bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Zechariah 13
Zechariah 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 14 →
1
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsiku limenelo banja la Davide adzalikonzera kasupe wa madzi, kuti iwo pamodzi ndi anthu a ku Yerusalemu aŵachotsere machimo ao ndi zoipa zao.
2
“Tsiku limenelo ndidzafafaniziratu ndi maina omwe a mafano m'dziko, kotero kuti sadzaŵakumbukiranso. Ndidzachotsanso m'dziko aneneri pamodzi ndi mzimu wonyansa Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.
3
Wina aliyense akadzafunabe kuti azilosa, bambo wake ndi mai wake adzamuuza kuti, ‘Sudzakhalanso ndi moyo chifukwa choti ukulosa zabodza m'dzina la Chauta.’ Motero makolo ake omwe adzambaya pamene munthuyo akulosa.
4
“Tsiku limenelo mneneri aliyense adzachita manyazi chifukwa cha zinthu zimene akuti amaziwona m'masomphenya pamene akulosa. Sadzavalanso mwinjiro wake waubweya woti azinamizira anthu.
5
Koma adzati, ‘Sindine mneneri ai. Ndine mlimi, poti ndakhala ndikulima munda kuyambira ubwana wanga.’
6
Ndipo wina akadzafunsa kuti, ‘Nanga zilonda zili kumsana kwakozi, udatani?’ Iye adzati, ‘Zilondazi ndidazilandira m'nyumba mwa abwenzi anga.’ ”
7
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Lupanga iwe, dzambatuka, ukanthe mbusa wanga. Ukanthe munthu amene ali pafupi ndi Ine. Ndikutero Chauta Wamphamvuzonse. Kantha mbusa kuti nkhosa zimwazikane. Pamenepo ndidzakantha ndi anthu wamba omwe.”
8
Chauta Wamphamvuzonse akuti, “Mwa zigawo zitatu za anthu m'dziko monsemo ziŵiri zidzaphedwa, chidzangokhalako chigawo chimodzi chokha chamoyo.
9
Anthu a m'chigawo chachitatuchi ndidzaŵaika pa moto, ndidzaŵayeretsa monga m'mene amayeretsera siliva. Ndidzaŵayesa monga m'mene amayesera golide. Tsono adzatama dzina langa mopemba, Ine mwiniwake nkuŵayankha. Ndidzanena kuti, ‘Ameneŵa ndi anthu anga.’ Iwowo adzati, ‘Chauta ndi Mulungu wathu.’ ”
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14