodzikondweretsa nokha?
7
Pajatu nzimenezi zija ankanena Chautazi kudzera mwa aneneri akale, pamene munali modzaza ndi anthu ndiponso zinthu zinkapita m'tsogolo mu mzinda wa Yerusalemu ndi m'mizinda yake yozungulira, ku madera a kumwera ndi ku chigwa.’ ”
8
Chauta adapatsa Zekariya uthenga uwu wakuti,
9
“Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Muziweruzana molungama. Muzimverana chisoni ndi kuchitirana chifundo.
10
Musamazunze akazi amasiye ndi ana amasiye, alendo ndiponso amphaŵi. Musamaganizirane zachiwembu m'mitima mwanu.
11
“Koma iwowo adakana kumvera, adandifulatira ndi mtima wokanika. Adatseka makutu ao kuti asamve.
12
Mitima yao adaiwumitsa kwambiri, kuti asamve malamulo ndi mau amene Ine Chauta Wamphamvuzonse ndidaŵaphunzitsa ndi Mzimu wanga kudzera mwa aneneri amakedzana. Nchifukwa chake Ine Chauta Wamphamvuzonse ndidaŵakwiyira kwambiri.
13
Poti sadandimvere nditaŵaitana, Inenso sindidaŵamvere atandiitana. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.
14
Monga momwe amachitira kamvulumvulu, ndidaŵamwaza pakati pa mitundu ina ya anthu imene iwo sankaidziŵa, ndipo dziko lao lidasanduka chipululu, kotero kuti palibenso wina amene ankayendamo. Choncho dziko lao lokomalo lidasandukadi chipululu.”
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14