bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Zechariah 2
Zechariah 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 3 →
1
Ndidaonanso zinthu m'masomphenya: ndidaona munthu atatenga chingwe choyesera m'manja mwake.
2
Ndidamufunsa kuti, “Kodi mukupita kuti?” Iye adandiyankha kuti, “Ndikukayesa mzinda wa Yerusalemu kuti ndidziŵe kutalika kwa muufupi mwake ndi m'litali mwake.”
3
Apo mngelo uja ankalankhula naneyu adasendera, mngelo winanso adadzakumana naye.
4
Woyamba uja adauza mnzakeyo kuti, “Thamangira mnyamata wachingweyo, ukamuuze kuti mu Yerusalemu mudzakhala anthu ambiri ndiponso zoŵeta zochuluka, kotero kuti mzindawo udzakhala wopanda malinga.
5
Chauta akuti Iye yemwe ndiye adzakhale linga lamoto loteteza mzindawo, ndipo adzaonetsa ulemerero wake m'kati mwake.”
6
Chauta akunena kuti, “Tiyeni, tiyeni, thaŵaniko ku dziko lakumpoto. Paja ndidakumwazirani ku mphepo zinai za mlengalenga.
7
Tiyeni, thaŵirani ku Ziyoni, inu amene mudatengedwa ukapolo kupita ku Babiloni.
8
Aliyense wokantha inu, wakantha chinthu cha mtengo wapatali zedi kwa Ine.” Tsono Chauta Wamphamvuzonse adandituma kwa mitundu imene idaagwira anthu ake kukaiwuza uthenga wake wakuti,
9
“Ine Chauta ndidzaŵamenya anthuwo ndi dzanja langa, ndipo amene anali akapolo ao, ndiwo amene adzaŵalande chuma chao.” Pamenepo mudzadziŵa kuti Chauta Wamphamvuzonse ndiye wandituma.
10
“Inu anthu a ku Ziyoni, imbani mokondwa, chifukwa ndikubwera, ndikudzakhala pakati panu,” akutero Chauta.
11
Nthaŵi imeneyo anthu a mitundu yambiri adzabwera kwa Chauta, adzasanduka anthu ake, ndipo Iye adzakhala pakati panu. Apo mudzadziŵa kuti Chauta Wamphamvuzonse ndiye wandituma kwa inu.
12
Iyeyo adzamtenganso Yuda kuti akhale chuma chake m'dziko lopatulika, ndipo Yerusalemu adzakhala mzinda wake wapamtima.
13
Anthu nonsenu, ingokhalani chete pamaso pa Chauta, chifukwa wadzambatuka ndi kutuluka ku malo ake oyera.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14