bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Zechariah 11
Zechariah 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 12 →
1
Tsekula zitseko zako, iwe Lebanoni, kuti moto upsereze mikungudza yako.
2
Lirani mokweza, inu mitengo ya paini, pakuti mikungudza yagwa, mitengo yamphamvu yaonongeka. Lirani mokweza inu mitengo ya thundu ya ku Basani, pakuti nkhalango yoŵirira ija aiyeretsa.
3
Imvani abusa, nawonso akulira mokweza, pakuti mabusa ao obiriŵira auma. Imvani misona ya mikango ikubangula, pakuti nkhalango yoŵirira ya ku Yordani aiyeretsa.
4
Chauta, Mulungu wanga, adandiwuza kuti, “Ŵeta bwino nkhosa zimene zili kukaphedwa.
5
Amene amagula nkhosa amazipha, koma salangidwa. Amene amazigulitsa amanena kuti, ‘Atamandike Chauta, ine ndalemera!’ Ndipo abusa ake sadzazimvera chifundo nkhosazo.
6
Choncho onse okhala m'dziko lapansi, sindidzaŵamveranso chifundo. Ndikutero Ine Chauta. Munthu aliyense ndidzampereka m'manja mwa mtsogoleri wake ndi mwa mfumu yake. Ndipo iwowo adzasakaza dziko lonse, koma Ine sindidzampulumutsa aliyense m'manja mwao.”
7
Tsono ine ndidayamba kuŵeta nkhosa zokaphedwa zija. Ndidatenga ndodo ziŵiri: yoyamba ndidaitcha dzina lakuti “Kukoma mtima”, yachiŵiri ndidaitcha “Umodzi.” Tsono gulu la nkhosa lija ndidaliŵetadi bwino.
8
Pa mwezi umodzi ndidachotsa abusa atatu aja. Adafika pondipsetsa mtima, ine osathanso kuŵapirira. Iwonso adadana nane.
9
Tsono ndidauza gulu la nkhosa lija kuti, “Sindidzakuŵetaninso. Imene ikuti ife, ife basi. Imene ikuti isokere, isokere, ndipo otsalanu, muzidyana.”
10
Pambuyo pake ndidatenga ndodo yanga ija yotchedwa “Kukoma mtima” ndi kuithyola, kusonyeza kuphwanya chipangano chimene ndidaapangana ndi mitundu yonse ya anthu.
11
Motero chipanganocho chidatha tsiku limenelo, ndipo ochita malonda a nkhosa aja, amene ankangondiyang'anitsitsa, adazindikira kuti zonse zimene ndinkachita zinali zochokera kwa Chauta.
12
Tsono eni nkhosawo ndidaŵauza kuti “Ngati zakukomerani, mundilipire. Koma ngati si choncho, sungani ndalama zanu.” Ndiye iwowo adandilipira masekeli asiliva makumi atatu.
13
Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Uziponye mosungira chuma.” Motero ndidatenga masekeli asiliva zija, mtengo uja adaati ndiyenera kulandirawu, nkukaziponya mosungira chuma m'Nyumba ya Chauta.
14
Kenaka ndidathyolanso ndodo ina ija yotchedwa “Umodzi,” kusonyeza kuthetsa ubale pakati pa Yuda ndi Israele.
15
Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Tenganso zida za mbusa, mbusa wake wopandapake.
16
Pakuti ndidzakuika mbusa m'dziko, mbusa amene sadzasamala nkhosa zotayika, sadzanka nafunafuna zosokera, kapena kuchiritsa zopunduka, ndi kudyetsa zamoyo. Koma iye azidzangodya nyama ya nkhosa zonona, mpaka kumapulula ndi ziboda zake zomwe.
17
“Tsoka kwa mbusa wanga wopandapakeyo, amene amasiya nkhosa! Amkanthe ndi lupanga pa mkono, ndi pa diso lake lakumanja. Mkono wakewo ufwape, ndipo diso lakelo lichite khungu kotheratu!”
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14