bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Zechariah 5
Zechariah 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 6 →
1
Ndidaonanso zinthu zina m'masomphenya: ndidaona chikalata chofutukula chikuuluka.
2
Mngelo uja adandifunsa kuti “Kodi ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Chikalata chofutukula chikuuluka, muutali mwake mamita asanu ndi anai, muufupi mwake mamita anai ndi hafu.”
3
Tsono adandiwuza kuti, “Pamenepo palembedwa temberero limene lidzagwera dziko lonse lapansi. Aliyense wakuba adzachotsedwa m'dziko potsata zimene zalembedwa mbali iyi, ndipo aliyense wolumbira zabodza nayenso adzachotsedwa potsata zimene zalembedwa mbali inai.
4
Chauta Wamphamvuzonse wanena kuti, ‘Temberero limeneli ndidzalitumiza m'nyumba ya munthu wakuba ndi m'nyumba ya munthu wolumbira zabodza potchula dzina langa. Lidzakhala m'nyumbamo mpaka kuiwonongeratu, mitengo yake ndi miyala yake yomwe.’ ”
5
Pambuyo pake mngelo amene ankalankhula nane uja adabwera, nandiwuza kuti, “Upenyetsetse, uwone chinthu chikubwerachi.”
6
Ndidafunsa kuti, “Kodi nchiyani?” Iye adati, “Chimenechi ndi gondolo loyesera, ndipo likutanthauza uchimo wa anthu m'dziko lonse.”
7
Chovundikira chake chinali chamtovu, ndipo chitatukuka, ndidaona mkazi atakhala tsonga m'gondolomo.
8
Mngeloyo adati, “Ameneyu akutanthauza kuipa konse.” Atatero adakankhira mkaziyo m'gondolo muja, nabwezera chovundikira chamtovu chija pamwamba pake.
9
Nditayang'ananso, ndidaona akazi aŵiri okhala ndi mapiko onga a kakoŵa. Akaziwo ankabwera chouluka ndi mphepo. Adanyamula gondolo lija, kupita nalo pakati pa dziko lapansi ndi mlengalenga.
10
Tsono ndidafunsa mngelo amene ankalankhula nane kuti, “Nanganso gondololi akupita nalo kuti?” Iye adandiyankha kuti,
11
“Akupita nalo ku dziko la Sinara kuti akalimangire nyumba. Nyumbayo ikadzatha, adzakhazikamo gondololo pa phaka lake.”
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14