bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Zechariah 4
Zechariah 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 5 →
1
Pambuyo pake mngelo amene ankalankhula nane uja adabweranso nandidzutsa monga momwe amadzutsira munthu amene ali m'tulo.
2
Adandifunsa kuti, “Ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Ndikuwona choikaponyale, chonse chagolide, ndi mbale pamwamba pake. Chili ndi nyale zisanu ndi ziŵiri, iliyonse ili ndi ziboo zisanu ndi ziŵiri zoloŵetsamo zingwe zoyatsira.
3
Pambali pake pa choikaponyalecho pali mitengo iŵiri ya olivi, wina ku dzanja lamanja, wina ku dzanja lamanzere.”
4
Ndiye mngelo amene anali naneyo ndidamufunsa kuti “Mbuye wanga, kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?”
5
Mngeloyo adayankha kuti, “Monga iwe zimenezi sukuzidziŵa?” Ine ndidati, “Inde, mbuye wanga, sindikuzidziŵa.”
6
Tsono iye adandiwuza kuti ndidziŵitse Zerubabele uthenga wa Chauta wakuti, “Inde udzapambana, koma osati ndi nkhondo kapena ndi mphamvu, koma ndi mzimu wanga.
7
Kodi iwe phiri lalitali, ndiwenso chiyani? Udzasanduka dziko losalala pamaso pa Zerubabele. Ndipo akadzabwera nawo mwala wotsiriza wa pa Nyumba yanga, namauika pamwamba, anthu adzafuula kuti, ‘Ati kukongola ati!’ ”
8
Chauta adandipatsanso uthenga uwu wakuti,
9
“Zerubabele adamanga maziko a nyumba imeneyi ndi manja ake, adzaitsiriza ndi manja ake omwewo. Motero anthu adzadziŵa kuti Chauta Wamphamvuzonse adandituma kwa iwo.
10
Pakali pano anthuwo ndi okhumudwa kuwona kuti ntchito sikufulumira. Koma akadzamuwona Zerubabele atatenga mwala wotsiriza uja m'manja mwake, pamenepo adzakondwa. “Nyale zisanu ndi ziŵiri ndi maso a Chauta amene akunka nayang'anayang'ana pa dziko lonse lapansi.”
11
Tsono ndidamufunsa munthuyo kuti, “Nanga mitengo iŵiri ya olivi ili kumanja ndi kumanzere kwa choikaponyalecho ikutanthauza chiyani?”
12
Ndidamufunsanso kuti, “Pambali pa mipopi iŵiri yagolide yodzera mafutayo pali nthambi ziŵiri za mtengo wa olivi, zimenezi zikutanthauza chiyani?”
13
Iye adati, “Monga iwe zimenezi sukuzidziŵa?” Ine ndidayankha kuti, “Inde, mbuye wanga, sindikuzidziŵa.”
14
Tsono iye adati, “Ameneŵa ndi anthu aŵiri odzozedwa aja, amene amatumikira Chauta, Ambuye a dziko lonse lapansi.”
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14