bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Zechariah 3
Zechariah 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 4 →
1
Tsono m'masomphenya Chauta adandiwonetsa Yoswa, mkulu wa ansembe, ataima pamaso pa mngelo wake, ku dzanja lake lamanja kutaima Satana woti amuimbe mlandu.
2
Mngelo wa Chauta uja adauza Satanayo kuti, “Chauta akudzudzule, iwe Satana! Chauta amene adasankhula Yerusalemu akudzudzule ndithu iwe! Kodi uyu sali ngati chikuni choyaka chofumula pa moto?”
3
Yoswa anali atavala zovala zalitsiro, pa nthaŵi imene adaaima pamaso pa mngelo uja.
4
Tsono mngeloyo adauza anzake omperekeza kuti, “Mvuleni zovala zake zalitsirozi.” Kenaka adauza Yoswa kuti, “Ona ndakuchotsera machimo ako, tsopano ndikuveka zovala zokongola.”
5
Mngelo uja adauza omperekeza aja kuti, “Mvekeni nduŵira yabwino.” Motero adamuveka nduŵira yabwino pa mutu, namuvekanso zovala zatsopano. Nthaŵiyo nkuti mngelo wa Chautayo ataima pomwepo.
6
Mngelo wa Chauta uja adauza Yoswa kuti,
7
“Zimene akunena Chauta Wamphamvuzonse ndi izi, akuti, ‘Mukamayenda m'njira yanga, ndi kumamveradi malamulo anga, mudzalamulira m'nyumba mwanga, ndipo mudzayang'anira mabwalo anga. Tsono ndidzakulolani kuti mudzakhale pamodzi ndi aŵa ali panoŵa.
8
Tsopano imva, iwe Yoswa, mkulu wa ansembe, imvani nanunso ansembe anzakenu, amene muli chizindikiro cha zabwino zimene zidzachitike. Ndidzabwera naye mtumiki wanga wotchedwa dzina loti “Nthambi.”
9
Nawutu mwala umene ndaika pamaso pa Yoswa, mwala umodzi wa mbali zisanu ndi ziŵiri. Mwiniwakene ndidzazokotapo mau, ndidzachotsa machimo a m'dziko lino pa tsiku limodzi.
10
Tsiku limenelo, nonsenu mudzaitanizana kuti mukakondwerere ufulu wanu, aliyense atakhala pa mtengo wake wa mphesa ndi wa mkuyu,’ akutero Chauta Wamphamvuzonse.”
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14