bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Zechariah 6
Zechariah 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 7 →
1
Pambuyo pake ndidaona zinthu zinanso m'masomphenya: ndidaona magaleta anai akutuluka pakati pa mapiri aŵiri, mapiri ake amkuŵa.
2
Galeta loyamba linkakokedwa ndi akavalo ofiira, lachiŵiri akavalo akuda,
3
lachitatu akavalo oyera, lachinai linkakokedwa ndi akavalo otuŵa a maŵanga ofiirira.
4
Tsono ndidafunsa mngelo amene ndinkalankhula naye uja kuti, “Mbuye wanga, kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?”
5
Iye adayankha kuti, “Zimenezi zikutanthauza mphepo zinai zakumwamba, zimene zimachokera kwa Chauta, Ambuye a dziko lonse lapansi.
6
Galeta la akavalo akudali likupita ku dziko lakumpoto. Galeta la akavalo oyerali likupita kutali kuzambwe. Galeta la akavalo amaŵangali likupita ku dziko lakumwera, ndipo galeta la akavalo ofiirali likupita ku dziko lakuvuma.”
7
Akavalowo atatuluka, anali ndi phamphu kufuna kuyendera dziko lonse lapansi. Iye uja adaŵauza kuti, “Pitani mukayendere dziko lapansi.” Akavalowo adapitadi kukayendera dziko lapansi.
8
Apo mngeloyo adandiŵuza mokweza mau kuti, “Amene apita ku dziko lakumpotowo atsitsa mzimu wanga kumeneko.”
9
Kenaka Chauta adandipatsa uthenga wakuti,
10
“Ulandire mphatso kwa anthu aŵa: Heledai, Tobiya, ndi Yedaya, amene abwerako ku ukapolo wa ku Babiloni. Iweyo upite tsiku lomwelo kwa Yosiya mwana wa Zefaniya.
11
Siliva ndi golide amene ulandireyo upangire chisoti chaufumu. Chisoticho uchiike pamutu pa mkulu wa ansembe uja Yoswa, mwana wa Yehozadaki.
12
Tsono umuuze kuti, Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Ndi ameneyutu munthu wotchedwa ‘Nthambi’ uja. Adzaphuka ndi kukulira pomwe aliripo, ndipo adzamangapo Nyumba ya Chauta.
13
Ndiye amene adzamange Nyumba ya Chauta. Ndiye amene adzakhale ndi ukulu waufumu, ndi kumalamulira atakhala pa mpando wake waufumu. Pafupi ndi mpando wake padzakhala wansembe, ndipo aŵiriwo adzagwira ntchito mwamtendere ndi mogwirizana.
14
Chisoti chaufumucho azidzachisunga m'Nyumba ya Chauta, kuti chikhale chikumbutso kwa Heledai, Tobiya, Yedaya ndi Yosiya, mwana wa Zefaniya.
15
“Anthu okhala kutali adzabwera kudzamanga Nyumba ya Chauta. Motero mudzadziŵa kuti Chauta Wamphamvuzonse wandituma kwa inu. Zimenezi zidzachitika ngati mumveradi mwachangu Chauta, Mulungu wanu.”
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14